Chichewa

Osauka alibe mawu

 

 

Kwa zaka 12, ena mwa omwe akuwaganizira milandu yakupha akadali pa alimandi m’ndende podikira chilungamo pa milandu yoganiziridwa kuti adapha anzawo. Milanduyi, ikumatenga nthawi kuti iweruzidwe.

Izi zikusemphana ndi gawo 161 la malamulo okhudza milandu ikuluikulu lomwe limati munthu azengedwe mlandu pasanathe miyezi iwiri ndipo ngati zavutitsitsa isadutse itatu.

Komatu zodabwitsa nzoti anthu ambiri omwe akungokhala m’ndendewa asadaweruzidwe, alibe ndalama ndipo sangafikire owaimilira. Choncho amakhala akudikira ndondomeko ya boma pomwe anthu a ndalama zawo akapalamula, milandu yawo imayenda mwachangu chifukwa amapeza owaimira.

Mwachitsanzo, polisi ya Ntcheu chaka chathachi, idatumiza anthu 22 kundende ya Ntcheu, ndipo onsewa, palibe ngakhale mmodzi amene adakalowa bwalo la milandu.

Moyo wa kundende ndi wovuta

Izi zingotanthauza kuti milanduyo yakumana ndi ya chaka chino.

Izi zikukhumudwitsa omenyera ufulu wa anthu m’dziko muno.

Mkulu wa limodzi mwa mabungwewa la Centre for Human Rights Education, Advice and Assistance (Chreaa), Victor Mhango, adati ndende  za dziko lino zikusungira anthu oposa 1 000 pa limandi pa milandu yoganiziridwa kupha.

Mhango adati milandu ya mtunduwu imaweruzidwa ndi bwalo lalikulu lomwe lili ndi oweruza ochepa.

“Milanduyi imakhala yokwera mtengo chifukwa oweruzawa ndi omwe amayendera kuboma la opalamula mlandu. Tsopano ndi kapezedwe ka chuma, zikumavuta kuti aziyenda pafupipafupi kumakaweruza milandu ya mtunduwu,” adatero Mhango.

Iye adati anthu omwe amapeza okha owaimira pa milandu sakhalitsa m’ndendemu chifukwa owaimirirawa amathamanga kuwapezera belo kuti zawo ziyere mwachangu.

“Vuto lagona pa anthu omwe sangakwanitse kupeza owaimilira ndipo amadalira aulere ochokera nthambi ya boma ya Legal Aid. Anthuwa amaiwalika ndipo amatha zaka zambiri ali m’ndende,” adalongosola Mhango.

Iye adati a nthambiyi alibe owaimira pa milandu ambiri zomwe zimachedwetsanso milandu.

Kuchokera chaka cha 2014 mpaka 2016 bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lidatsogolera ntchito yothandiza kuti milandu ina iunikidwenso. Ntchitoyi yomwe inkatchedwa Kafantayeni, idathandiza kuunika milandu ya omwe adapha anzawo 154.

Malinga ndi yemwe ankatsogolera ntchitoyi Peter Chisi, milandu 161 ndi yomwe inkafunika kuunikidwa.

Iye adati ntchitoyi inkalunjika kwa okhawo omwe adapatsidwa chilango chonyongedwa atapezeka olakwa popha anzawo malamulo adziko lino asadasinthe.

“Ndi ntchitoyi, anthu 131 adatuluka chifukwa adali atasewenza kale zaka zokwanira ndi chilango chomwe adapatsidwa. Ndipo tidapezanso kuti anthu atatu samayenera kumangidwa,” adatero iye.

Iye adaonjezeranso kuti bungwe lake lili  ndi chiganizo chopanga kafukufuku woti apeze kuti ndi anthu angati omwe akukhala m’ndende pokhudzana ndi milandu yopha anzawo koma asadaloweko kubwalo la milandu.

“Pakufunika kuti papezeke dongosolo loti milanduyi iziyenda mwachangu chifukwa palibe chilungamo kwa olakwa ndi olakwiridwa,” adatero Chisi.

Mkulu wa Legal Aid Department, Masauko Chamkakala adavomereza za mavutowa.

“Anthuwa akukhalitsadi milandu yawo isadaweruzidwe. Koma kumbali yathu tikuyesetsa kuti zinthu zisinthe,” adalongosola Chamkakala.

Chamkakala adati ambiri mwa anthu omwe ali pa limandi, ma failo awo akadali kupolisi.

Koma Chamkakala adati zinthu zisintha kutsogoloku chifukwa pakhala ntchito yomwe igwiridwe ndi thandizo la bungwe la European Union, yoika mafoni aulere m’ndende komanso polisi kuti anthu omangidwawa aziwadziwitsa okha a nthambiyi za milandu yawo.

Iye adati ntchitoyi idzayamba yoyeserera isanafalikire ndipo adatinso akupempha boma kuti awonjezere ogwira ntchito chifukwa alipo ochepa.

“Mwachitsanzo, ku chigawo chonse cha m’mawa kuli munthu mmodzi basi, yemwe amayendera maboma a Machinga, Zomba, Machinga ndi Balaka,” adatero Chamkakala.

