Nkhani

‘Ndinkamphunzitsa kuimba gitala’

Listen to this article

Pa 29 October chaka chino, anthu mumzinda wa Lilongwe adaona zachilendo pamene mkwati ndi mkwatibwi adakwera chitharakitale chokonza misewu osati Benz monga ambiri amachitira. Uwutu udali ukwati wa Sally Nyundo, katakwe woimba chamba cha Reggae, ndi Tionge Kalua. Nyundo adatchuka kwambiri ndi nyimbo yake yotchedwea Ras amadya nzimbe.

Ukwatiwutu adadalitsira pampingo wa Lilongwe Pentecostal pomwe madyerero adali ku Louis Garderns ku Area 3 mumzinda womwewu wa Lilongwe.

Nyundo ndi mkazi wake
Nyundo ndi mkazi wake

Nyundotu akuti adakumana ndi mkazi wake Tionge panthawi yomwe njoleyi inkafuna kuphunzira kusewera gitala.

Iye adati Annie Matumbi,naye m’modzi mwa oimba kuno ku Malawi, ndiye adauza Tionge kuti Nyundo ndi kadaulo pa nkhani za magitala ndipo akhoza kumuphunzitsa bwino lomwe.

“Ndinamuuza Matumbi kuti ampatse nambala yanga tilumikizane. Tidalankhulana pafoni ndipo adaguladi gitala. Apapatu nkuti tisadakumanepo. Tidakumana pa Cross Roads mumzinda wa Lilongwe kuti tiuzane za maphunziro a gitala,” adalongosola motero Nyundo.

Iye adati komatu maphunziro amayenda mwamanyazi chifukwa aliyense adali ndi mawu kukhosi koma amasowa woyambitsa.

Malinga ndi Nyundo, m’manyazimu mudautsa kachikondi kanchibisira.

“Ndidakopeka naye mtima chifukwa adali munthu wodekha, wozichepetsa komanso maonekedwe ake okongola,” iye adatero.

Koma pajatu naye mkazi amakhala nayo mbali yake yomwe amakopedwera ndi mwamuna, ndipo kwa Tionge, adakopeka ndi kudzichepetsa komanso kucheza bwino ndi anthu kwa Nyundo.

“Tidadziwana bwino lomwe ndipo aliyense adali wofunitsitsa kumanga banja,” Nyundo adalongosola.

Awiriwatu adakhala paubwenzi kwa zaka zitatu ndipo akumana ndi zovuta monga zokambakamba zambiri zochoka kwa anthu omwe samawafunira zabwino, komatu sadazitengere izi, adamasukirana ndi kumvetsetsana.

“Tidatseka makutu, nthawi zomwe tinkakumbutsana za chikondi chathu. Ndipo akazi anga nthawi zonse ankandilembera timakalata tachikondi takupulaimale monga ta ‘kiss to kiss’ ndi ‘love to love’, zomwe zinkakometsa chikondi chathu. Komanso tinkakhala ndi nthawi yambiri yopita ku picnic kukacheza,” adatero Nyundo.

Related Articles

Back to top button
Translate »