Nkhani

Olumala asaiwalidwe, Fedoma yatero

Listen to this article

Makhansala awapempha kuti akamakonza ndondomeko zachitukuko aziganiziranso olumala omwe amasalidwa.

Mkulu wa mapologalamu ku mgwirizano wa mabungwe oona za olumala la Fedoma, Simon Munde, adapempha izi Lachitatu pamsonkhano wokambirana ndi makhansala za mavuto omwe olumala amakumana nawo.

Iye adati zitukuko zambiri siziganizira olumala kuwapangitsa kuti asamatenge nawo gawo pa chitukuko.

“Mmbuyomu timati poti kudalibe makhansala nchifukwa chake zitukuko zambiri zimakhala zokomera anthu alungalunga okha koma pano tachiona chamwayi kuti pali makhansala omwe ndi eni a zitukuko tiwafotokozere zipsinjo zathu,” adatero Munde.

Iye adati ntchito zotukula olumala zimakumana ndi mavuto ambiri monga kusalidwa, kusapatsidwa ndalama zokwanira zogwirira ntchito mundondomeko ya zachuma ndi kusaganiziridwa pa mapulani a zitukuko monga pomanga sukulu, zipatala ndi maofesi.

Mmodzi mwa makhansala omwe adali nawo kumsonkhanowo Peter Chikuse wa ku Nteza kwa T/A M’bang’ombe ku Lilongwe adatsimikizira bungweli kuti adamva madandaulowo ndipo achitapo kanthu.

Iye adatsimikiza kuti anthu olumala amakumana ndi mavuto ambiri omwe sangathe popanda akuluakulu kuchitapo anthu.

“Nzachisoni kuti nthawi zina anthu amakhala ngati sakuona mavuto omwe anzawo makamaka olumala akukumana nawo. Ife mwantchito yathu yopititsa patsogolo zitukuko tikaonetsetsa kuti kumadera kwathuko anthu olumala akuganiziridwa,” adatero Chikuse.

Iye adakumbutsa makhansala anzake kuti ino ndi nthawi yoti aonetse mawanga awo pokwaniritsa kapena kulephera zomwe adalonjeza anthu omwe adawasankha.

Msonkhanowu udachitikira ku Lilongwe ndi thandizo la ndalama lochokera ku National Democratic Institute.

 

Related Articles

Back to top button