Nkhani

Oferedwa akusowa mtendere ku ntchisi

Listen to this article

Adanena mawu oti mvula ikakuona litsiro sikata sadaname. Banja la anamfedwa ena ku Ntchisi likusowa mtendere pamene nyakwawa ya m’mudzi mwawo yauza banjalo kuti lichitepo kanthu pa imfa ya ana awo zitamveka kuti ana omwalirawo “auka” ndipo akumagogoda m’makomo mwa anthu.

Koma banja loferedwali lati silikudziwa choti lingachite ndi zomwe zikulankhulidwazo.

Mphenzi ngati iyi ndi yachilengedwe koma ena amaganiza kuti ena amatha kulenga mwamatsenga
Mphenzi ngati iyi ndi yachilengedwe koma ena amaganiza kuti ena amatha kulenga mwamatsenga

Tate wa anawo, Samson Mvula, wa m’mudzi mwa Chungamiro kwa T/A Malenga m’bomalo wati anawo adafa mwangozi pa 17 February chaka chino pamene mphenzi idaomba nyumba yawo.

Iye adati usiku wa ngoziwo iye ndi ana ake anayi adagona pabalaza ndipo mwadzidzidzi kudamveka chiphaliwali chomwe chidakuntha nyumba yawo ndipo m’nyumba monse mudadzadza utsi kuti kobo!

“Adali madzulo cha m’ma 7 koloko. Ine ndi ana onse tidagona pabalaza. Wamkulu adali wa zaka 15, wina 14, 9 ndi womaliza wa zaka zisanu.

“Mphenzi idaomba mvula itangoyamba kumene. Idamenya pabalazapo ndipo m’nyumba monse kudzadza utsi. Ine ndi mkazi wanga tidayamba kutulutsa anawo amene adali atafookeratu. Tidathamangira nawo kuchipatala, koma zachisoni, wa zaka 14 ndi 9 adamwalira, enawo adatsitsimuka ndipo ali moyo,” adatero Mvula.

Pa 18 February mudzi udasonkhana kuwaperekeza anawo kumanda, koma akuti zodabwitsa zidayamba kuoneka.

Mvula adati ali kumandako, anthu ena akuti adayamba kuwaona anawo akuyendayenda maliro ali mkati.

“Adandifunsa ngati ndingakwanitse kuwaona anawo. Ndidawauza kuti ine sindidatemere ndiye sindingakwanitse. Koma amene adatemera ndipo angathe kuona zaufiti amati anawo akuwaona,” adatero Mvula.

Patangotha sabata, akuti mphekesera zidayamba kumveka kuti anthu ena ayamba kukumana ndi anawo. Mmodzi mwa anthuwo ndi nyakwawa Chungamiro yemwe wauza Msangulutso kuti anawo adafika kawiri kunyumba kwake.

“Afika kawiri koma usiku okhaokha, ndidamva mapazi komanso akumagogoda akafika pakhomo, poti ndituluke uona akuthawa,” adatero Chungamiro.

Titafunsa nyakwawayo kuti idadziwa bwanji kuti ndi ana omwe adafa amene ankagogoda pakhomo pakeusiku n’kuthawa?

Idayankha: “Kunena zoona sindidawaone, koma ena amene adakumana ndi anawo masana ndi amene awazindikira. Ndiye chifukwa akumayenda m’makomo kumagogoda, tikungoganiza kuti ndi iwowo amene akuchita izi.”

Mfumuyi yati yalandira madandaulowa kwa anthu oposa 7 ndipo idaitanitsa banja loferedwali Lolemba sabaya yatha kuti iwauze chochita.

“Ndawauza kuti apeze njira kuti mizimu ya anawo igone pansi. Apeza njira, mwina akudziwa chomwe chikuchitika,” idatero mfumuyo, yomwe sidafotokoze njira zake.

Koma tate wa anawa wati nayenso ndi wodabwa kuti amfumuwo amuuza kuti achitepo kanthu pamene iwo sakudziwapo kalikonse za zomwe zikuchitikazo.

“Anthu akungolankhula kuti akumana ndi ana anga koma inenso ndikusowa kuti ndivomereza bwanji chifukwa sindidawaone ngakhale anthu akulankhula choncho. Izi zikutisowetsa mtendere ndipo tikulephera kuiwala mavuto” adatero Mvula.

“Ndikulira ine, ndiye ndilibe mphamvu kuti ndiletse izi. Iwo akuti ndipondeponde koma ndilibe ndalama zopangira zimenezo chifukwa ndalama zanga zidatha panthawi ya zovutazi,” adatero tateyo.

Koma mfumuyi yati anthu akuchita mantha ndi nkhani zikumvekazo n’chifukwa chake idaganiza zoitanitsa banjali kuti lichitepo kanthu.

Anthu ena amene akadandaula kubwalo la mfumuyi ati anawo akumakumana nawo kumunda pena mumsewu pamene ena akuti adafika kunyumba kwawo.n

Related Articles

Back to top button
Translate »