Nkhani

Okwiya aimitsa kumanga njanje

Listen to this article

Madzi achita katondo ku Nkaya m’boma la Balaka komwe anthu okwiya aletsa kampani ya Mota Engil yomwe ikumanga njanje kumeneko kuti isiye kuthira dothi m’minda mwawo komanso galimoto zawo zisadutsenso m’mindamo.

Anthuwa ati sasintha ganizo lawo pokhapokha akuluakulu a kampani ya sitima zapamtunda m’dziko muno omwe akumangitsa njanjeyi ya Central East African Railways (Cear) awapepese.RAILWAY

Kuyambira Lolemba mpaka Lachitatu m’sabatayi, ogwira ntchito pakampu ya Nkaya adangogwira m’chiuno kudikira kuti akuluakulu awo akambirane ndi kugwirizana ndi anthuwo asanayambe kupitiriza kugwira ntchitoyo.

Gulupu Nkaya adatsimikizira Tamvani Lachiwiri kuti anthu ake akwiya ndi zomwe anjanje akuchita pomatayira dothi m’minda yawo popanda kukambirana kulikonse.

“Panopa anthuwo akufuna amvetsetse kuchokera kwa omanga njanjewa pazomwe zikuchitikazo, adabwera kunyumba kwanga kudzandifotokozera koma nanenso ndalephera kumvana nawo ndipo ndawauza anjanjewo kuti aime kaye ntchito yawo mpaka titakambirana,” adatero Nkaya.

Lachiwiri masana akuluakulu a Cear adakhamukira kumaloko kuti akakambirane ndi mfumuyo koma ngakhale Nkaya adatsimikizira anthuwo kuti ntchito iyambiranso, izi sizidachitike.

Malinga ndi mneneri wa Cear, Chisomo Mwamadi, mgwirizanowo udali woti pofika 2 koloko masana a Lachiwiri ntchitoyo ikhala itayambiranso.

Koma polowa kwa dzuwa Lachiwiri, ntchitoyo n’kuti isadayambe, malinga ndi Nkaya.

“Ndayesera kukamba ndi anthu anga onse amidzi ya Nsoma, Mbiya ndi Nkaya kuti awalole anthu agwire ntchito yawo, koma ndalephera.

“Anthu akukana ndipo akuti pokhapokha a Cear awapepese [ndi kena kake osati pakamwa pokha] mpamene awalole kuti apitirize kugwira ntchito. Poyamba tidakambirana ndi akuluakulu a Cear ndipo tidagwirizana kuti tiwalole apitirize kugwira ntchito titagwirizana kuti tsiku lina abwera anthu ena kuchokera ku Cear kuti adzakambirane ndi anthuwo.

“Mpaka lero palibe chogwirika tachiona n’chifukwa chake anthuwa akukana kuti ntchito isagwiridwenso pokhapokha anthu amene adawatchulawo atabwera,” idatero mfumuyi.

Koma mkulu wa Cear, Hendry Chimwaza, adati nayenso ndi wodabwa kuti mfumuyi ikulephera kulamula anthu ake kuti amvere zomwe adagwirizanazo.

“Njanje si yathu, njanje ndi ya anthu ndipo mfumuyi ndi mboni kuti kubwera kwa chitukuko cha njanje kwabweretsa ntchito zambiri zotukula anthu ake monga kulembedwa ntchito ndi malonda kungotchulapo zochepa. Za malo otaya dothi komanso modutsa makina athu tidakambirana koma tikudabwa lero kumva nkhaniyi.

“Mfumu kulephera kukambirana ndi anthu ake? Komabe tisathe mawu, tikambirana nawo ndipo ntchito ipitirira. Tikulankhula pano nkhaniyi taikamba kale ndipo kwatsala nkuona ntchitoyi ikugwiridwa,” adatero Chimwaza Lachitatu.

 

Atafunsidwa ngati nkhaniyi akuidziwa akuluakulu a boma, Chimwaza adati idakali kaye m’manja mwawo ndipo ngati pena patavuta adziwitsa akuluakuluwa.

Kupatula kuthira dothi m’minda, china chomwe anthuwa akudandaula ndi galimoto zikuluzikulu ndi makina awo zomwe zimadutsa m’mindamo.

Mmodzi mwa anthuwo, amene adakana kutchulidwa dzina, adati mgwirizano wawo ndi anjanje udali woti alandira ndalama kuti galimotozo zizidutsa m’minda mwawo komanso kuti azitayira dothi m’dera lawo.

“Poyamba amati angothira dothi mmalo amene minda yakokoloka ndipo dothilo athira ndipo akupitirizabe kuthira moti sitingalimenso n’chifukwa chake tawaletsa,” adatero.

Ntchito yomanga Nkaya siteshoni idayamba chaka chatha mu November ndipo gawo loyamba latha June chaka chino.

Chimwaza adati gawo loyamba lidali kumanga njanje zina ziwiri kuphatikizapo yakale yomwe idalipoyo, kukwanitsa zitatu.

Kumanga kwa njanjezi kuthandiza kuti sitima zitatu zizitha kupatukirana pa Nkaya popanda vuto lililonse komanso azitha kuchulutsa ndi kuchepetsa mabogi, zomwe sizimachitika poyamba.

“Apa ndiye kuti sitima yochokera ku Balaka ingathe kukhotera pomwepa kupita ku Liwonde, kupita ku Mwanza komanso ku Limbe. n

Related Articles

Back to top button
Translate »