Chichewa

Mpando Wamkulu afika pa Wenela

Abale anzanga, tsikulo kudali nyimbo zija zogawa tonse pa Wenela. Adayamba ndi Patience Namadingo, yemwe waimba Nyimbo yotamanda uja mneneri wathu Majuscule Profit Bashiri. Musandifunse kuti dzina ili lidabwera bwanji chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna muchitenji?

Sinjenjemera ndiyo nyimbo adayamba kuika Gervazzio. Iyitu ndi nyimbo imene ikutamanda kuti Majuscule Profit Bashiri akunenedwa kuti ngakhale alasidwe mikondo yamoto, sanjenjemera.

Wina uyu.

tadeyo

Idaikidwanso nyimbo ya anyamata ena, ati kuyankha ija ya David ya Osaopa. Sindikudziwa kuti nyimbo ya anyamatawa kwenikweni akumati chiyani, koma akumanenamo zakuti iwo sakuopa. Kaya sakuopa chiyani?

Pasanathe nthawi idaikidwanso ya Kalawe, yotamandira Bashiri. Adaikanso nyimbo ija ya Onesimus (ndikumva kuti uyu ndi mbale wake wa Twosimus!). Iyetu ndiye adabwera ndi nkhani ati Miracle Money.

Major do it!

I need money

In my pocket

In my wallet

In my handbag

In my bank account.

Koma isanathe, kudabwera nyimbo ya Osaopa, ya David.

Muli ulaliki umo! Ndapha mikango, akutero. Sindilekerera ngati mikango ipha ziweto zanga! Sindichita mantha ngakhale kulekerera ngati nkhosa zanga zijiwa ndi mikango. Ndaphapo mikango ngakhalenso zimbalangondo ndiye sindingaope Mfilisiti wosaumbala akuzunza anthu anga.

“Komatu izi za ‘miracle money’ ndizo zikuchititsa ambiri kukhala aulesi. Nanga taonani a mipira akuti koma miracle money! A nkhonya nawonso akuti miracle money,” adatero Abiti Patuma.

Tidangozindikira Majuscule Profit Bashiri watulukira, amvekere: “Ndili pano ndi miracle money! Ndani akufuna chozizwa?”

Kukonda ndalama ndicho chiyambi cha uchimo. Ngati aneneri odzodzedwa akuyamba kuzika mzimu wokonda ndalama mwa nkhosa zawo, zitha bwanji?

“Zanuzo ife ayi. Sitifuna kupempha ndalama monga achitira ena. Ife kwa inu tipempha pemphero kuti Mulungu atipatse nzeru zopezera ndalama. Komanso sitingapemphe kwa Mulungu kudzera mwa inu chifukwa simunakhalepo Yesu,” adatero Abiti Patuma.

Mawu ake ali mkamwa adatulukira Mpando Wamkulu.

“Mumadziwa inu za kuchitekete? Mumawadziwa inu anyamata a patauni? Mumamvetsa za changu pamalo? Lero ndabwera. Mwana uja amafuna kundipinga wazitaya. Si nkhanitu ya miracle money iyiyi, ayi,” adatero iye.

Abale anzanga, munthu uyu sindimumvetsa. Sindidzamumvetsa.

“Mwayenera. Ifetu titangomva kuti ena akukomoka tidadziwiratu kuti zavuta,” adatero Abiti Patuma.

Palibe ndidatolapo.

“Izi ndikuchita chifukwa ndidasolola zochepa kuposa Adona Hilida ngakhalenso Mfumu Mose. N’kadadziwa kuti ndalamazi n’zophweka chonchi, mukadamva zina. Ine ndi nyatwa,” adatero iye.

Zidandipitanso.

Gwira bango iwe! Upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button