Nkhani

Mizinda tsopano ili ndi mafumu

Listen to this article

Patadutsa zaka 10 dziko lino lisadakhale ndi mafumu a mizinda, iyi tsopano ndi mbiri pamene mafumuwa abwereranso m’mizinda itatu ya dziko lino.

M’sabatayi kudali kalikiliki m’mizindayi kusankha mafumuwa.

Ali ku Mzuzu:  Mkandawire (Kumanzele)
Ali ku Mzuzu:
Mkandawire (L)

Fumbi lidabonga mumzinda wa Blantyre komwe tsopano kwasankhidwa Noel Chalamanda kuti ndiye mfumu ya mzindawo. Otsatira chipani cha DPP adakwenyana ndi apolisi atamva kuti yemwe amafuna kupikisana nawo pampandowu kuchipani chawo, Lewis Ngalande, sapikisana nawo.

Mumzinda wa Mzuzu anthu adasankha William Mkandawire amene adali mphunzitsi.

Mumzinda wa Lilongwe ndiye adasankha Willie Chapondera mkulu wa bizinesi kukhala mfumu ya mzindawo.

Dziko lino lidakhala ndi mafumuwa mu 2005. Mafumuwa kwakhala kulibe chifukwa chosowa makhansala.

Related Articles

Back to top button