Chichewa

Ndime ya vakabu yapita, koma samalani

Listen to this article

 

Ena mwa anthu okhala mumzinda wa Mzuzu ati ngakhale bwalo lounika za malamulo oyendetsera dziko lino lidati lamulo la vakabu nlosayenera, apolisi ayenera kukhala tcheru pogwiritsa ntchito malamulo ena owapatsa mphamvu zomanga anthu opanda chilolezo cha bwalo la milandu(warrant of arrest)kuopa zigawenga kutengerapo mpata wozunguza anthu usiku.

Lachiwiri lapitali  oweruza milandu atatu: Zione Ntaba, Micheal Mtambo ndi Sylvester Kalembera adalamula kuti gawo 184(1) (c) ya malamulo a dziko lino ngolakwika ndipo sakugwirizana ndi ulamuliro wa demokalase omwe uli mdziko lino.

Venda wina wogulitsa majumbo Mayeso Gwanda ndiye adatengera nkhaniyi ku bwaloli mothandizidwa ndi woimira milandu Mandala Mambulasa.

Kadadzera: Anthu
asadere nkhawa

Pomwe Msangulutso udacheza ndi ena mwa anthu okhala mzinda wa Mzuzu, mmodzi mwa anthuwa Chrissy Phiri yemwe amakhala ku Masasa mzindawu

adati sadasangalale ndi kuchotsa kwa lamuloli ata kaamba koti zigawenga zipezerapo danga lozunguza anthu maka usiku.

Phiri adati zigandanga zambiri zimaenda usiku ndipo ndi lamulo la vakabu, apolisi amatha kuzilonda mpaka kuzigwira.

“Ndili ndi mantha kuti zigawenga zikhonza kupezerapo mwai pakuchotsa kwa ndimeyi,” adatero Phiri.

Pomwe Frank Chisale adati vakabu imalakwika poti pena apolisi amanyamula aliyense ndi wosalakwa omwe.

“Nthawi zina amanyamula ndi opita kumapemphero ausiku omwe,” adatero Chisale.

Iye adati apolisi amayenera kunyamula okhawo omwe akuganiziridwa kuti ndi zigawenga kapena apalamula mlandu.

Koma polankhulapo, mneneri wa ku likulu la polisi ku Lilongwe James Kadadzera adati anthu asadere nkhawa kaamba koti apolisi azikwidzingabe  oganiziridwa kuti ndi zigawenga pogwiritsa ntchito malamulo ena.

Kadadzera adati izi zithandiza kuchepetsa umbava ndi Umbanda ngakhale achotsa ndime ina ya ya gawo 184(1) ya malamulo yomwe imakamba za vakabu. Iye adati lamuloli lithandiza kutsatira ndi kutsekera mchitokosi oganiziridwawa ngakhale oyenda pansi koma alibe zida sazinjatidwa.

“Okha okhawo omwe apezeka ndi zida zowopsa ndiwo azikwidzingidwa ndi unyolo mpaka kuimbidwa mlandu poyesetsa kuteteza mzika za dziko lino,” adatero Kadadzera.

Ndime yachotsedwayi  imapatsa mphamvu apolisi kugwira ndi kutsekera m’chitokosi  munthu aliyense wooneka kuti akhoza kudzetsa chisokonezo kapena ali ndi zolinga zochita zosemphana ndi malamulo kumene kaya ndi mu msewu kapena mmalo ena ndi ena.

Bwaloli lidanenetsa kuti ndi kandime kokhaka komwe kali kosayenera ndipo ndime zina zonse m’gawo lonselo zikhoza kugwiritsidwa ntchito.

Oweruzawa adapemphanso Amalawi kuti asatanthauzire kuchotsa kwa ndimeyi molakwika, apolisi azimangabe anthu pogwiritsa ntchito malamulo ena. n

Related Articles

Back to top button