Nkhani

‘Ndalama za mthandizi siziphula kanthu’

Listen to this article

Pomwe anthu akumudzi amayembekezera kuti kuonjezera kwa ndalama zomwe azipeza akagwira ntchito ya mthandizi kuchepetsa ululu wa njala, Tamvani wapeza kuti vutoli langosintha m’mafigala koma moyo ukadali chimodzimodzi.

Boma litalengeza mu August kuti laonjezera ndalama za pologalamuyi, padali chiyembekezo chakuti banja lizitha kugula matumba awiri a chimanga a 50kg likagwira ntchito ya chitukuko kapena thumba limodzi kuchokera ku ndalama ya mtukula pakhomo.

Anthu akumudzi amapulumukira ntchito za Mthandizi ngati izi
Anthu akumudzi amapulumukira ntchito za Mthandizi ngati izi

Nduna ya zachuma Goodall Gondwe idalengeza kuti ndalama za pologalamuyi zawonjezeredwa kufika pa K13.2 biliyoni kuti banja likagwira ntchito ya chitukuko lizilandira K14 400 ndipo mabanja olandira ndalama za mtukula pakhomo azilandira K6 500 pamwezi.

Gondwe adati boma lidapanga izi pofuna kuti anthu ambiri, makamaka akumudzi, athe kupeza ndalama zogulira chimanga kumisika ya Admarc pofuna kupulumutsa anthu pafupifupi 6.5 miliyoni omwe akukhudzidwa ndi njala chaka chino.

Nkhaniyi idatanthauza kuti ndi K14 400, banja likadamagula matumba awiri a chimanga pamtengo wakale wa K5 500 ndi kutsala ndi K3 400 yopangira zinthu zina, pomwe a mtukula pakhomo bwenzi akugula thumba limodzi nkutsala ndi K1 000 yapamwamba.

Lipoti loona za chiwerengero cha anthu m’Malawi muno la National Statistical Office (NSO) la m’chaka cha 2000, limasonyeza kuti banja lililonse lili ndi anthu pafupifupi 5 ndipo malingana ndi buku la ndondomeko zapamwamba za ulimi, munthu mmodzi wamkulu amafunika kudya matumba 6 olemera 50kg pachaka.

Izi zikutanthauza kuti pamwezi munthu mmodzi amafunika makilogalamu 25, kuyimirira matumba awiri ndi kota pa banja la anthu 5 pamwezi umodzi.

Kutengera pamtengo watsopano wa chimanga wa K12 500, banja lodalira ntchito ya chitukuko lizikwanitsa kugula thumba limodzi la chimanga nkutsala ndi K1 800 pomwe odalira mtukula pakhomo aziyenera kuonjezera K6 000 kuti agule thumba limodzi.

Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalengeza atangofika kumene kuchokera ku America kuti Admarc ikweze mtengo wa chimanga kufika pa K12 500.

“Ndalamula bungwe la Admarc kuti ligulitse chimanga pamtengo wa K250 pakilogalamu. Uwu ndi mtengo womwe Admarc imagulira chimanga kuchokera kwa alimi,” adatero Mutharika.

Mneneri wa bungwe la Admarc Agnes Chikoko adati padalibe njira ina yopewera kukwenzaku kaamba kakuti mtengowu ndi womwe bungweli limagulira kwa alimi, kutanthauza kuti likungofuna kubweza zake kuti chaka cha mawa lidzathenso kugula.

“Umenewu ndiye mtengo womwe timagulira kuchokera kwa alimi ndiye sitingagulitse pamtengo wotsikira pamenepa chifukwa tidagula ndi ndalama za ngongole zofunika kubweza kuti chaka chamawa tidzathe kupeza ngongole ina,” adatero Chikoko.

Iye adati pakalipano bungweli lili ndi chimanga chokwanira kudzafika nyengo yokolola pomwe anthu angadzayambe kudalira zakumunda moti kulephera kupeza chakudya, akhala mavuto ena kwa anthu.

Bungwe la Alliance Capital Limited ndi bungwe la Transformation Alliance adauza nyuzipepala ya Fuko yomwe imasindikizidwa ndi kampani ya Nation Publications Limited (NPL) kuti mtengo watsopanowu upangitsa kuti mavenda nawo akweze mitengo yawo mosaganizira.

Potsatira chenjezoli, Tamvani  adafufuza mitengo m’misika ina ndipo adapeza kuti kwa Goliati ku Thyolo, chimanga chili pa K12 500 pa thumba la 50kg; Kasungu K9 000, kwa Che Musa ku Blantyre ndi K13 000, Zingwangwa K14 000 ndipo Mzuzu K11 250 pa thumba la 50kg.

Anthu omwe adalankhula ndi Tamvani adati boma likhoza kupereka zifukwa zokwezera mtengo wa chimangawu koma zifukwazi sizikutanthauza kuti anthu apepukidwa chifukwa agulabe chimangacho kuti apulumuke.

“Boma likhoza kupereka zifukwa zambirimbiri zokwezera mtengowu koma zifukwazo sizikutanthauza kuti anthu apeza chimanga mosavuta komanso afune asafune, akakamizidwa kugula kuti asafe ndi njala,” adatero Damiano Limbani wa ku Katondo m’boma la Lilongwe.

Aureliano Banda wa ku Nambuma m’boma lomweli adati iye ndiwokayika ngati kukweza mtengoku kudadutsa mukufuNsa maganizo a anthu ndi kuunika momwe anthu aliLi pa nkhani ya zachuma.

“Akadakhala kuti akuluakuluwa amapita m’midzi mwenimweni kukaona momwe zinthu zilili, si bwenzi kusintha kwinaku kukukhala momwe kumakhaliramu, ayi. Mwachitsanzo, m’midzimu muli umphawi wadzaoneni wosowa kolowera nawo,” adatero Banda.

Janet Zgambo, wabizinesi mumsika wa Mchesi, adati zoona zake za kukula kwa vutoli zioneka ndi momwe anthu azipezekera m’misika ya Admarc, makamaka m’miyezi yomwe ikudzayi.

Kampani ya Alliance Capital Limited idatulutsa chikalata posachedwapa chomwe chidasonyeza kuti anthu ambiri sadapite kukagula chimanga kumisika ya Admarc potsegulira. n

Related Articles

Back to top button