Pachifukwachi, Chamkakala adati bungwe lake lilowa mgwirizano ndi anthu komanso mabungwe omwe ali ndi kuthekera koimira anthu pa milandu monga sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ndi bungwe la Law Society mwa ena.

Iye adatinso zinthu zisintha kwambiri dziko lino likadzavomereza malamulo oti aliyense oimira anthu pa milandu azigwira ntchito yaulere kwa ma ola angapo.

Ndipo adawonjezeranso kuti afikira ku Ntcheu kuti akaone m’mene zinthu ziliri chifukwa maboma ngati amenewo omwe ali kutali ndi mizinda, amaiwalika.

Mankhwala owetera nkhunda

Mukadzaona khola la nkhunda, pansi pake pamakhala zibalobalo. Ena amadabwa, kodi n’zachiyani? Izi akuti ndi mankhwala amene amapangitsa kuti nkhunda zisathawe. Pamene ena amati cholinga chake n’chakuti nkhunda ziswane. Kodi zenizeni n’ziti? BOBBY KABANGO adacheza ndi mfumu Kuziona ya kwa T/A Dambe m’boma la Neno yomwe ikufotokoza zambiri motere:

Wawa mfumu….

Fikani ndithu.

Ndadabwa ndi zomwe zili pansi pakhola la nkhundali. Kodi n’chiyani?

Ndi mlerankhunda kapena kuti mankhwala oimikira nkhunda kuti ana asamafe. Amagwira ntchito zambiri pa nkhunda.

Ndi zipatso zanji?

Dzina lake sindidziwa koma madera ena amangoti sopo wa m’tchire chifukwa ena amachapira akasowa sopo.

Chifukwa chiyani mwamangirira zimenezi?

Pali zifukwa zambiri, koma nkhani yaikulu ndikufuna kuti nkhundazi ziziswa ndipo kuti anawo asamafe.

Zichulukana bwanji oti nkhunda imaikira mazira awiri okha?

Sitifuna kuti nkhunda izitenga nthawi ikhale yaikira kale ena. Inde amakhala mazira awiri omwewo koma timafuna izichita changu komanso asamafe.

Kutanthauza kuti kupanda kumanga sizingaswe?

Zimaswa koma amangofa. Pamene ndamangirira zimenezi ndiye kuti sangafe ndipo azibadwa awiri awiri chifukwa choti ndamangiriranso zipatso ziwiri.

Chingachitike n’chiyani mutamangirira chipatso chimodzi?

Ndiye kuti atha kumabadwa mwana mmodzi. Ikaswa awiri winayo atha kufa ndipo mmodzi ndiye atsale.

Zimachitika chonchi chifukwa chiyani?

Apo inenso sindidziwa koma mwina ndimo Mulungu adazipangira kuti zizitero.

Mukukhulupirira bwanji oti simukudziwa?

Makolo anga akhala akugwiritsira ntchito zipatsozi pakhola la nkhunda. Ndimaona chomwe chimachitika tikati tachotsa ndiye zifukwa zokhulupirira zipatsozi zikukwanira.

Taonapo alimi ali ndi nkhunda zambiri koma sagwiritsira ntchito mankhwala, inu simukungodzinyenga apa?

Nawonso ali ndi podalira, atha kukunamizani kuti sagwiritsa ntchito mankhwala pamene akudziwa pamene akudalira. Afufuzeni.

Mukachotsa chimachitika n’chiyani?

Kungochotsa mudabwa zikaswa ana amangofa.

Mumamangirira bwanji zipatsozi?

Choyamba mukamanga khola, kayang’aneni zipatsozi ndipo mumangirire. Mutha kumangirira pamene mwangomanga khola kapena nkhundazo zikangolowa kumene m’kholamo.

Mumakazipeza kuti?

Zimakonda kumera mumtsinje, mutasakasaka muzipeza.

Mukamangirira sichimafota?

Chimafota koma musachotse chifukwa mphamvu yake imagwirabe ntchito. Ngati mwachotsa ndiye pezani zina mubwezeretsepo.

Kodi mwana atangothothola mungatani?

Ndimulanga ndipo ndiyesetsa kuti tsiku lisadutse ndikayang’ane china.

Kodi palibe mankhwala ena?

Mwina alipo koma amene makolo anga adandisiira ndi amenewa. Awa ndiye mankhwala a nkhunda amene amalera nkhunda pamudzi.

Kodi simungamangirire pakhola la nkhuku?

Ayi, awa ndi nkhunda zokha basi. Mwina ena angachite koma zomwe ndikudziwa ine ndi nkhundazi basi.

Kodi khola simupasula?

Zimatheka, ndipo zipatsozi timakazimangiriranso pakhola latsopanolo.

Pano muli ndi nkhunda zingati?

Sizingapose 20, ndazimaliza chifukwa kanthawi kena zimaposa 50.

Koma nkhunda zamankhwalazi zingakome?

Kwabasi, kodi ngati mankhwalawa amalowa m’thupi mwake? Mumangomangatu pa mtengo wa kholalo ndipo sizikugwirizananso. Mwangowona kuti ndatangwanika bwezi nditagwira kamodzi mulawe. n

Related Articles

Back to top button