Chichewa

Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake

 

Akamaimba nyimbo ya Musalolere Mulungu Ephraim Zonda amaimba ndi mtima wonse polingalira kuti akulowa m’banja mwezi ukubwerawu ndipo Mulungu asalolere kuti adani alepheretse zimenezi.

Atupele ndi Ephraim kukonzekera kudzakhala thupi limodzi
Atupele ndi Ephraim kukonzekera kudzakhala thupi limodzi

Ngati kumaloto, Ephraim       akamakumbukira tsiku lomwe adaonana ndi Atupele Chikaya. Akuti sadadziwe kuti iwo akhoza kudzakumananso.

“Ndidamuona koyamba Atupele ku tchalichi cha Zambezi ku Kawale komwe tinkakaimba. Panthawiyo sitidayankhulane koma mwachisomo cha Mulungu tidakumananso ku Chefa komwe tidakaimbanso,” adatero Ephraim.

Mnyamatayu ndi wachiwiri kubadwa m’banja la ana asanu ndi awiri. Ali ndi luso lopeka nyimbo komanso ali ndi mawu anthetemya moti amaimba mukwaya ya Great Angels. Si zokhazo, amachitanso bizinesi yogula ndi kugulitsa katundu wochokera ku China kuphatikizapo galimoto.

Atupele ndi wachiwiri kubadwa m’banja la ana anayi ndipo amagwira ntchito ku Road Traffic ku Zomba.

Awiriwa adayamba kucheza muchaka cha 2009 pomwe adakumana ndipo patatha chaka akucheza chomwecho Ephraim adamufunsira Atupele ataona kuti ndi mkazi wabwino.

“Atupele ndi mkazi amene ali ndi zomuyenereza zomwe mwamuna aliyense amafuna pa mkazi. Atu ndi mkazi wakhalidwe, woopa Mulungu, wanzeru komanso womvetsetsa,” adatero Ephraim akunyadira bwezi lakelo.

Patatha zaka zisanu ndi chimodzi chikumaniraneni, awiriwa adaganiza zomanga ukwati kuti anthu atsimikize za chikondi chawo.

Ukwati wawo uliko pa 12 September chaka chino ndipo akadalitsira ku mpingo wa CCAP ku Area 23 mumzinda wa Lilongwe ndipo madyerero akakhala ku Capital Hotel.

Ephraim adanenetsa kuti chomwe chidzawalekanitse iwo ndi imfa basi. Iye adati nthawi yawathandiza kudziwana, zomwe iye akuti zidzawathandiza m’banja mwawo.

Ephraim amachokera m’mudzi mwa Mutchindwe, T/A Malanda m’boma la Nkhata Bay ndipo Atupele ndi wa m’mudzi mwa Liwewe, T/A Malengachanzi, ku Nkhotakota.no.n

Related Articles

Back to top button