Nkhani

Mtembo usagone pano—Achipatala

Pasathe tsiku mtengo wanu musadadzatenge. Uthenga omwe a zipatala za Rumphi ndi Machinga akuuza anthu chifukwa cha kuonongeka kwa malo wosungira mitembo pachipatalapo.

Pachipatala cha boma ku Rumphi, zaka ziwiri zatha malo osungira mitembowa atasiya kugwira ntchito pamene ku Machinga, miyezi itatu yatha malowa atasiya kugwira ntchito.

Jobe: Boma lichitepo kanthu

Izi sizidakomere anthu amene amagwiritsa ntchito zipatalazi amene anena kuti boma ndi mabungwe alowererepo kuti zotere zisinthe.

T/A Nyambi ya m’boma la Machinga akuti pakhala povuta kuti anthu azikatenga thupi la malemu tsiku lomwelo chifukwa palibe amene amakonzekera maliro.

“Ambiri tikukhala kutali ndi chipatalachi. Zovuta zikagwa timadalira kuti pathe tsiku kuti tipeze mayendedwe. Tikuvutika chifukwa kuchipatalako kulibe galimoto zokwanira kuti azikatisiyira zovuta pakhomo pathu,” adatero Nyambi.

Mneneri wa chipatala cha Machinga, Clifton Ngozo akuti sangachitire mwina chifukwa ngati angasunge thupi kwa nthawi ndiye kuti lingathe kuonongeka.

“Kudachitika ngozi, tidasunga matupi amene amakha magazi. Padatha masiku awiri kuti matupiwo apite kukaikidwa koma kudali fungo loipa. Ndiye sizithekanso kuti tisunge mtembo pokhapokha malowa atakonzedwa,” adatero Ngozo.

Iye adati ngati atapitirira kumagoneka mitembo ndiye kuti zingabweretse zotsatira zoipa monga matenda kwa amene akugwira ntchito kumalowa.

“Poyamba timasunga mitembo kwa masiku oposa awiri kapena atatu koma akamadzatenga mtembowo umakhala uli bwinobwino. Panopa sizingathekenso chifukwa malowa aonongeka.

“Panopa uthenga omwe tikuuza anthu amene amagwiritsa ntchito malowa ndikuti sitikwanitsanso kuti matupi azigona kumeneku. Zovuta zikachitika atha kusunga koma asagone chifukwa aonongeka,” adatero Ngozo.

Kuchipatala cha Rumphi, anthu adasiya kugoneka mitembo chifukwa cha kuonongeka kwa malo osungira mitembo.

Mneneri wa chipatalachi Bwanalori Mwamlima akuti malo osungira mitembo adaonongeka zaka khumi zapitazo koma akhala akukonzetsa mpaka 2015.

“Panopa sitingakonzenso, chifukwa pena tikakonza sichimachedwanso kuonongeka. Apapa zavuta ndipo tasiya kugoneka mitembo chifukwa ikumaonongeka,” adatero Mwamlima.

Iye akuti vuto nkuti zipangizozi zakhalitsa. “Ndikakumbuka bwino, zipangizozi zidaikidwa m’ma 1976, zakhala zikugwira ntchito mpaka lero,” adatero Mwamlima.

Izi zakhumudwitsanso mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe amene wati aphungu a Nyumba ya Malamulo akuyenera aikambirane pamene akhale akukumana.

“Amene adamanga nyumba yachisoni adali ndi cholinga ndipo adaona kufunikira kwake. Izi si zoona kuti mpaka malowa asiye kugwira ntchito chifukwa talephera kuwakonza.

“Palibe amene amayembekezera maliro pamene wapita kuchipatala. Ndiye simunganene kuti maliro akangochitika basi munyamule,” adatero Jobe.

Ku Salima nakonso akhala akukumana ndi mavuto omwewa koma pano zidayenda pamene malo osungira mitembowo adakonzedwa.

T/A Mwanza wa m’bomali akufotokoza.  “Tidakumana ndi mavutowa koma panopa zinthu zilibwino pachipatalachi chifukwa adakonza,” adatero Mwanza.

Jobe akuti sadamverepo malipoti akuonongeka kwa malo osungira mitembowa chichitikireni nkhani ya ku Kamuzu Central Hospital pamene matupi amaola. n

Related Articles

Back to top button