Chichewa

Muli phindu mu ulimi wa chinangwa

Listen to this article

Cassava_planting_man
Mlimi amaonetsa chitsakano ngati akupindula ndi mbewu zake. Ulimi weniweni umakhala umenewu woti mlimi azipindula kusiyana nkuti azikhalira kukanda m’mutu ndi mavuto. Ndidali m’mudzi mwa Chikoja kwa T/A Kadewere m’boma la Chiradzulu komwe amacheza ndi mlimi wa chinangwa. Iyeyu akuti akupha makwacha kusiyana ndi chaka chatha. Adacheza motere:

Tidziwane wawa
Ndine Desideliyo Kulapa, muno ndiye m’mudzi mwathu. Ali kumbuyowa ndi akazi anga.

Muchita chiyani?
Basitu bizinesi achimwene. Ndikugulitsa chinangwa pakuti ino ndiye nthawi yake.

Mtundu wanji wa chinangwa uwu?
Uwu ndi mtundu wa manyokola. Manyokolayu ndachita kugula kwa Nambala m’boma la Zomba.

Inu mumalima?
Eya, ndine mlimi wa chinangwa, chimanga komanso nandolo ndi mbewu zina. Ku Zomba ndiko kumayambira chinangwa ndiye ndimati chikayamba ku Zombako ndimapita kukaoda ndi kumadzagulitsa kuno pamenepo ndiye kuti ndikudikira kuti changa chikhwime.

Mwalima mtundu wanji wa chinangwa?
Ndalima manyokola yemweyu koma pena ndikumagulitsanso chinangwa cha mtundu wa nakachamba chija chimaoneka chofiira.

Msika wa chinangwa uli bwanji?
Chaka chino pamsika pali bwino chifukwa mtengo wake ukusiyana ndi wa chaka chatha. Chaka chatha timakaoda thumba la makilogalamu 50 pa mtengo wa K5 000 ndi kugulitsa K7 000. Koma pano tikuoda pa mtengo wa K6 000 ndi kugulitsa K9 000 kapena kuposera apo. Izi zili bwino ndipo ndapha makwacha.

Kodi nthawi ya chinangwa ndi ino?
Chinangwa chinachi chimayamba kukhala bwino mwezi wa April moti ino ndi nthawi yake koma chinangwa cha mtundu wa manyokola chidayamba kudyedwa mwezi wa February.

Kodi chaka chino alimi alima chinangwa chambiri?
Chaka chino kwalimidwa chinangwa kusiyananso ndi zaka zina chifukwa choti chimanga sichidakhale ndiye anthu alima chinangwa ndi mbatata kuti adzaone populumukira.

Ulimiwu wakuthandizani bwanji?
Ineyo ndimadalira ulimiwu, sindigwira ntchito iliyonse kapena kudalira thandizo kwa ena. Pakhomo panga ndagula ziweto komanso thandizo lililonse likuchokera mu ulimiwu.

Related Articles

Back to top button