Nkhani

Mlonda anjatidwa kaamba kosolola

Pamene kampani ya Inovantis m’boma la Machinga imanyadira kuti izigona tulo tozuna chifukwa yalemba ntchito Ibrahim Justin, wa zaka 23, ngati mlonda woteteza katundu wawo ku ndipsi, kampaniyi sinadziwe kuti yatuma galu kumalondera nyama ya mbuzi yowotcha kale.

Wapolisi wotengera milandu kukhothi pa Liwonde Police Post, Ezekiel Kalunga, adauza bwalo la milandu la Liwonde kuti pa April 19 chaka chino akuluakulu a kampani ya Inovantis adakagwada kupolisi kukadandaula kuti chipangizo chopanga mphamvu ya magetsi kuchokera kudzuwa (solar panel) chidasowa pakampanipo.ARREST

Kafukufuku woyang’ana chipangizochi ali mkati mkulu wa alonda pakampanipo adakumana ndi munthu wina atanyamula chipangizocho, chimene adachizindikira kuti ndi cha kampani yawo.

Alonda onse adatengeredwa kupolisi ndipo atapanikizidwa ndi mafunso kuti adazembetsa chipangizocho ndani, Justin adavomera kuti ndiyeyo adasolola.

Kalunga adapempha khothi kuti limuthyape Justin ndi chilango chachikulu popeza khalidwe lakelo ndi lothawitsa anthu, makamaka a maiko akunja monga Inovantis, kudzakhazikitsa bizinesi zawo m’dziko muno.

Popereka dandaulo, Justin adapempha bwalo kuti limupatse chilango chochepa popeza iye ndi nsanamira ya banja lake.

Woweruza milandu, Esther Phiri, adagwirizana ndi Kalunga ponena kuti khaliwe lakuba limabwezeretsa chitukuko mmbuyo kotero adamugamula kuti mlondayo akaseweze ndende kwa zaka ziwiri akugwira ntchito yakalavulagaga.

Justin amachokera m’mudzi wa Kaudzu m’dera la mfumu yaikulu Sitola m’bomalo.

Related Articles

Back to top button