Nkhani

Ndende zisanduka makhoti

Listen to this article

Zanathina m’mabwalo a milandu. Sitalaka ya ogwira ntchito m’mabwalowa idasandutsa zitokosi za polisi kukhala mabwalo ozengera milandu.

Izi zimachitika akuluakulu a mabwalowa atalephera kunyengerera ogwira ntchito kuti asiye sitalakayi ndi kubwerera kuntchito.

Mkulu wa makhoti Andrew Nyirenda adapempha oweruza milandu onse kuti ayambe kuweruzira milandu kupolisi ndi kundende.

Nyirenda adapempha mamajisitiliti kuti agawane ntchito kuti ena azimasulira chigamulo, ena azilemba ndipo ena azinyamula mafailo, ntchito zomwe zimagwiridwa ndi owathandizira.

“Ofesi ya mkulu wa makhoti ikudziwitsa kuti malinga ndi sitalaka yomwe ikuchitikayi, mukupemphedwa kuti muyambe kumva milandu ndipo ngati n’kotheka muzipereka belo,” udatero uthenga wa Nyirenda.

Kutsatira uthengawu, mamajisitileti adayamba kuzenga milandu, komanso kupereka belo kwa anthu oganiziridwa kuti adapalamula milandu omwe amasungidwa m’zitolokosi.

Kupolisi ya ku Limbe mu mzinda wa Blantyre, mamajesitilitiwa adatulutsa anthu angapo pa belo, komanso kumva milandu yosinasiyana. Izi zimachitikira m’chitolokosi.

Nako ku Dedza, mamajesitilitiwa adapatsidwa ofesi yapadera momwe amagwiritsiramo ntchito ngati khoti.

Majesitiliti wina akamaweruza mlandu, mnzake amatanthauzira m’chilankhula chomwe woganiziridwa angamve mosavuta. Wina ndiye amanyamula mafailo. Mkango ukazingwa, umadya udzu.

Ku Nkhata Bay, khoti lidagamula Paulos Lungu kukaseweza kundende zaka zitatu atavulaza Julius Mwaluswa kwa Chinguluwe m’boma lomwelo.

Bwalolo lidathethetsanso Rute Makuluni, yemwe ali ndi zaka 32, kukaseweza miyezi 6 kundende popezeka ndi chamba.

Wapolisi wofufuza milandu wa pa polisi ya Nkhata Bay, Keston Chiona, adati ganizo la Nyirenda lathandizira kuti musakhale kuthinana kwambiri m’zitolokosi zawo.

“Chomwe chikuchitika n’kuti tikumawatenga oweruza milanduwa kuti akamve milandu. Amene wavomera kulakwa akumupatsiratu chilango. Amene wakana akumupatsa belo kapena kumutumiza kulimande,” adatero Chiona.

Naye mneneri wapolisi m’chigawo chakumpoto, Peter Kalaya, adati polisi zonse zam’chigawocho zimatsata ndondomekoyo.

“Timamanga anthu tsiku lililonse kutanthauza kuti zitolokosi zathu n’zodzadza. Njira iyi ikuthandiza,” adatero Chiona.

Malinga ndi mneneri wa makhoti Mlenga Mvula, ganizoli linadza ngati njira imodzi yochepetsera kuchulukana kwa anthu m’zitolokosi za apolisi.

“Ndondomekoyi ikuchitika m’maboma onse,” adatero Mlenga.

Mneneri wa ndende Smart Maliro adati chiwerengero cha anthu otumizidwa kundende kuchokera kupolisi chidatsika chifukwa anthu amangosungidwa m’zitolokosi.

Boma kudzera mwa mlembi wa zachuma Ben Botolo adadzudzula ogwira ntchito m’mabwalowa kuti sitalaka yawo ndi yosavomerezedwa ndipo sizitheka kuti boma lipereke ndalama zanyumba zoyambira m’chaka cha 2012.

Akutero Botolo: “Boma launguza madandaulo anu, koma mfundo ya boma sikusintha—siipereka ndalama zapadera za nyumba.”

Related Articles

Back to top button
Translate »