Nkhani

Mulanje yadya wani pa chitukuko

Boma la Mulanje ladya wani pogwiritsa ntchito ndalama za thumba la chitukuko m’dera la phungu la Constistuency Development Fund (CDF), pulogalamu yosanthira momwe thumbali likugwiritsidwira ntchito m’maboma 14 a dziko lino ya Kalondolondo yapeza.

Izi zidadziwika Lachiwiri pamsonkhano wounikira momwe ntchito za chitukukozi zidayendera m’bomali umene udachitikira ku Hapuwani Village Lodge m’bomalo.

Malinga ndi kafukufuku amene bungwe la Women’s Legal Resource Centre (Wolrec), lomwe limagwira ntchito mogwirizana ndi Kalondolondo, magawo 73 mwa 100 aliwonse a ntchito zachitukuko m’madera a aphungu 9 a m’bomalo adatha.

Mkulu wa Kalondolondo Jephter Mwanza adati adakhutira ndi momwe ntchito zachitukuko zayendera ku Mulanje.

“Zambiri mwa ntchito za chitukuko ku Mulanje zakhala pang’ono kutha. Apa zili bwino poyerekeza ndi maboma ena amene kwamangidwa zinthu zosalingana ndi ndalama zomwe zidaperekedwa,” adatero Mwanza.

Bwanamkubwa wa boma la Mulanje Jack Nguluwe adati kuchita zinthu mosabisa ndiko kwachititsa kuti ndalama za CDF zisalowe m’matumba mwa anthu.

Chaka chilichonse, dera la phungu aliyense limapatsidwa K7 miliyoni yogwirira ntchito za chitukuko zing’onozing’ono.

“Ena amaganiza kuti boma likapereka ndalamazo zimapita kwa phungu ndipo iye akhoza kusolola. Sizili choncho chifukwa zimafika kuofesi kwathu ndipo phungu amangonena ntchito za chitukuko zimene anthu a m’dera lake akufuna. Ofesi yathu ndiyo imagula katundu ndipo malisiti onse timasunga komanso timawapereka kwa makomiti owona zachitukuko,” adatero Nguluwe.

Ndipo phungu wa dera lapakati m’bomalo Kondwani Nankhumwa adati mgwirizano ndiwo ukufunika pa chitukuko. Iye adatsagana ndi phungu wa kumpoto m’bomalo Stephen Namacha komanso wa kumwera cha kummawa Ben Bonongwe.

“Popanda mgwirizano, palibe chitukuko. Timagwira ntchito limodzi osatengera kuti uyu ndi wotsutsa kapena wachipani cholamula. Izi ndizo zathandiza kuti chitukuko m’boma lino chipite patsogolo,” adatero Nankhumwa.

Related Articles

Back to top button