Nkhani

Mwambo woliza mfuti pamaliro Achingoni

Listen to this article

Mfumu Yachingoni ikagona, pamaliropo amaomba mfuti thupi la mfumuyo lilowe m’manda. Mwezi wathawu, kudachitika maliro a T/A Bvumbwe m’boma la Thyolo. ku malirokonso kudalizidwa mfuti, chomwe anthu ena amene adali kumwambowo adadabwa nacho. BOBBY KABANGO adacheza ndi mkulu amene amaomba mfutiyo kuti amve zambiri za mwambowu motere:vumbwe2

Wawa…

Fikani ndithu musaope. 

Ndikudziweni bwanji?

Choyamba dzina langa ndine Moses Chikoko. Mungandidziwe monga mbali ya mbumba kwa T/A Bvumbwe. Ngati mudamvapo za Gomani Chikuse amene adadulidwa khosi, ameneyo ndiye adabereka mayi anga. Mkazi wachinayi wa Gomani Chikuse ndi amene adabereka mayi angawo.

Ndiye mudapezeka bwanji kuti mukukhala ku Thyolo kuno?

Pajatu Angoni adali ankhondo, ndiye gulu la mayi anga ndi lomwe lidabwera kuno pamene Angoni ena ankafikira madera ena. Mayi anga adali wa mtundu wa Maseko koma bambo anga adali a kwa Mulauzi.

T/A Bvumbwe wagonayu adali ndani wanu?

Wagonayu ndi mwana wanga, koma sindikutanthauza kuti ine ndi amene ndidabereka iyeyu, koma kuti bambo ake adayenda limodzi ndi ine kusukulu, amenewo adali a Steven Bvumbwe.

Mfuti mwatengayi mufuna mugwiritsire ntchito yanji?

Ngati mukumva kulira mfuti pamalo pano ndikuliza ndineyo, ntchito yake n’kuti ilire pamene tikugoneka mfumu yathu. Dziwani kuti pamaliro a mfumu Yachingoni pamalira mfuti mpaka mfumuyo itatsikira m’manda.

Mumaliza kangati?

Mfuti imalira kanayi. Koyamba imalira kusonyeza kuti mfumu yamwalira. Apa amakhala kuti amene alowe m’malo mwake wabwera kudzaona nkhope ndi kutsimikizadi kuti mfumuyo yamwalira. Imalira kachiwiri pamene tikutulutsa thupi la mfumuyo m’nyumba. Timalizanso kachitatu pamene tanyamula thupi ulendo kumanda. Pamenepa timaomba kusonyeza kuti akutsanzika. Timadzaombanso komaliza pamene bokosi latsitsiridwa m’manda kusonyeza kuti wafika.

Chifukwa chiyani mumaomba mfuti?

Kusonyeza kuti Mngoni ndi wankhondo. Ndiye ngati Mngoni, yemwe timamudziwa bwino kuti ndi wankhondo, wamwalira zotere zimayenera zichitike.

Bvumbwe adamenya kuti nkhondo yake?

Bvumbwe adali Mngoni ndipo Angoni amadziwika kuti ndi ankhondo ngakhale sadamenye nkhondoyo. Sindingakuyankheni kuti adamenya kuti koma dziwani kuti Bvumbwe adali Mngoni yemwe ndi wankhondo.

Nkhondo yake iti kodi?

Mukudziwa kuti Angoni adachita kumenya nkhondo mpaka kudutsa ku Domwe. Akafika pamalo amayamba amenya nkhondo ndi kukhazikika bwino. Nkhondo yake ndi imeneyo.

Kodi ndimayesa nkhondoyo idatha kalekale? Nanga inu mukuchitabe izi bwanji?

Eya, koma nkhondo yathu ndi ya m’magazi, kusonyeza kuti simatha. Mwambo umenewu udayamba kalekale ndi makolo athuwo.

Mfuti zisadayambe kupangidwa mumaliza chiyani?

Aaah, mwaiwala? Kudali mfuti zagogodera zomwe tinkagwiritsa ntchito nthawi ngati ino.  

Mwapeza bwanji chilolezo choliza mfuti?

Choyamba dziwani kuti ndine msirikali, mfuti ndimaidziwa chifukwa cha ntchito. Ndilinso ndi mfuti komanso ndidali Wapayoniya. Ndiye m’nyumba mwanga mfuti si yachilendo.

Anthu enatu amadzidzimuka, mumakhala ndi chilolezo kuti muombe mfuti?

Nchifukwa chake mwandiona kuti ndakhala kutchire ndekhandekha podziwa kuti pali anthu odwala mtima amene angathe kukomoka mfuti ikalira.

Ndiyetu tailozetsani kumbali kuopa kuti chipolopolo chingafwanthuke…

Ndikudziwa chomwe ndikuchita, apapa olo zitachita kuvuta kotani singalire.

Related Articles

Back to top button