Nkhani

Moto utentha misika, njakata izinga

Listen to this article

A malonda omwe katundu wawo adapsera m’misika ya mavenda ya Tsoka ku Lilongwe komanso wa Blantyre akulira chokweza, uku akupempha boma kuti liwakongoze kangachepe koyambiranso bizinesi.

Moto udatentha misikayi Lamulungu lapitali, kufikitsa chiwerengero cha misika yakupsa pa 10 m’zaka ziwiri.

Mneneri wa polisi kumwera komanso mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Mzuzu ati kusasamala pakapalidwe ka magetsi kungakhale chimodzi mwa zomwe zachulutsa ngozi za moto m’misika.

Mneneriyu, Davie Chingwalu, wati kupatula msika wa Blantyre womwe sakuuganizira kuti wayaka kaamba ka magetsi, zofufuza pa ngozi za misika ingapo zimatulukira zizindikiro za kusagwiritsa ntchito magesti moyenera.

Iye wati n’kuthekanso kuti omwe amaphika m’misika komanso moyandikana ndi misikayo sazimitsa bwino lomwe moto kapena kandulo poweruka.

Mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Mzuzu, Victor Masina, wati zofufuza pa moto omwe udatentha msika wa Mataifa mu mzindawo zidaonetsa kuti padali kusasamala kwa magetsi.

Iye adati pali anthu ena omwe akamanga golosale amakokeramo okha moto wa magetsi zomwe tsiku lina zimadzabutsa moto.

Pomwe Tamvani idayendera msika wa Blantyre pomwe udangopsa, mavenda adadandaula kuti ndi bwino boma kapena mabanki apereke ngongole kwa mavendawa zomwe ziwathandize kuyambiranso mabizinezi awo.

Rafael Nameta Mwini sitolo ya zamagetsi ya Ranambe Electronics, Rafael Nameta, akuti wataya katundu wa pafupifupi K7.6miliyoni.

Wati patapezeka ngongole, mavendawa angakhale m’magulu n’kuyambiranso bizinesi.

Steve Maliyoti amachita buzinesi yogulitsa lamya mumsikaku ndipo akuganiza kuti boma liyenera kuthandiza mavendawa chifukwa iwo ndi Amalawi omwe akufuna thandizo laboma.

Mkulu wa khonsolo ya Blantyre, Ted Nandolo adakana kuikirapo ndemanga pa kupsa kwa msikawu, ati sadalandire lipoti la zomwe zidadzetsa motowo kumsika wa Blantyre.

Koma Chingwalu adati zofufuza zikulunjika koti adayatsa moto adali ana ongoyendayenda.

Iye wati mwana wina wa zaka 12 yemwe apolisiwa akumusunga m’chitolokosi akuulula kuti anzake anayi ndi amene adayatsa msikawo.

Iye wati akuganizira kuti apeza zenizeni kuchoka kwa mwanayo.

“Izi zatipatsa ntchito yogwira ana onse oyendayenda m’misika usiku. Tikawagwira tiwapereka kwa makolo awo ndipo omwe alibe makolo apita kumalo osungira ana amasiye.

Related Articles

Back to top button