Editors PickNational Sports

Nam yagwira utsi, Tigresses ipambana mlandu

Listen to this article
Tigresses, Mhango ndi timu yake tsopano ndi amfulu
Tigresses, Mhango ndi timu yake tsopano ndi amfulu

Choona chavumbuluka, zenizeni zakulumana pakati pa bungwe loyang’anira zamasewero a ntchemberembaye la Netball Association of Malawi (Nam) ndi timu ya Tigresses tsopano zili pa mbalambanda.

Loweruka pa 21 September chaka chino Nam idalamula Tigresses kuti isapikisanenawonso m’chikhochi timuyi itaseweretsa Lauren Ngwira yemwe amati adali wotupa mchombo. Masewerowo amachitikira ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe.

Patsikulo Tigresses imasewera ndi Civonets m’masemifayinolo. Nam idalanda mapointsi anayi kwa timuyi ndipo idayitana matimu a Mafco ndi Karonga kuti apunthane polimbirane kukakumana ndi Civonets.

Pabwalopo ndiyetu padali utsi, osewera a Tigresses kukana kutuluka mpaka Nam itafotokoza bwino. Akuluakulu ena a Nam akuti adagwiridwa.

Kutsatira izo, osewera a Tigresses adasiyidwa m’ndandanda wa osewera a timu ya dziko lino amene anyamuka dzulo kupita ku Australia. Mphunzitsi wa timu yayikuluyi Griffin Saenda adati Nam ndiyo yamuuza kuti osewerawo asatengedwe.

Koma Lachinayi bungwe loona zamasewero m’dziko muno la Malawi National Council of Sports lidagamula kuti Nam ilibe mphamvu yolanda mapointsi a Tigresses komanso sikuyenera kuchotsa timuyi m’chikhocho.

Malinga ndi kalata yachigamulocho, bungweri lidayitanitsa mamulumuzana pazamasewero monga Patrice Nkhono, Yasin Osman, Krishna Achuthan ndi Griffins Longwe.

Mwazina akamunawa adati Nam sidatsate ndondomeko yake yothamangitsira Tigresses m’chikhocho.

“Komitiyi idaunikanso ngati kusiyidwa kwa osewera a timu ya Tigresses kumakhudzana ndi nkhaniyo monga timu ya Tigresses ikunenera. Ngati ndichoncho ndiye Nam idachita molakwitsa komanso mopanda dongosolo lake,” mbali ya chigamulocho idatero.

Gamuloli lidatinso ngakhale Tigresses idaseweretsa wosewera wotupa komabe Nam ikuyenera kupeza chilango kuchokera m’malamulo ake kuti ilange wosewerayu.

Ngakhale zili choncho padali chikayiko osewera a timuyi amene adasiyidwa kutimu yayikulu monga Grace Mwafulirwa Mhango, Sindi Simtowe, Beatrice Mpinganjira ndi Ngwira angatengedwe.

Mphunzitsi wa timuyi Charles Mhango wati zomwe Nam imafuna kuti osewerawa asiyidwe m’ndandandawo zakwaniritsidwa.

Timu ya dziko linoyi imayembekezereka kunyamuka dzulo pa 11. Timuyi yayenda ndi osewera 12 mwa osewera 20 amene adayitanidwa kukampu.

Related Articles

Back to top button
Translate »