Nkhani

‘Ndalama zaperewera m’magawo ofunikira’

Listen to this article

Ngakhale maunduna a zamalimidwe, umoyo ndi maphunziro alandira ndalama zochuluka kwambiri mundondomeko ya momwe boma liyendetsere chuma kuyambira pa 1 July chaka chino mpaka pa 30 June chaka cha mawa, akadaulo a nthambizi ati ndalama ndi zochepa kupititsa patsogolo ntchito za maundunawa.

Izi zikudza pomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo alowa m’milaga kukambirana ndondomeko ya zachuma imene nduna ya zachuma Goodall Gondwe adapereka pa 19 May.

Ana ena akuphunzira m’zisakasa ngati izi

Mwachisanzo, unduna wamaphunziro wapatsidwa K235 biliyoni, koma mkulu wa bungwe loona zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati kusalana pamaphunziro kupitirira m’dziko muno chifukwa ndalamazo sizikwanira kuthetsa mavuto.

Kondowe adati ndalama zoonjezera zikufunika kuti ana akumidzi apeze maphunziro abwino okweza umoyo wawo.

“Zikungooneka zochuluka koma magawo othandiza kuti tikhale ndi maphunziro abwino sadaganiziridwe. Palibe dongosolo lolemba ntchito aphunzitsi 10 000 a m’sukulu za pulaimale omwe boma lidaononga ndalama kuphunzitsa. Silidaikenso ndalama zoonjezera malipiro aphunzitsi omwe adakwezedwa maudindo. Mabajeti anayi apitawo boma limaika K300 miliyoni yothandizira kukhazikitsa koleji ya aphunzitsi a ana olumala koma chaka chino ayi,” adatero Kondowe.

Popereka ndondomekoyi Gondwe adati unduna wa zamaphunziro walandira ndalama zochuluka polingalira kuti ukuyenera kuonjezera zipangizo m’sukulu za ukachenjede ndi zophunzitsa maluso osiyanasiyana.

Iye adati kupatula apo, undunawu ukuyenera kuonjezera ndi kukonza zofunika m’sukulu zosiyanasiyana kuti maphunziro apite patsogolo m’dziko muno.

“Tikufunitsitsa kuti m’dera la phungu aliyense mukhale sukulu yoyendera ya sekondale ya zipangizo zonse zoyenera monga nyumba yophunzirira sayansi ndi kuwerengeramo mabuku,” adatero Gondwe.

Koma Kondowe adati ndalama yomangira nyumba za sayansi ndi zokwanira m’sukulu 100 zokha zomwe sizifikira ophunzira a kumidzi ndi maphunzirowa.

Iye adati boma likuyenera kukwaniritsa ndondomekoyi chifukwa chaka chatha lidalonjeza kumanga nyumba zowerengeramo zomwe silidamange mpaka pano.

Mmodzi wa akatswiri a zamalimidwe m’dziko muno Tamani Nkhono-Mvula adati ndalama ndi zochepa chifukwa akatswiri adayerekeza K250 biliyoni kapena K300 biliyoni kuti ulimi uchite bwino m’dziko muno. Unduna wa malimidwe udapatsidwa K192 biliyoni pa ndondomeko ya chaka chinoyo.

“Ndizochepa, undunawu ulibe ogwira ntchito 50 pa 100 ofunikira.Gawo la ulangizi likufuna ndalama zambiri chifukwa limagwira ntchito ndi alimi m’midzi.Ndalamazi sizikwanira chifukwa zofunika za unduwa ndi zambiri,” iye adatero.

Mvula adaonjezera kuti ulimi m’dziko muno ukhonza kupita patsogolo ngati boma ndi mabungwe atagwiritsa ntchito moyenera ndalama zomwe zili m’gawoli.

“Ndalama zambiri sizigwira ntchito yake.Malingana ndi mavuto a zachuma, bajeti yachepa koma zochoka ku mabungwe ndi zambiri zomwe zingathandize kuthetsa njala m‘dziko zitalondolozedwa bwino,” adatero Nkhono-Mvula.

Mkulu wa bungwe loona umoyo wabwino wa anthu la Health and Rights Education Programme (HREP) Maziko Matemba adati aphungu ku mlaga wa zaumoyo ku Nyumba ya Malamulo adziwe kuti ndalama zopita ku zipatala za zing’ono komwe anthu m’midzi amapeza thandizo zachepa.

“Boma likulingalira zoika aliyense ali ndi HIV pa ma ARV, koma bajeti ya mankhwala [K10 miliyoni] siyidakwere zomwe zikudzetsa nkhawa ngati ikwanire. Dziko lili m’migwirizano ndi mabungwe monga Global Fund komwe tikuyenera kupereka K11 biliyoni kuti chaka chamawa tilandire mankhwala a chifuwa chachikulu (TB) ndi ma ARV kuchoka pa K129 biliyoni,” adatero iye.

Related Articles

Back to top button