Mphekesera zizunza anthu ku Mangochi

Zina ukamva, kamba anga mwala ndithu. Anthu a m’boma la Mangochi sabata yapitayi adadzuka pakati pausiku, ena m’bandakucha, n’kuyamba kukupa phala pokhulupirira mphekesera zoti khanda longobadwa kumene laopseza kuti yemwe sachita zimenezo awona zakuda.

Mfumu Makanjira ndi bwana mkubwa wa bomalo, Moses Mphepo, atsimikiza za nkhaniyo, koma ati sakukhulupira zoti mphepo yamkuntho yomwe yaononga nyumba, mizikiti ndi katundu m’bomalo ikugwirizana ndi mphekeserazo.

Makanjira: Anthu amwa phala

Mfumu Makanjira ikuti munthu wina adaitchaila lamya usiku yofotokoza kuti khanda longobadwa kumene la m’dziko la Mozambique lalosera kuti m’boma la Mangochi mugwa mavuto aakulu ngati anthu sakupa ndi kudya phala.

“Nditatsiriza kulankhula pa lamyayo, ndinatuluka panja koma ndinadabwa kuona anthu ali pikitipikiti kukupa phala, ena akumwa. Anthu ena anafika kunyumba kwanga kukafunsa nzeru.

“Tsiku lotsatira chimphepo chachikulu chidaononga nyumba, mizikiti ndi katundu wambiri moti anthu ena akuti zikugwirizana ndi mawu akhanda lija,” adatero Makanjira.

Mphekeserazo zikuti khandalo, lomwe lidabadwira m’dera Kumwembe m’dziko la Mozambique, lidamwalira litangotsiriza kupereka uthengawo.

Mussa Malekano ndi mmodzi mwa anthu omwe adakupa ndi kumwa phalalo. “Ndinalandira foni yondichenjeza kuti ndiona zakuda ndikapanda kukupa ndi kudya phala ndi banja langa lonse.”

Mneneri wapolisi wa m’bomalo, Rodrick Maida, adati ofesi yawo siigwiritsa ntchito zikhulupiriro pogwira ntchito, koma malamulo a dziko.

Chimphepo adati mphepo yomwe yawononga katundu ndi mizikiti m’bomalo siikugwirizana ndi mphekesera za khandalo.

“Ndalandira malipoti woti mphepo yaononga katundu, koma sindikukhulupirira kuti zikukhudzana ndi mphekesera za khandalo,” adatero bwanamkubwalo.

Anthu omwe Msangulutso walankhula nawo alephera kupereka umboni wogwirika woti khanda linabadwadi, koma wapeza kuti mphepo yaonongadi nyumba, mizikiti ndi katundu m’madera a Makanjira, Nankumba ndi Chimwala. n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.