Nkhani

Otsutsa adzudzula MEC

Listen to this article

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) liyenera kutambasula bwino za pangano lake ndi bungwe limene likupereka zitupa za unzika la National Registration Bureau (NRB) pa zoti lidzagwiritsa ntchito zitupazo pa kalembera wa chisankho cha 2019, watero kadaulo pa ndale Mustafa Hussein.

Zipani za ndale, makamaka zotsutsa boma zakhala zikunena kuti chikonzero cha MEC n’kufuna kudzathandiza chipani cha DPP kubera mavoti.

Kalembera wa nzika ali mkati

“Mwati mudzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti Amalawi alowe m’kaundula wa zisankho. Apatu mpofunika kuti pamveke bwino chifukwa anthu akusokonekera,” adatero Hussein.

Zipani zotsutsa boma zakhala zikudandaula ndi ganizo la MEC lodzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti munthu adzalowe m’kaundula wa chisankho cha 2019.

Zipanizi zakhala zikubweretsa nkhaniyi m’Nyumba ya Malamulo momwe aphungu akukambirana za bajeti ya 2017/18 ndipo moto weniweni udabuka lolemba lapitali pa nkhumano yomwe bungwe la MEC lidapangitsa kuti lifotokozerane ndi zipani nkhani yokhudza chisankhochi.

Nthumwi za zipani zotsutsazi makamaka za Malawi Congress Party ndi Peoples Party, zidabooleza kuti zikukhulupilira kuti ganizoli ndi njira imodzi yofuna kudzabera chisankhochi ndipo zidanenetsa kuti sizilola kuti pulaniyi idutse.

Phungu wa kummawa kwa boma la Dowa Richard Chimwendo-Banda wa Malawi Congress Party (MCP) adati akuona kuti MEC ikukonza zodzathandiza chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) kubera chisankho.

Iye adati ndiwodabwa ndi kukakamira kwa bungwe la MEC kuti lidzagwiritse ntchito zitupa za unzika popanga kaundula wa anthu odzaponya voti chonsecho silikutengapo gawo lililonse pa zakapangidwe ka zitupazi.

“Bungwe la MEC lidali kuti pomwe nthambi yopanga kalembera wa zitupazi imayamba ntchito yake? Tili ndi chikhulupiliro kuti ali ndi mapulani odzabera chisankho ndipo ndikuuzeni kuti ulendo uno sitikulekelerani,” adatero Chimwendo-Banda.

Iye adati bungwe la MEC lisiye kulowerera ntchito za eni ndipo lipange pologalamu yake yakalembera wa m’kaundula wa chisankho mmalo modalira kuwolokera pamsana pa anzawo.

Wampampando wa bungwe la MEC Jane Ansah yemwe ndi woweruza milandu ku khothi lalikulu la apilo sadakondwe ndi zomwe adanena aphunguwo ndipo adawadzudzula kuti nawo akulephera udindo wawo posafotokozera anthu awo za kufunika kwa zitupazi.

Iye adatsutsa zoti bungweli lili ndi maganizo odzabera chisankho mwanjira iliyonse koma kuti likufuna kuti anthu ovomerezeka okha ndiwo adzaponye voti mu 2019.

Nduna ya za m’dziko ndi chitetezo Grace Chiumia adavomera kuti kalembera wa zitupa za unzika ikukumana ndi zokhoma monga kufaifa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito.

Related Articles

Back to top button