Nkhani

Osiyidwa pachilumba cha Ruo alira koto!

Ndi 5 koloko mmawa, Belita Zakeyu wa m’mudzi mwa Manthenga kwa T/A Mlolo m’boma la Nsanje wafika kale m’manda a Chikoje kudzatola nkhuni. Iye akufuna akagulitse nkhunizo tsidya linalo, komwe ndi m’dziko la Mozambique komwenso akufuna akaguleko chimanga.

Manda a Chikoje ndi dzina chabe tsopano poti madzi osefukira adakokolola mabokosi a maliro n’kuwataya kutali.

Ruo watsopano yemwe wabweretsa mavuto kwa Mlolo
Ruo watsopano yemwe wabweretsa mavuto kwa Mlolo

Zakeyu, yemwe sakudziwa zaka zake, akusunga ana 9. Anayi ndi ake pamene enawo ndi amasiye. Alibe mwamuna, ndipo banja lonse likuyang’ana kwa iye kuti alidyetse. Alibe kothawira chifukwa boma ati lidasiya kuwathandiza.

Mayiyu ndi mmodzi mwa anthu 16 100 amene adatsakamira pachilumba cha Makhanga m’boma la Nsanje kwa T/A Mlolo kumayambiriro a chaka chino kaamba ka ngozi ya kusefulira kwa mtsinje wa Ruo.

Madzi osefukirawo pa 12 January 2015, adaphotchola njira n’kusiya anthu a midzi isanu ndi iwiri mwa gulupu Sambani ndi magulupu ena pakachilumba ndipo mpaka pano akukhalabe pomwepo kusowa kopita.

Pachilumbapo pali msika wa Admarc, chipatala cha Makhanga, Makhanga CDSS ndi sukulu ya pulaimale. Anthuwa kuti alandire thandizo zikuvuta chifukwa azunguliridwa ndi mtsinjewu.

Anthu a midzi 11 ya mwa gulupu Manyowa ndi Osiyana ndi omwe boma lidakwanitsa kuwasamutsa kukawasiya malo ena, komabe ophunzira amaolokabe mtsinjewo pangalawa kupita kuchilumbako kutsatira sukulu Makhanga CDSS.

Monga akunenera Zakeyu, boma lidawalonjeza anthu otsalawo kuti awasakira kokakhala koma mpaka lero kuli chuuu!

“Tikudikira lonjezo la boma. Panopa tikafuna msika wa Admarc, chipatala kapena zinthu zina timayenera tioloke mtsinje wa Ruo.

“Ngakhale tili ndi sukulu komanso chipatala, palibe zipangizo zokwanira. Tikubwerera kuchipatalako chifukwa chosowa mankhwala. Chimanga chidasiya kalekale kubwera pa Admarc ya Makhanga chifukwa cha mavuto a mayendedwe. Izi zikupangitsa kuti tizilowera m’dziko la Mozambique tikafuna thandizo, apo ayi, kuoloka Ruo kupita kumsika wa Osiyana,” adatero Zakeyu.

Gulupu Osiyana akuti ngati madzi osefulira angabwere lero, pali mantha kuti midziyi ingathe kukokoloka.

“Anthuwatu ali pakati pa madzi. Kungoti mvula yoopsa yagwa lero ndiye kuti anthuwa titayanso,” adatero Osiyana.

Iye akuti ngakhale midzi yake ili idaolotsedwa kupita tsidya linalo, ana alibe koti akaphunzire kupatula kupitbe kuchilumbako.

“Tilibe sekondale, moti ana athu akumakaphunzira ku Makhanga CDSS yomwe ili pachilumbapo. Sukuluyonso ili ndi mavuto ambiri chifukwa thandizo silifika,” adatero Osiyana.

Pamene kwangotsala miyezi iwiri kuti mvula iyambe, boma likuyenera kuolotsa anthuwa, apo ayi, likuyenera kuchita chotheka kuti mtsinje wa Ruo utenge njira yake yakale.

Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Climate Change and Meteorogical Services yalosera kuti chaka chino madzi angathenso kusefukira chifukwa mayendedwe a mpweya akusonyeza kuti mvula ingagwe moposera mlingo wake, maka kumalo okwera.

Koma mneneri wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), Jeremiah Mphande akuti ntchito yosamutsa anthuwa iyamba posachedwapa.

Iye wati padakalipano nthambi yawo yalemba ntchito kampani ina yomwe ikuyeza momwe angathanirane ndi vutoli.

“Chomwe tikufuna ndi kupanga mulambala kuti mtsinjewu ubwerere komwe umadutsa chifukwa pali mtunda wa makilomita 7 kuchokera komwe ankadutsa poyamba.

“Pakutha pa miyezi iwiri, atiuza zomwe apeza ndipo tikatero tiyamba kusaka ndalama zoti zithandizire ntchitoyi,” adatero Mphande.

Iye adati ntchitoyi yachedwa chifukwa ngoziyi idachitika ndondomeko ya zachuma ya boma itadutsa kale.

“Panopa ndiye kuti pakufunika ndalama zapadera kuti ntchitoyi igwiridwe,” adatero.

Kodi anthu adikire izi?

Mphande adati padakalipano anthuwo akuyenera asamuke poopetsa ngozi ina ngati mvula ingagwe msanga.

“Azanyengo akuti mvula mwina ingagwe yambiri chaka chino. Ndiye anthu akuyenera asamuke. Tidali komweko sabata yomweyi komwe taona kuti zinthu sizili bwino. Galimoto za boma zikulephera kuwafikira anthuwa ndi thandizo, ndiye akuyenera achoke,” adatero Mphande, amene adatsimikiza kuti pachilumbapo patsakamira anthu 16 100. n

Related Articles

Back to top button