Ndithu chili ndi mwini

Kusankha Balaba

Kumukana Yesu

Usapange mistake, chonde chonde

Nyimbo ya Evans Meleka idali kuphulika pa Wenela tsiku limenelo.

Ya Ndirande iyi! Machinjiri inayo! Za Lilongwe mpaka ku Area 18 mwinamo!

Koma abale anzanga, ngati pali dera limene latchuka zedi zaka zimenezi ndiye ndi Area 18. Pajatu nanenso mizu yanga ili ku Upper Area 18, inde kuja kwa Senti! Chomwe ndimadabwa nchoti akaphika nsima imakoma ngati muli kale soya pieces.

Abale soya akanakhalako ndi khalidwe. Akanangosankha chimodzi. Soya yemweyo ena akukonza mkaka. Soya yemweyo ena akukonza masoseji! Akanakhala ndi khalidwe soyayu.

Kumukana Yesu

Kufuna Balaba!

Nyimboyi idavuta kwambiri pa Wenela tsiku limenelo potengera ndi zija zidaachitika kwa Chinsapo. Atitu kumeneko chigandanga china chotchedwa Balaba chidaphedwa n’kuvulidwa chinochino.

Ya Ndirande iyi! Ya Machinjiri iyo! Ya ku Area 18 inayo!

“Mkulu anali oopsa uyu. Ngakhale apolisi amamuopa, moti anthu akakanena kupolisi kuti Balaba akuwasautsa, apolisiwo amaneneratu kuti mukamugwira Balaba mumubweretse kuno. Mpake anthuwo anamupititsa Balaba wakufa kupolisiko,” adatero Abiti Patuma.

Kusankha Balaba

Kumukana Yesu

Usapange mistake, chonde chonde!

“Ndipo ndangomva kuti mkulu wina wa kampani ya alonda wapeza tender yolondera polisi ya pa Wenela. Koma zisatikhudze,” adatero wa pamalopo, Gervazzio.

Gervazzio adayatsa kanema. Padali MBC-TV ndipo adabwera Jeffrey Kapusa. Adali kuulutsa nkhani ya mwana wina amene adagwiriridwa ndipo apolisi komanso amene amayenera kumuthandiza ena sanatero, msungwana kumangolira.

“Anthu ogwirira anawa tikadatha kuwatchula kuti zitsiru, koma sititero chifukwa mawuwo siwoyenera kuwatchula pagulu. Choncho tingoti ndi wopusa. Si zitsiru ayi,” Kapusa adali kutero. Mr Splash!

Mawu ake ali mkamwa, adatulukira Moya Pete.

“Ndakwiya khwambiri. Anthu inu ndi zitsiru! Ndinu zitsiru kwambiri! Zitsiru zakumwa madzi wochapira ndevu,” adali kutero Moya Pete.

Kenako, adatenga cholembera, n’kulemba pamalaya a Gervazzio: Chitsiru.

Gwira bango! Upita ndi madzi iwe! n

Share This Post