Nkhani

‘Padali pachiwaya cha tchipisi’

Listen to this article

“Adayezetsa tchipisi cha K150, ine ndidamuonjezera kuti agule cha K200.” Mmenemo ndi momwe zidayambira kuti Henry Mbinga akumane ndi Chimwemwe Edwin amene tsopano amangitsa woyera.

Chiyambicho chidaoneka chachibwana, koma lero ndi nkhani ina chifukwa tsiku lililonse Chimwemwe akusisita chifuwa cha Henry mwabata, mopanda mantha kapena manyazi.

Henry yemwe akugwira ntchito ku Magic Clean adati umu mudali mu July 2014 pamene iye adapita pasukulu ya Zingwangwa Progressive mumzinda wa Blantyre.

Kumeneko iye akuti amakaonera mpira wa ntchemberembaye ndipo ako kadali koyamba kumuona Chimwemwe akusewera mpira.

“Lidali Lachinayi, mawa wake ndidamuonanso pachiwaya cha tchipisi. Ndidakhotera pomwepo. Iye adayezetsa tchipisi cha K150, ine ndidauza mwini chiwayacho kuti amuyezere namwaliyo tchipisi cha K200,” adatero Henry.

Komatu mtsikanayu akuti adali asakumudziwa Henry, pamenenso Henry akuti kadali kachiwiri kumuona komabe adalimba mtima kucheza naye.

Ndiyetu Henry akuti adayamba kumuperekeza uko namwaliyu akudya tchipisicho, chidakoma ndipo sichidachedwe kutha chifukwa cha tinkhani ta Henry.

Asadamalize kudya tchipisicho mawu adagwa kuti akumufuna amange naye banja, koma Chimwemwe adazinda mauwo.

Padadutsa masiku atatu pamene adagwirizana zokumananso. Zidatheka ndipo namwaliyu adavomera kuti wagwa m’manja mwa Henry.

“Ndimafuna ndione ngati amanena zoona komanso ndimuone khalidwe lake,” adatero namwaliyu.

Ukwati udachitika pa 27 December chaka changothachi ndipo awiriwa akukhalira limodzi mwachimwemwe.

Henry amachokera m’mudzi mwa Joni, Senior Chief Somba m’boma la Blantyre pomwe Chimwemwe ndi wa m’mudzi mwa Chikoja kwa Senior Chief Somba komweko.

Related Articles

Back to top button
Translate »