Pac iwopseza boma pa bilo yachisankho

Lisafike Lachitatu sabata ya mawa musanabweretse bilo yokhudza chisankho ndi maboma ang’ono. Latero bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) Lachinayi m’sabatayi.

Izi zimanenedwa pamene bungweli lidayenda ulendo ku Nyumba ya Malamulo komwe limakapereka mfundozi. Bungweli lati ngati sizitheka, boma liyembekezere zionetsero zokwiya ndi boma.

Atavala mikanjo, ena makolala, akuluakulu amipingowa motsogozedwa ndi mkulu wa PAC Mbusa Felix Chingota, adayenda ndawala kuchokera ku Area 18 mumzinda wa Lilongwe mpaka kukafika ku Nyumba ya Malamulo komwe adakapereka mfundo zawo kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi sipikala wa nyumbayo.

Izitu zikuchitika pamene PAC, akuluakulu a malamulo komanso amabungwe akhala akufunsira nzeru pa biloyi.

Nayo nduna ya zamalamulo Samuel Tembenu adalonjeza Amalawi pamene amalankhula M’nyumbayi kuti biloyi ikambidwa ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo. Koma chilankhulireni, boma lapinda manja pamene silikulankhulapo.

Mfundo zomwe PAC yalemba zati pamene biloyi ikubwera ku Nyumba ya Malamulo, boma lionetsetse kuti aphungu akambiranenso zokhudza lamulo loti opambana pachisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, azipeza mavoti oposa 50 pa 100 alionse.

“Ngati izi sizikambidwa mpaka pa 29 November, 2017, ife sitichitira mwina koma kuchita zionetsero dziko lonse,” idatero mbali ya kalatayo.

Polandira kalatayo mmalo mwa Mutharika, mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Lilongwe Charles Makanga adalonjeza PAC kuti nkhaniyi saikhalira ndipo ikamupeza Mutharika komanso onse ofunikira.

Share This Post