Chichewa

‘Mudali m’galimoto ulendo ku Area 23’

Listen to this article

 

Kumwetulira kwa Shreen Mbendera, muulutsi pawailesi ya Galaxy FM, kunachititsa kuti Kimu Kamau amuthere mawu namwaliyu. Ukwati walengezedwa kale kuti ndi pa 29 October chaka chino.

Kamau, yemwe akugwira ku Union Building Contractor’s ngati woyang’anira chigawo chapakati, lero alibenso mawu. October akumuona kuchedwa malinga ndi momwe June waziziriramu.

Kamau akuti idali ntchito yaikulu chifukwa mtsikanayu amalimba chifu kuti pavute patani, Kamau yekha ayi. Mapemphero adathandiza ndipo tsiku lidakwana kuti Shreen akhale ndi mawu omaliza pa Kamau.

Akuti mudali mu 2014 pomwe adamutenga Shreen ulendo naye ku 23 komwe namwaliyu amakhala komwenso ndikoyandikana ndi kunyumba kwa Kamau.

Akuti akamwetulira Shreen Kamau mawu onse balala
Akuti akamwetulira Shreen Kamau mawu onse balala

Pumbwa wakankhidwira kuchipwete! “Apa nkuti nditamudziwa kale Shreen chifukwa tidakumana ku Galaxy pamene ndidapita kukaona mnzanga. Pokaona mnzangayo, mpamene pamabwera Shreen yemwe amacheza ndi mnzangayo.

“Inenso ndidayamba kumacheza ndi namwaliyu mpaka pamene ndidayamba kumufuna nditazindikiranso kuti sadali pabanja,” adatero.

Komabe Kamau akuti sakadatha kukhala nthawi yaitali asadathire mawu namwaliyu chifukwa cha zomwe zimatakasa mtima wake.

“Akati amwetulire, komanso maonekedwe ake, eeh ndidafuna ndichite kanthu kuti zimenezi ndizikazionera pafupi,” adayamikira Kamau.

Adayesera kutulutsa mawu osiyanasiyana koma namwaliyu adakana. “Ndidayendera mpaka kutopa, kuyesera kukamba za manifesto yanga yonse koma osavomera. Kenaka ndidadabwa akundiyankha mmenemo nditataya chikhulupiriro,” adatero Kamau.

“Nthawi ya Mulungu ndiyo nthawi yabwino, chilichonse chili ndi nthawi yake. Amene akusaka, afunse kaye Ambuye ndipo adzawapatsa wachikondi weniweni,” adatero namwaliyu.

Ukwati wawo ukachitikira ku Banja Loyera Parish ku Chilinde 2 mumzinda wa Lilongwe. Shreen ndi wa m’mudzi mwa Gambatula kwa T/A Chakhumbira m’boma la Ntcheu ndipo Kamau ndi wa m’mudzi mwa Mpagaja, kwa Senior Chief Somba ku Blantyre.

Related Articles

Back to top button