Chichewa

Othawa nkhondo akutuwa ndi njala

 

Kwathina kukampu ya anthu othawa nkhondo m’dziko la Mozambique amene akukhala ku Mwanza ndi Neno komwe anthuwa akutuwa ndi njala.

Ena atha sabata ziwiri tsopano popanda chakudya ndipo amene ali bwino ndi anthu amene adabwera ndi ndalama kuchokera m’dziko lawo.

Gulupu Ngwenyama wa m’boma la Mwanza wati anthuwa akusowa mtengo wogwira kupatula anthu amene adayenda ndi ndalama kuchokera m’dziko lawo.

Ndiwo ndi vuto lalikulu kwa othawa nkhondo
Ndiwo ndi vuto lalikulu kwa othawa nkhondo

“Amene adabwera ndi ndalama ndiwo sakulira kwambiri chifukwa akumagula zakudya, koma amene adangobwera opanda kanthu ndi amene akuvutika chifukwa akungodikira thandizo la mabungwe,” adatero.

Gulu la anthu lidayamba kukhamukira m’dziko muno kuchokera ku Mozambique komwe akugwebana pachiweniweni pakati pa otsutsa boma ndi aboma.

Kumenyanako, komwe kudayamba chaka cha

tha, kudafika poipitsitsa mu January pamene nzika zina za dzikolo zidayamba kuthawira m’dziko la Malawi.

Kampu ya Luwani ku Neno yomwe ikusunga anthu pafupifupi 1 400 njomwenso yakhudzidwa kwambiri ndi njalayi. Kampu ina ndi ya Kapise m’boma la Mwanza komwe kuli anthu pafupifupi 900.

Malinga ndi Ngwenyama, pali chiyembekezo kuti Lolemba likudzali bungwe la World Food Programme (WPF) ligawa chakudya kwa anthuwa.

Naye Senior Chief Saimoni wa m’boma la Neno wati mavuto a njala ndi osakambika chifukwa nthawi zonse kukumakhala mavuto.

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.