Mkangano wa mafumu sukuzirala

Ntchito za chitukuko zagwedera m’boma la Neno, Nsanje komanso Salima kaamba ka mpungwepungwe wa mafumu womwe sukutha.

Ku Neno boma lidathotha mfumu Chekucheku mu 2014. Mpaka lero boma silidabwezeretse mfumuyi zomwe zapangitsa kuti ofesi ya DC ndi khansala asowe wogwira naye ntchito za chitukuko.

Chekucheku amene akudikira boma limubwezeretse

DC wa boma la Neno, khalansala komanso phungu wa Nyumba ya Malamulo kumeneko akuti m’dera la Chekucheku chitukuko chikuvuta chifukwa palibe mfumu yeniyeni yomwe angagwire nayo ntchito.

Nako ku Nsanje, boma lidaimitsa mfumu Chimombo ndipo lidapatsa mphamvu Harrison Chimombo kuti abagwirizira. Mpaka lero boma silidapezebe wolowa mmalo mwake zomwe zapangitsa kuti anthu agawanike.

Mfumu Bibi Kuluunda ya ku Salima yomwe idaimitsidwa paudindo ndi boma akuti maso ake ali ku boma kuti amubwezeretse ufumu wake chifukwa iye ndiye woyenera ufumuwo.

Boma lidaika mbale wa mfumuyi kuti agwirizire ufumuwu kufikira mpungwepungwe utazirala.

Mafumuwa ndiwo amathandizira kuti chitukuko cha paboma lawo chiyende bwino pogwira ntchito ndi makhansala, ofesi ya chitukuko pa boma, komanso ofesi ya DC.

Koma mneneri wa ku unduna wa za maboma ang’ono Muhlabase Mughogho akuti bata lidzabwerera pokhapokha eni banja atadya khonde ndi kutulutsa munthu woyenerera amene angagwire ntchito ndi boma.

“Tili ndi gawo lothandizira komabe mphamvu zili m’manja mwa abanja kuti atipatse mfumu,” adatero Mughogho.

Mughogho akuti boma silivomereza mfumu yogwirizira. “Dziwani kuti boma siligwira ntchito ndi mfumu yogwirizira.”

Izi zikutanthauza kuti ku Salima, Nsanje ndi Neno kulibe mafumu omwe boma lingagwire nawo ntchito.

Naye DC wa ku Neno Ali Phiri adapempha abanja kuti atulutse munthu amene angalowe mmalo mwa mfumu Chekucheku amene adachotsedwa, koma mwadzidzidzi kudaperekedwa maina asanu.

“Sizikadatheka kuti onse angakhale mfumu nthawi imodzi. Zidakanika. Ndiye ndivomereze kuti mpaka pano tilibe mfumu Chekucheku,” adatero Phiri.

Phiri adati akugwira ntchito ndi makomiti azachitukuko akumudzi chifukwa chosowa mfumu zomwe adati n’zovuta. “Komabe chitukuko chikutheka ngakhale zina zikufunika amfumu.”

Khansala wa dera la Chikonde kwa mfumu Chekucheku, MacPherson Dzimadzi adati ntchito yomanga midadada pa sukulu ya Kalioni ndi Chiwamba ikukanika chifukwa chosowa kwa mfumu Chekucheku.

“Pali ntchito yotuta mchenga, njerwa komanso kwale yomwe ikukanika. Ndidauza mafumu ang’onoang’ono kuti atsogolere anthu awo koma zikukanika chifukwa palibe wamkulu amene angawalankhule. Nthawi zina ndikumaweruza milandu ya mafumuwa akayambana nthawi zina ndikumawatengera kwa DC,” adatero Dzimadzi.

“Ndivomere mavuto alipo chifukwa chosowekera kwa mfumu Chekucheku,” adaomba mkota Dzimadzi.

Malinga ndi ndime 23:03 gawo II gawo  la malamulo okhudza mafumu, boma lidaimitsa mfumu Chekucheku yemwe dzina lake ndi Francis Magombo kuti asagwirenso ntchito za ufumuwu m’boma la Neno kuyambira pa 15 May 2014.

Lachiwiri m’sabatayi, Chekucheku adauza Tamvani kuti akudikirabe boma limuvomere kuti ayambirenso kugwira ntchito.

“Ufumu umene uja ndi wanga ndipo ndikungodikira mtsogoleri wa dziko lino kuti andibwezeretse pa mpandopo,” adatero.

Ku Nsanje mamembala ena abanja la mfumu Chimombo adalembera DC wa bomalo, komanso unduna wa maboma ang’ono kuti asabwezeretse Chimombo amene adachotsedwa mu December 2012.

Mfumu yochotsedwayo, Stanford Tukula, idachotsedwa pamene imaganiziridwa milandu yosowetsa katundu.

Ku Salima boma lidaimitsa mfumu Kuluunda, Khadija Habib Saidi, mu May chaka chatha chifukwa chomuganizira ziphuphu.

Mpaka lero boma silinabwezeretse mfumuyi ndipo mbale wake wa mfumuyi ndiye akugwirizira ufumuwo.

Pocheza ndi Tamvani Lachiwiri, mfumuyi idati “ndikudikirira aboma kuti andibwezeretse pampando”.

Koma katswiri pa zandale Henry Chingaipe mmbuyomu adauza Tamvani kuti dziko lino silidafike pomagwira ntchito yake popanda mafumu.

“Pakufunika Chiefs Act [Malamulo okhudza mafumu] atakonzedwanso kuti tidziwe ntchito za mafumu komanso za mtsogoleri wa dziko pa nkhani zokhudza mafumu,” adatero.

“Sitidafikepo pomagwira ntchito popanda mafumuwa, ndiwofunikabe koma pokhapokha titadziwa ntchito zawo pamene tili [mu ulamuliro wa zipani zambiri].”

Mkulu woyendetsa nkhani zachitukuko ku Neno, Henry Chitema, akuti kusowekera kwa mfumu Chekucheku kwasokoneza nkhani zachitukuko.

Chitema akuti mfumuyi imayenera kutsogolera anthu ake ndi mafumu ake kuti agwire ntchito za chitukuko.

“Ena tikawauza kuti tigwire ntchito akumatiuza kuti iwo ndi abanja lachifumu kotero sangagwire ntchito,” adatero.

“Boma la Neno lili ndi mafumu anayi panopa tatsala ndi ma T/A atatu. Tilibe amene angayimire anthu a kwa Chekucheku. Izi zatikhudza.”

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.