Nkhani

‘Osalanga nokha oganiziridwa ufiti’—Apolisi

Anthu m’mudzi mwa Chimchembere kwa T/A Chekucheku m’boma la Neno adavomera mwa mphamvu kuti ufiti ulipo, makamaka mphenzi  zopanga anthu.

Iwo adanena izi poyankha funso la wapolisi wa m’bomalo, Senior Inspector Evertone Pound, pamwambo wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust wozindikiritsa anthu kuipa kwa mchitidwe wolanga okha oganiziridwa kuti aphwanya malamulo pamsika wa Kambale m’deralo sabata yatha.

Pound: Musalange nokha owakayikira

Pound adati ngakhale mchitidwewu suzindikiridwa m’malamulo a dziko lino, oganiziridwa apititsidwe kupolisi ndipo pasapezeke owalanga m’njira iliyonse.

“Kupha agogo anayi kudachitika chaka chatha poganiziridwa kuti anapha munthu ndi mphenzi sikololedwa ndi malamulo chifukwa ndi udindo wa makhoti kupeza kulakwa ndi kulanga oganiziridwawo. Kaya ndi zokhudza mphenzi, kuphana kapena umbanda, musalange poti kutero ndi milandu wopha munthu ndipo mukakhala moyo wonse kundende kapena wovulaza munthu zaka 7,” iye adatero.

Pound adati wovomera yekha pakhothi kuti ndi mthakati amamangidwa mpaka zaka 6 chifukwa chobweretsa chisokonezo m’dera.

Mlangizi wa bungwe la Nice Trust m’bomalo, Wallace Kudzala, adati akangalika kudziwitsa anthu kuipa kotengera malamulo m’manja mwawo polimbikitsa bata ndi maufulu.

“Aliyense, kaya waba kapena kuganiziridwa kuphwanya lamulo, ali ndi ufulu wokhala ndi moyo komanso kuimbidwa mlandu ndi khoti basi,” iye adatero.

Gulupu Chimchembere ndi wapampando wa komiti ya chitetezo m’deralo, Chelasiti Matemba, adathokoza Nice Trust powawunikira dongosolo la malamulo a dziko lino.

“Nthawi zambiri, kutengera oganiziridwa ku polisi kumavuta chifukwa anthu amafuna kungothana nawo. Apa, tamva ndipo malamulo azitsatidwa,” adatero Chimchembere.

Related Articles

Back to top button