Nkhani

Ndewu ya gule kudambwe

Listen to this article

Kudali fumbi koboo! Kudambwe la Phingo m’boma la Chikwawa pamene gulewamkulu adaponyerana zibakera pokanganirana zovala zovinira.

Mneneri wapolisi ya Chikwawa Foster Benjamin, gule wina adavulazidwa pamene adamutema pamutu ndi botolo ndipo adamutengera kuchipatala kuti akamusoke.

Kudavuta ku Chikwawa, gulewamkulu kutola mwala

Izitu zimachitika mmawa cha m’ma 7 Lamulungu pamene guleyu amafuna avale kuti atakase kudambweko.

Benjamin adati kudambweko kudasonkhana anthu amene amafuna kuvala gulewamkulu. Mnyamata wina, Innocent Tayi akuti adapitako koma alibe zovinira.

Izi zidachititsa kuti iye apemphe mnzake, Colless Tiwa kuti amubwereke zovala zake koma adakanizidwa.

“Tayi adakakamira mpaka ndewu idabuka pakati pa iye ndi Tiwa,” adatero Benjamin.

Podziwa kuti avulazidwa, Tayi, 17, adatola botolo lagalasi ndi kumenyera nalo Tiwa pamutu mpaka kutemeka.

Malinga ndi Benjamin, anthu am’mudzi ndiwo adathamangira kudambweko kukaleletsa ndewuyo.

“Dambwelo lili pafupi ndi mudzi ndiye pamene anthuwo amamva kulira adathamangirako kuti

akaone chimene chimachitika. Kenaka adagwira Tiwa kubwera naye kupolisi komwe tidamutsekera Lamulungu pamlandu wovulaza komanso tidamutengera kuchipatala Tayi,” adatero.

Tiwa adamutsegulira mlandu wovulaza. Koma Lachiwiri Tayi atatulutsidwa kuchipatala, adapita kupolisiko kukathetsa mlandu.

Paramount Lundu ya m’bomalo yati izi zimachitika kuti anthu pena amasemphana Chichewa. “Nanga pali nkhani pamenepo? Inu simusemphana ndi anzanu?” idafunsa mfumuyo.

Titafunsa ngati m’bomali muli gulewamkulu, Lundu adati Chikwawa ndi kuchimake kwa gulewamkulu.

“Inu simudziwa kuti kuno ndi kwawo kwa gulewamkulu? Simukudziwa kuti m’chaka cha 1969 Kamuzu Banda adadzafika kuno komwe ndi kudambwe langa? Kuno tili ndi gulewamkulu,” adatero Lundu amene adati kudambweko aliyense amakhala ndi zovala zake.

Koma mkulu wa bungwe la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) George Kanyama Phiri adati zimene wapanga gulewamkulu ku Chikwawa ndi chisonyezo kuti amenewo si ometa.

“Tikamakamba za gulewamkulu timanena za chigawo chapakati ndi ku Blantyre pang’ono koma osati ku Chikwawa,” adatero Kanyama.

“Komanso muyenera kudziwa kuti gulewamkulu ndi mizimu ndipo imachokera kumanda. Sibwino kusambira gulewamkulu.”

Masiku apitawa, gulewamkulu amavutitsa ku Mchesi mumzinda wa Lilongwe pamene amagenda galimoto ngati samupatsa ndalama.

Related Articles

Back to top button