Osinthasintha zipani ngosadalilika—Akadaulo

Andale osinthasintha zipani ndi osadalilika, ndipo amachita izi chifukwa cha dyera, atero akadaulo ena a zandale. Koma ena mwa andalewo atsutsa izi.

Akadaulowo, Mustapha Hussein, Happy Kayuni ndi Ernest Thindwa adanena izi polankhula ndi Tamvani paderapadera potsatira mchitidwe wa andale ena wosamuka m’zipani zawo ndi kulowa zina umene umachulukira makamaka nthawi ya chisankho ikayandikira. Mwachitsanzo, Lamulungu Brown Mpinganjira, Ken Lipenga ndi Henry Phoya, omwe adakhalapo nduna za boma m’maulamuliro a zipani zina mmbuyomu, adalengeza kuti alowa chipani cha DPP limodzi ndi mbusa Daniel Gunya.

Mutharika (Pakati) kulandira anayiwo Lamulungu

Izi zili choncho, miyezi ingapo yapitayo Sidik Mia, yemwe adakhalaponso nduna m’maboma a mmbuyomu, naye adalengeza kuti walowa MCP ndipo akufuna mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanicho.

Hussein adati andale osinthasintha zipani ndi wosadalirika chifukwa phindu lawo ndi losaoneka ndipo adangotsala maina okha. Iye adati anthu akudziwa kale kuti ndi wosakhazikika kotero kuwatsatira n’kudzipachika wekha.

“Ndimaina aphindu koma sangasinthe zinthu m’chipani chifukwa cha mbiri zawo zoyendayenda. Adayamba ndale kalekale ndipo anthu amawadziwa komanso amadziwa mbiri zawo,” adatero Hussein.

Polankhulapo za akuluakulu akhamukira ku DPP, Kayuni adati anayiwo akungofuna kudzawolokera pamsana pachipanicho kuti apeze mipando ya uphungu pachisankho cha chaka chamawa.

“Anthuwa akuchokera m’madera momwe DPP ili ndi mphamvu ndipo akudziwa kuti kuimira chipani china pampando wa uphungu, akhoza kugwa. Iwo akungoponya khoka kozama. Komabe sitikuwadabwa chifukwa ndimo alili,” watero Thindwa.

Malinga ndi Kayuni, pambali posintha zipani ngati malaya chifukwa cha dyera, vuto lina ndi la kusowa mfundo kwa zipani. Iye adati zipani za m’maiko ena zimakhala ndi mfundo zokhazikika choncho munthu amadziwiratu zomwe chipanicho chimafuna kukwaniritsa, osati kuphinduka monga zimachitira zipani za ku Malawi.

“Chipani chimakhala ndi mfundo zokhazikikazimene amatsata. Koma kuno kwathu chipani chimayamba mfundo iyi, kenako n’kutembenuka. Amene amatsatira mfundo imene yasiyidwa amatuluka chipanicho kukalowa china,” adatero Kayuni.

Iye adati kubwera kwa alendowo kumangobweretsa chilimbikitso nthawi yochepa chifukwa ngosadalilika. Ndipo kubwera kwawo kukhonza kubweretsa nthenya m’zipani akulowazo chifukwa a mkhalakale amaona ngati akufuna kulandidwa mipando.

Izi zaoneka kale kuchipani cha MCP kumene kubwera kwa Mia kwadzetsa mpungwepungwe, pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanicho Richard Msowoya ndi akuluakulu ena adzudzula mtsogoleriyo Lazarus Chakwera pogodokera khosi kwa Mia. Asanalowe chipani cha MCP, Mia adakhalapo m’zipani za UDF, DPP komanso PP. Polankhula ndi Tamvani, iye adatsutsa zoti dyera ndilo lamukokera ku MCP.

Iye adati chiyambireni ndale, sadakhaleko ndi mtima odzinthangatira yekha koma kutumikira anthu n’chifukwa chake adalowa m’chipani cha MCP chomwe mfundo zake n’zokomera Amalawi.

Mpinganjira adali mu UDF ndipo adachoka kukayambitsa chipani cha NDA. Chipani cha PP chitalowa m’boma, iye adalowera komweko koma zinthu zitavuta pachisankho cha 2014, iye adachitaya.

Iye adati mbiri yake isakhale chomuyezera pandale ndipo adati walowa DPP pofunanso kutumikira Amalawi.

“Boma ili limaika mtima pamiyoyo ya anthu, n’chifukwa chake ndikufuna kugwira nalo ntchito ndipo ndidzakhala nacho pamtendere ndi pamavuto pomwe,” adatero Mpinganjira.

Lipenga wakhalako m’mipando ya unduna kuyambira m’boma la chipani cha UDF chomwe adachisiya kukalowa DPP momwenso adali nduna koma adachitsika mtsogoleri wa chipanicho Bingu wa Mutharika atangomwalira mu 2012 n’kulowa PP yomwe idalowa m’bwalo.Samayankha foni yake.

Phoya adayamba ndi chipani cha UDF momwe adali nduna ndipo adasintha thabwa kulowa DPP kenako adalowa MCP, kumene sadakhalitseko. Iye adafunsa kuti timutumizire mafunso, amene sanayankhe.

Share This Post