ChichewaEditors Pick

Othawa nkhondo ku Mozambique asamukira ku Neno

Listen to this article

Bungwe lothandiza anthu othawa kwawo pazifukwa zosiyanasiyana la UNCHR layamba kusamutsa anthu othawa nkhondo ku Mozambique kupita ku Luwani m’boma la Neno.

Anthuwa, omwe akuthawa  nkhondo yapachiweneweni, amafikira kumisasa yongoyembekezera m’maboma a ku Nsanje, Chikwawa, Mwanza komanso Neno omwe achita malire ndi dziko la Mozambique.

Bungwe la UNHCR lidayamba kusamutsa othawa nkhondowa sabata ziwiri zapitazi pamene anthu 81 adawapititsa ku Luwani m’boma la Neno kuchokera kumalo omwe amangodikirirapo ku Nsanje.

Ena mwa othawa nkhondo ku Mozambique ulendo  wa ku Luwani
Ena mwa othawa nkhondo ku Mozambique ulendo
wa ku Luwani

Mkulu wofalitsa nkhani kubungweli m’Malawi muno, Kelvin Shimoh, adati cholinga chawo ndi kuti othawa nkhondowa akhale malo amodzi komwe angakalandire thandizo lokwanira.

Iye adati pali pafupifupi anthu okwana 11 000 omwe athawa nkhondo kuchokera ku          Mozambique ndipo chiwerengerochi chikuyemebezeka kukwera kwambiri.

Ku Kapise m’boma la Chikwawa kuli anthu pafupifupi 10 000 ndipo akuyembekezeranso kusamutsidwa kupita ku Luwani komwe kuli malo abwino okhala, olandirira thandizo la mankhwala komanso  sukulu zoti ana omwe ndi ambiri azikaphunzirako.

Mkulu wina wa bungwe lomweli la UNHCR woona za chitetezo cha othawa kwawo, Elsie Bertha Mills-Tettey, wapemphanso dziko la Malawi ndi anthu onse kuti asawasale anthuwa powaganizira kuti ndi achiwembu.

“Kafukufuku wathu wapeza kuti anthu othawa nkhondowa ali pachipsinjo choopsa chifukwa ataya katundu wawo, abale awo ena aphedwa akuona, komanso ena mwa iwo apulumuka atazunzidwa,” adatero Mills-Tettey.

Iye wayamikiranso bungwe la Unicef pachithandizo chomwe likupereka kwa anthuwa nkhondowa, makamaka ana, pankhani zowambikitsa kuti apitirizebe maphunziro awo.

Related Articles

Back to top button
Translate »