Nkhani

Moto buuu! 2019 yafukiza zipani

Listen to this article

Fumbi lachita kobooo! m’zipani pamene kwangotsala chaka chimodzi kuti chisankho cha patatu chichitike m’dziko muno. Chisankho cha patatu chidzakhalako pa 21 May 2019.

Izi zili choncho, zikuoneka kuti m’zipani mwabuka moto pomwe nkhondo yolimbirana wodzaimira zipanizo yakula.

Kumsonkhano wa Aford ena adachita kugona komweko

Pamene ena m’chipani cha DPP akhala akunena kuti Peter Mutharika apereke mpata kwa wachiwiri wake Saulos Chilima kuti adzaimire chipanicho, mtsogoleri wadziko linoyo wati zivute zitani, adzaimirabe DPP. Ku chipani chachikulu chotsutsa boma cha MCP ndiye kokera kwako wayala nthenje pomwe mpaka lero sizikudziwika kuti msonkhano waukulu uchitika liti kuti akasankhe wochiimirira.

Chipani cha UDF nacho kuli mkokemkoke pomwe mlembi wamkulu wachipanicho Kandi Padambo wati ngakhale chipanicho chikhale ndi msonkhano waukulu pa 1 August, chipanicho chagwirizana kuti Atupele Muluzi ndiye adzachitsogolere, chonsecho Lucius Banda wakhala akunena kuti akufuna kudzaimira chipanicho.

Koma njerengo zili ku Aford komwe pofika Lachinayi kudali ochitsogolera awiri: Enoch Chihana ndi Frank Mwenifumbo. Zidaliko Lachiwiri kumsonkhano waukulu wa chipanicho pomwe adalephera kugwirizana kuti woyenera kuvota ndani ndipo mbandakucha wa Lachitatu otsatira Mwenifumbo adamusankha kukhala mtsogoleri. Masana a tsikulo, otsatira Chihana adamusankha kuti ndiye mtsogoleri.

Chihana adati Mwenefumbo amabweretsa mamembala a DPP kumsonkhanowo kuti akavote—nayenso Mwenefumbo adati Chihana adafika ndi anthu amene maina awo mulibe mu kaundula wa chipanicho.

“Uwu si msonkhano wa DPP. Iyi ndi Aford, ndine wokonzeka kuwauza anthu avote bolani akhale athu,” adatero Chihana.

Koma Mwenifumbo sadaimve: “Aford si chipani cha banja kuti chilichonse chizichokera kwa Chihana basi.”

Ndipo ngakhale Mutharika wanenetsa kuti adzaimira DPP, omwe akufuna Chilima akuti ndi maloto chabe. Mmodzi mwa iwo, Bon Kalindo, wati achita zotheka kuti Mutharika asaime, koma Chilima.

“Tikukumana ndipo posakhalitsapa tilankhula zomwe takonza, koma dziwani kuti Chilima ndiye atitengere kuchisankho. Kodi n’chifukwa chiyani tizikakamirabe Mutharika yemwe wakula?” akudabwa Kalindo.

Mneneri wa DPP Francis Kasaila adati chipani chawo chikudziwa kuti  Mutharika ndiye atengere chipanichi kuchisankho.

 

Mgwirizano wa zipani

Pamene mkokemkokewu ukupitirira, zikuoneka kuti zipani zikudzigulira malo polowa mumgwirizano.

Pofika m’dziko lino kuchokera kunja kumene wakhala zaka zinayi chichokere pampando, adalandiridwa ndi otsatira PP komanso a MCP amene adakumana nawo kwa mphindi 30.

Polankhula kwa anthu, Banda adakwanitsa kupereka moni kwa MCP: “Tilandirenso anzathu a MCP amene tili nawo pano.”

Koma mlembi wa MCP, Eseinhower Mkaka adakana kuyankhapo za mgwirizano wa zipanizi. “Ndisayankhe zimenezo koma nditsimikize kuti anthu athu adapita kukalandira mtsogoleri wakale wa dziko lino Joyce Banda. Uwu ndi ulemu wathu chifukwa adali mtsogoleri wa dziko lino,” adatero Mkaka.

Malinga ndi kadaulo pa zandale, Henry Chingaipe, n’zosadabwitsa kuti zipani za MCP ndi PP zikhoza kulowa mumgwirizano.

“Chisankho cha 2014 chisadachitike, padali zingapo zoonetsa ubale wa chipani cha PP ndi MCP. Sindikudabwa kumva zomwe zidachitika pamene Banda amafika m’dziko muno. Izi zingatheke,” adatero Chingaipe.

Ndipo pachisankho chapadera cha makhansala chimene chidachitika m’madera ena miyezi ingapo yapitayo, zipani za UDF ndi DPP zidayendera limodzi popatsana mpata m’madera amene ali ndi mphamvu. Ndipo atapambana, otsatira zipanizo amaimba nyimbo imodzi.

Chingaipe adati zikuoneka kuti DPP ndi UDF angayendere limodzi m’chisankhocho komabe wachenjeza UDF kuti uwu ungakhale ulendo wokutha ngati makatani.

“DPP ikulamula kale, ngati angachite ubale ndiye kuti UDF itha kumezedwa, zomwe zingazimitse banja la Muluzi pankhani ya ndale. Atha kuchita mgwirizano, koma asamale,” adaonjeza motero.

Related Articles

Back to top button