Nkhani

Mpingo ukana mbusa womangidwa za zitupa

Mpingo wa Lord’s Chosen Charismatic Revival Ministries (LCCRM) wakana zomwe munthu wina wa ku Cameroon adauza nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno kuti iye ndi mbusa komanso mtsogolera wa mpingowu m’dziko muno.

Abusa ndi Akhrisitu a mpingowu ati Israel Ejelli adachoka mumpingowo iwo atapempha a kulikulu lawo ku Nigeria kuti amuchotse patchalitchipo chifukwa chosasangalala ndi zomwe amachita.

Mmodzi mwa abusa akuluakulu a mumpingowu Desmond Ugochukwu wa ku Nigeria wati Ejelli anali mkulu wa mpingowu kuno ku Malawi koma ankachita zosemphana ndi malamulo a mpingowu komanso sankalemekeza mtsogoleri wa mpingowu.

“Vuto lenileni lomwe anali nalo ndi lakuti amaderera mtsogoleri wa mpingo wathu dziko lonse, mbusa Lazarus Muoka, yemwe ali ku Nigeria komanso amaphwanya malamulo a mpingo wathu,” adatero Ugochukwu.

Iye wati mpingowu udaganiza zoyamba kumusala ndipo likulu la mpingowu lidatumiza mbusa wina Peter Ndukwe wochokeranso ku Nigeria kuti adzatenge udindo wotsogolera mpingowu.

Ugochukwu akuti mbusa wokanidwayo ataona kuti sakugwirizana ndi Akhristu a mumpingowo adapempha kulikulu kuti akufuna kuchoka mumpingowo ndipo adamulembera kalata yomuvomereza kuchokako yomwe adadzaipereka kutchalitchiko.

“M’mabuku mwathu tikudziwa zoti adatuluka mumpingo ndipo si mbusanso koma tikudabwa kuti akumagwiritsa ntchito mpingowu ngati chizindikiro chake. Posachedwapa atamangidwa adauza apolisi kuti ndi mtsogoleri wa mpingo uno chonsecho adapuma ndipo mtsogoleri panopa ndi mbusa Peter Ndukwe.

“Zimenezi zakwiyitsa Akhristu athu ndipo tikhala pansi kuti tione chomwe tingachite asanapitirize kuononga mbiri ya mpingo,” adatero Ugochukwu.

Mneneri wa nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno kuofesi ya ku Lilongwe, Ealack Banda, adati Ejelli adamangidwa pamlandu wopanga ziphaso zachinyengo.

Iye adati nkhaniyi idaphulika akuofesi ya kazembe wa dziko la China atauza nthambiyi kuti munthu wina adapita kuofesiko ndi ziphaso zinayi zachinyengo zomwe ankafuna kutengera zilolezo za anthu ena a ku Ghana.

“Titamva izi tidamanga munthuyo, Daniel Bart-Plange, wa zaka 32, koma titafufuza nkhaniyi idakhudzanso mbusayo [Ejelli] ndipo tidawamanga,” adatero Banda.

Akuluakulu a mpingowu ati kalata zomwe mpingowo udamupangitsira Ejelli kuti adzagwire ntchito ngati mbusa kuno ku Malawi zidatha ntchito.

Mpingowu akuti udabwera kuno ku Malawi mu 2003 ndipo uli ndi nthambi ku Lilongwe ku Area 2 ndi ku Mzuzu.

Banda wati Ejelli anamutulutsa pabelo ndipo akuti azikaonekera ku ofesi yowona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno Lolemba lililonse pomwe mnzakeyo, Bart-Plange, ali kundende ya Maula koma onse akudikira tsiku la mlandu.

Tidalephera kulankhula ndi Ejelli chifukwa samadziwika kumene akukhala.

Awiriwa akadzapezeka olakwa adzamangidwa ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zitatu chifukwa chophwanya gawo 356 la malamulo a dziko lino.

Related Articles

Back to top button