Nkhani

‘Ndale pamaliro n’chitonzo’

Listen to this article

Katswiri pa zachikhalidwe, Emily Mkamanga wati zomwe zakhala zikuchitika pa miyambo ya maliro m’dziko muno ndi belu lozindikiritsa kuti andale si ofunika kuwapatsa mpata wolankhula pa miyamboyi.

Mkamanga adanena izi pamene mpungwepungwe udabuka pamaliro a mayi a Senior Chief Lukwa ku Kasungu pomwe phungu wa deralo wa chipani cha MCP Amon Nkhata adalandidwa chimkuzamawu  ndi gavanala wa DPP Osward Chirwa pomwe mmodzi mwa akuluakulu a DPP Hetherwick Ntaba adathothedwa pamaliropo.  Izi zachititsa mfumu yaikulu ya Achewa ku Zambia, Malawi ndi Mozambique Kalonga Gawa Undi alembere mafumu a kuno kuti afotokoze chimene chidatsitsa dzaye kuti mpungwepungwewo ugwe.

Mmbuyomu, Paramount Lundu idawoozedwa pamaliro a mfumu Kabudula pomwe adanena kuti chipani cha MCP sichingalamulirenso dziko lino. Ndipo kudalinso mpungwepungwe ku zovuta za anthu amene adamira panyanja ku Jalawe m’boma la Rumphi pomwe achipani cha DPP adakhambitsana ndi a Livinstonia Synod ya CCAP.

Mkamanga adati nthawi ya maliro, anamfedwa amakhala m’chisoni ndipo khamu la anthu omwe limasonkhana limadzakuta ndi kukhuza malirowo osati kudzamvera kampeni kapena mfundo za ndale.

“Sindidziwa kuti amaganiza bwanji. Nthawi yoti mnzako akulira, iwe sungasandutse guwa lochitirapo kampeni. Kuli bwino andalewo asamapatsidwe mpata n’komwe woti alankhule pamaliro,” adatero iye.

Iye adati zimamvetsanso chisoni kuti anthu ena amaveka maliro dzina la chipani pomati maliro awa ndi achipani chakuti pomwe pachilungamo chake, chipani chilibe maliro, maliro amakhala a banja.

Chilowereni chaka chino chokha, malilo angapo makamaka a anthu akuluakulu kapena odziwika akhala akusokonekera chifukwa cha zolankhula za andale.

Related Articles

Back to top button