Nkhani

Njengunje pothana ndi matenda a khansa

Muli ntchito yaikulu m’dziko muno kuti odwala matenda a khansa apeze mpumulo. Izi wanena ndi yemwe adapulumuka ku matendawa, Blandina Khondowe.

Khondowe adaononga K5 miliyoni kuti apulumuke ndipo adachita kupita m’dziko la India zitakanika kuti athandizidwe m’dziko muno.

Mpaka zafikatu pamenepa, amayi kufola pa mzere kuti ayezetse khansa

Malinga ndi mkulu woyang’anira ntchito za umoyo mu unduna wa zaumoyo Charles Mwansambo, zipatala za Kamuzu Central ndi Queen Elizabeth ndi zokhazo zomwe zili ndi ukadaulo wa matendawa.

Kutanthauza kuti kupatula malowa, kulibenso kwina komwe wodwala angapite m’dziko muno.

Boma lidakhazikitsa ntchito yomanga malo wothandizita anthu odwala khansa mu 2007 koma mpaka pano malowa sadayambe kugwira ntchito.

Kwa Khondowe, ili ndi vuto lalikulu lomwe likuika pachiopsezo odwala matendawa.

“Kupatula kuti tili ndi zipatala zochepa, vuto lina ndi la zipangizo,” adafotokoza, “ineyo ndidazindikira kuti bere langa limalimba mchaka cha 2011 ndipo kwa zaka ziwiri ndimayenda m’zipatala koma amangondiuza kuti ndi chotupa, mpaka pamene ndidaganiza zopita ku India.”

Khondowe adaonjeza, “nditapita ku India, ndidaononga K5 miliyoni.” “Ndi angati angakwanitse ndalama zoterezi? Pokhapokha titapereka mphamvu zambiri ku zipatala zathu, anthu apitirirabe kufa ndi khansa.”

Mmodzi mwa akadaulo pa matendawa, Leo Masamba adati pakali pano, chaka ndi chaka, anthu pafupifupi 18 000 amapezeka ndi khansa.

Iye adati mwa anthuwa, amene ali pamoto ndi anthu akumudzi omwe chuma ndi chowavuta.

“Kuperewera kwa zipatala kukuzuza kwambiri anthu akumudzi chifukwa alibe ndalama kuti akapeze thandizo,” adatero Masamba.

Iye adati chofunika ndi kumema Amalawi kuti athandize boma kukwaniritsa pologalamu yokhazikitsa malo othandizirako anthu a vuto la khansa m’zigawo zonse za dziko lino.

Malinga ndi iye, mankhwala oyenera, zipangizo zogwirira ntchito, ogwira ntchito odziwa bwino ndi galimoto zokwanira zonyamula anthu osowa mayendedwe ndi zinthu zomwe zikufunikira.

Akatswiri pa za umoyo ati pokhapokha patachitika chozizwa, Amalawi apitilira kupululuka ndi matendawa chifukwa cha kusowekera kwa zipangizo komanso zipatala.

Mkulu woyang’anira nthambi yothandiza ku matenda a khansa pa chipatala cha Kamuzu Central, Richard Nyasosela wati chipatalachi chimalandira anthu osachepera 30 sabata iliyonse.

Steady Chasimpha wa ku nthambi yowona za matenda a khansa wati ku Queen Elizabeth Central Hospital, anthu ofuna thandizo sachepera 22 pa sabata imodzi.

Iye wati nambala zochuluka chotere nzowopsa poyerekeza kuchepa kwa ogwira ntchito ku nthambi za khansa ndi zipangizo zothandizira anthu ovutikawo.

“Nambala imeneyi ikusonyeza kuti zinthu sizili bwino, ndipo tikatengera vuto la ogwira ntchito ndi zipangizo, thandizo loperekedwa silingakhale loyenera,” adatero Chasimpha.

Kusowekera kwa zipatala kwachititsa kuti anthu ena m’midzi azipita kwa asing’anga kukalandira thandizo.

Mtsogoleri wa asing’anga m’dziko muno, Frank Manyowa akuti patsiku amalandira anthu pafupifupi asanu atatu odwala khansa.

“Ambiri mwa anthuwa sapulumuka chifukwa asing’ana ena amangofuna adyepo ngakhale sangakwanitse,” adatero.

Anthu pafupifupi 52 ndiwo amapezeka ndi matenda a khansa pa sabata m’dziko muno, pakutha pa mwezi, anthu pafupifupi 204 ndiwo amapezeka ndi matendawa.

Koma Khondowe akuti kutengera zomwe madotolo adamuuza ku India, khansa ndiyochizika ikapezeka mmasiku oyambilira komanso thandizo loyenera likakhala pafupi. “Apo ayi ndiye amakangodula chiwalo mukachedwa kulandira thandizo.”

Lero Khondowe adayambitsa bungwe la ‘Think Pink’ lomwe limapita m’madera osiyanasiyana kuphunzitsa anthu za khansa ndi kuwalimbikitsa kuti azikayezetsa.

Related Articles

Back to top button