ChichewaEditors Pick

Ngakhale ng’amba ikuwaula mmera, akuchilimikabe

 

Nkhani ya ng’amba siyochita kufunsa chifukwa momwe zikuwaukira mbewu m’minda ndiumboni wakuti dzuwa lalanda malo a mvula. Alimi ambiri pano manja ali m’khosi ndipo ena angofika potailatu mtima. Ngakhale zinthu zili choncho, alimi ena sakugonja ndipo akuti sangachoke m’munda pokhapokha ataona kuti mbewu yomalizira yauma ndi dzuwa. Loveness Billy a ku Salima ndi mmodzi mwa alimi olimbika chonchi ndipo STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Mlimiyo pakati pa munda wake wochititsa chidwi
Mlimiyo pakati pa munda wake wochititsa chidwi

Moni mayi komanso ndikudziweni.

Ndili bwino. Dzina langa ndi Loveness Billy ndimachokera m’mudzi mwa Mjunga ku Salima.

 

Tsono pamenepa mukutani?

Apa ndikupala udzu m’chimanga mwangamu kuti chikule bwino mosanyozoloka chifukwa chosokonezedwa ndi udzu kapena zomera zomwe si gawo la mbewu zanga.

Komatu chimangachi chikuoneka ngati palibepo chomwe mungatole ndi mmene chaumiramu.

Anthu owonanu mukuganiza choncho koma mwini wakene ndikuona kuti chiyembekezo chikadalipo. Mvula itangoti ibwere mukhoza kuona mmene chinganyamukire. Mmene ndikupala chonchimu, zindithandiza kuti chinyontho chochepa chomwe chilipo m’nthakamu chigwire ntchito ku mbewu zokha osati kulimbirana ndi udzu.

 

Mesa boma likuti ndi mmene zinthu zililimu mukuyenera kukangalika ndi mbewu zina zopirira ku ng’amba?

Zimenezo tikutsatiranso moti chakumunsi kwa mindayi kuli madimba komwe tagaula kale ndipo pompano tikabzalako mbewu zinazo monga nyemba, kachewere, mbatata ndi chinangwa. Chinangwacho ndiye tidabzala kale koma pano tikufuna kukabzala mbatata chifukwa timasakasaka mbewu ndiye yapezeka.

Alimi anzanutu atambalala kusungira mphamvu kuti mvula ikagwanso adzaunde mizere ya mbatata kapena chinangwa.

Ayi amenewo ndiwosamvetsa chabe chifukwa ngakhale a bomawo sakunena kuti tizule kapena kunyanyala chimanga koma kuti pambali pa chimangacho tibzalenso mbewu zina. Palibetu vuto kusakaniza mbewu zinazo ndi chimanga makamaka pomwe malo ali ochepa. Mwachitsanzo, munthu akhoza kubzala mbatata mmphepete mwa mzere wa chimanga. Chimanga chikakula pang’ono amatenga mbewu ya mbatata nkubzala ndipo zonse zimakula bwinobwino.

 

Inu mumachitaponji pa zaulimi wa mthirira?

Ulimi umenewonso timapanga mchilimwe. Tidakumba madamu okololeramo madzi omwe timagwiritsa ntchito kuonjezera omwe timapatutsa mumtsinje chifukwa mtsinjewo pena madzi amachita kutheratu nanga ogwiritsa ntchito si ambiri kuyambira kumtunda komwe udachokera mpaka kumunsi.

 

Mwakonzekera bwanji ulimi wa mthirira?

Pakadalipano tikuyang’anabe zipangizo zina makamaka mbewu ndi feteleza koma zina monga madzi ndi muja ndafotokozera kale kuti kupatula mumtsinje, tili ndi madamu okololera madzi. Ikakhala ntchito ina monga kugaula ndi kuunda mizire ziri mkati mmadimba ena pasi pakadali pofewa.

 

Kugawuliratu pano ndiye podzafika chilimwe sipadzakhala patalimbaso?

Ayi timalawirira kukatchefula mvula ija ikangotha pansi pakayamba kuchita mbuuu. Siyikhalanso ntchito yowawa komanso tikatero timadzipatsa mpata wokwanira wothira manyowa kuti ndi chinyontho chija, dothi ndi manyowawo zilowererane bwino.

 

Inu mungawauze chani alimi anzanu omwe ataya mtima?

Asataye mtima koma akhale ndi chikhulupiliro zonse zidzakhala bwino. Vuto ndilakuti akatambalala, pomwe mvulayi idzabwerenso adzakhala ndi chintchito chachikulu. Chofunika nkungosamala mbewu zomwe zidamera kalezi nanga sipadalowa kale zambiri. Mvula ikadzabweraso tizidzangopakiza momwe mbewu zaferatu.

Related Articles

Back to top button