Nkhani

 ‘Omanga mvula’ awaothetsa moto likuswa mtengo’

Listen to this article

 

Kudali gwiragwira Loweruka lapitalo m’midzi ya Kazembe, Golosi ndi Ntamba kwa T/A Nkalo m’boma la Chiradzulu pamene anthu olusa adagwira anthu 7 ndi kuwaothetsa moto masanasana ati chifukwa chowaganizira kuti ndiwo ankamanga mvula m’deralo.

Gulupu Ntamba komanso amene amaona nkhani za chitetezo kuderalo, Fanny Chinyanga, atsimikiza kuti izi zidachitikadi koma ngakhale apolisi adadziwitsidwa palibe amene wamangidwa.

Koma mneneri wapolisi m’boma la Chiradzulu, Victoria Chirwa, adati sakudziwapo chilichonse pa nkhani ya kuzunzidwa kwa anthu 7 ndipo adati apolisi afufuza.

Mwa anthuwo, atatu ndi okalamba pamene mtsikana adalipo mmodzi. Atatu enawo adali abambo.

Chinyanga akuti izi zidachitika masana dzuwa likuswa mtengo pamene anthuwo adagwidwa ulendo nawo kubwalo la m’mudzi mwa Ntamba komwe adawakolezera moto kuti aothe.

“Poyamba adagwira okalambawo ndipo adayamba kuululana ndiye amene amatchulidwawo kuti ndiwo akutseka nawo mvula amawagwira ulendo nawo ku bwaloko.

“Anthuwa adawasiya atatsimikizira gululo kuti mvula ibwera mmawa wake. Ndipo kudagwadi mvula yambiri tsiku limenelo,” adatero Chinyanga amene wati kuderalo mvula idasiya mu January.

Iye wati izi zitayamba kuchitika, achitetezo am’deralo adadziwitsa apolisi ya Nkalo koma mpaka pamene anthuwo amamasulidwa, apolisi sadabwere.

“Komabe poti ife ndi achitetezo cha m’mudzi, tikufufuza nkhaniyi ndipo tikawagwira amene adazuza anthuwa ndiye tiwapititsa kupolisi.”

Koma mneneri kunthambi ya zanyengo Elina Kululanga wati ndi kulakwa kuzuza anthu chifukwa cha vuto la mvula ponena kuti palibe amene angamange kapena kutsekula mvula.

Mawu a Kululanga akudzanso pamene miyezi iwiri yapitayo, okalamba anayi adaphedwa kwa Dambe m’boma la Neno kuti adalenga mphenzi yomwe idapha mtsikana wa zaka 17.

“Izi n’zachikale ndipo dziwani kuti palibe munthu angamange kapena kugwetsa mvula. Ngakhale mphenzi silengedwa ndi munthu, koma anthu amaona ngati izi zingatheke.

“Chaka chino mvula yavuta madera ambiri, kotero anthu asaganize kuti alipo amene akukhudzidwa ndi kuvuta kwa mvulaku,” adatero Kululanga, amene adalangiza anthuwa kuti azimvera zanyengo pawailesi kapena kudzera m’nyuzipepala.

“Sabata yathayi takhala tikulosera kuti mvula sibwera ndipo tidanenanso kuti sabata ino kuti chigawo cha kummwera chilandira mvula yambiri ndipo mwaonanso zikuchitika, ndiye anthu azimvera zomwe tikunena.”

Gulupu Ntamba wati panthawi yomwe izi zimachitika, iye n’kuti ali m’nyumba ndipo sangathe kufotokoza zomwepo kanthu.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »