Chichewa

Mwambo wa ukwati wa Chitonga

Listen to this article

 

Mtundu wina uliwonse uli ndi chikhalidwe chake. Ndipo nawo mtundu wa Atonga womwe umapezeka kwambiri ku Nkhata Bay ndi Nkhotakota uli ndi mwambo wawo wa ukwati. Masiku apitawa Martha Chirambo adacheza ndi MfumuVimaso yochokera m’dera la T/A Kabunduli ku Nkhata Bay ndipo idalongosola za mwambowu motere:

Takupezani gogo. Ifetu timafuna timve zambiri za mwambo wa ukwati wa Chitonga.

Ife Atonga monga mtundu wina uliwonse tili ndi dongosolo lathu lomwe timatsatira panthawi ya ukwati. Sitimafuna ukwati wa m’njira.

Vimaso kulongosola za mwambowu
Vimaso kulongosola za mwambowu

Tatambasulani kuchokera pachiyambi. Zimatani mkazi wa Chitonga akapeza bwenzi lomanga nalo banja?

Mkazi wa Chitonga weniweni akakumana ndi mwamuna woti akumfunsira banja savomerana kunjira konko, ayi. Mwamunayu pamodzi ndi mnzake amafika pakhomo pa namwaliyo kudzafunsira. Ndipo pofunsirapo namwaliyo pamakhala palibe, amafunsira agogo ake kapena achemwali ake. Awa ndi omwe amakamfunsanso namwaliyo kumbali. Mtsikanayo akavomereza, mwamunayo amapereka chikole mwina K200 000 kapena molingana ndi mapezedwe ake. Ndalama imeneyi imadzagwiritsidwa ntchito yogulira ziwiya panthawi ya ukwati. Apanso ndi pomwe mwamunayo amafunsa khomo lokafikira thenga pochita dongosolo lomanga banja.

Pamakhalanso dongosolo lina?

Eya, limakhalapo. Akwawo kwa mwamuna tsopano amafikanso pamudzipo kudzadziwitsa anthu kuti tambala wawo wapeza msoti pakhomopo. Apatu samangobwera chimanjamanja, ayi, amanyamulanso ndalama yomwe timaitchula kuti chiziyapamuzi  ndipo zokambirana zimayamba tsopano. Anthuwa akagwirizana, ndi pomwe amapereka malowolo. Zikatero ndipomwe amapempha za tsiku la ukwati.

Koma ndiye zolowa zikuchulukatu!

Apanso amakhala asanamalize chifukwa amaperekanso mkhuzi. Ili ndi bulangete lomwe limaperekedwa kwa make mwana. Komatu silimakhala bulangete wamba, ayi. Chimakhala chibulangete chenicheni.

Kodi patsiku la ukwati, zimakhala bwanji?

Pakatsala masiku awiri tsikuli lisadafike, akuchikazi amakatula nkhuni kuchimuna. Izi zimakhala zodzaphikira patsiku la ukwati komanso zina zoti akamusiyire namwaliyo. Ndipo kukatsala tsiku limodzi amakatula ufa wambirinso, nyama komanso ziwiya zophikira. Ukwati ukachitika, amayi ena pang’ono amatsalira ndipo amaphika zakudya zambiri ndi kupereka kwa abale a mwamuna. Izitu zimachitika ngati njira yowauzira kuti pamudzipo pafika mkazi watsopano.

Izi zikadutsa, amayiwa amabwerera mmbuyo.

Kodi palinso mwambo wina kapena zikafika apa basi zatha?

Amayi anayi tsopano amalowa m’bwalo. Awiri akuchikazi komanso awiri akuchimuna omwe timawatchula kuti azamba am’nyumba. Ntchito ya awa ndi kuwaphunzitsa awiriwa zenizeni za banja tsopano.

Apatu ndi pamene akuluakulu amadziwiranso ngati mwamuna ali wobereka kapena ayi, komanso ngati mkazi anali woyendayenda.

Ndi zothekadi zimenezi?

Awiriwa amapatsidwa tinsalu tiwiri togwiritsa ntchito akamaliza kugwira ntchito komanso kamphika ka madzi. Ndipo macheza akatha, azambawa amaona tinsaluto ngati mwamunayo ali wobereka kapena ayi mwaluso lawo.

Chimachitika ndi chiyani akapezeka kuti ngosabereka?

Ngakhale apezeke kuti sizidayende, azambawa saulula, chimakhala chinsinsi chawo.

Kodi amaunikidwa ndi mwamuna yekhayo? Nanga mkaziyo?

Naye mkazi ali ndi zake zomwe amamuunika. Makamaka amaunika ngati ali woti sanagonepo ndi mwamuna wina. Ndipo akapezeka zonse zili bwino, mwamunayo amalipira ndalama ndithu.

Akapezeka kuti izi zidachitikapo, zimamuthera bwanji?

Akuluakuluwa amakhumudwa kuti wawachititsa manyazi, komanso mwamunayo sapereka ndalama ija. Kwambirinso akuluakuluwa amakhumudwa kuti mwana wawoyo sadaulule kuti kunayendako munthu wina. Akaulula ukwati usadachitike, amapatsidwa mankhwala ndipo amakhalanso ngati wanyuwani. Amabwerera m’chimake bwinobwino ndithu.

Kodi zikuchitikabe?

Ife akumudzi timachitabe izi pomwe amtauni adaiwalako zotsatira mwambo ndipo akamakwatirana amakhala kuti adathana kalekale.

Pomaliza, tatiuzani kodi ukwatiwu ukatha zimakhala bwanji?

Ngati awiriwa sadamvane pazifukwa zina ndipo banja latha, akuchikazi amabweza malowolo okha basi. Pali nthawi zina pakakhala ana, akuchimuna amatha kuwauza akuchikazi kuti angobwezako pang’ono. n

Related Articles

One Comment

Back to top button