Nkhani

Mutharika achenjeza akamberembere

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wasonyeza kuti amatsatira ukamberembere omwe umachitika mkatikati mwa malonda a fodya ndipo wachenjeza ogulitsa ndi ogula kuti sakufuna nyansizi chaka chino.

Mutharika adapereka chenjezoli potsegulira msika wa fodya wa chaka chino ku ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe Lachitatu lapitali.peter_tobacco

Iye sadasiye mbali podzudzula ndi kuchenjeza onse okhudzidwa m’malondawa ponena kuti ogula ali ndi chisimo chosintha mawanga mkatikati mwa malonda pomwe ogulitsa adawadzudzula kuti amachulutsa

ukamberembere poika zitsotso m’mabelo awo.

“Inu makampani ogula fodya ndikuchenjezeni pano. Tsiku loyamba, mumagula fodya pamitengo yomwe idakhazikitsidwa koma kenako n’kusintha mawanga mkatikati mwa msika. Zimenezi sitikuzifuna chaka chino,” adatero Mutharika.

Iye adati mchitidwe wotere umayambitsa mikangano pakati pa ogula fodya ndi alimi mpaka msika kumasokonezeka chifukwa cha kusamvana.

Mutharika adatembenukiranso kwa alimi n’kuwadzudzula kuti achepetse ukamberembere woika zitsotso m’mabelo ndi cholinga chopusitsa makampani ogula fodya kuti mabelo awo azilemera pomwe muli fodya wochepa kapena woipa.

“Inuso alimi ndikuchenjezeni pakhalidwe loika zinthu zosayenera m’mabelo a fodya. Khalidwe limene lija ndilo limapangitsa kuti makampani azibweza fodya wambiri pamapeto pake mumakhala ngatimudagwira ntchito yopanda malipiro,” adatero Mutharika.

Iye adati ali ndi chiyembekezo kuti malonda a fodya ayenda bwino chaka chino poyerekeza ndi zaka za mmbuyo pomwe kumakhala kusamvana kwakukulu pakati pa alimi andi makampani ogula fodya, makamaka pankhani ya mitengo ndi maonekedwe a fodya.

Fodya wa chaka chino ayamba kumugula pamtengo wa $0.80 (pafupifupi K552) pa kilogalamu pomwe kusiyana ndi chaka chatha pomwe adayamba ndi $2.32 (pafupifupi K1, 044 pa kilogalamu potengera mphamvu ya kwacha panthawiyo).

Izi zili chonchi, bungwe la Tobacco Control Commission (TCC) lati ndi lokhudzidwa ndi kuchuluka kwa fodya yemwe akubwezedwa potengera tsiku lotsegulira msikali pomwe mabelo 30 pa mabelo 100 alionse amabwezedwa.

Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda adati nzodabwitsa kuti kwacha yayamba kukwera mphamvu pomwe alimi akugulitsa fodya pomwe adagula zipangizo mokwera kwacha itagwa.

Related Articles

One Comment

  1. Chimbomi Pius Nkoma amakala kuNkata Bay mudziko rino , phone me panumber +263712541986.

Back to top button
Translate »