Pemphererani dziko lino, ipempha ECM - The Nation Online

Pemphererani dziko lino, ipempha ECM

Mpingo wa katolika wapempha Amalawi kuti apempherere dziko la Malawi ndi utsogoleri wadziko lino panyengo ya Lenti.

Muuthenga wake wanyengoyi, mkulu wa mabishopu m’gulu la Episcopal Conference of Malawi (ECM) Joseph Zuza wati padakali pano, Amalawi akudutsa mumazunzo.

Zuza adati: “Atsogoleri athu ali ndi udindo waukulu woti moyo uzikhala ofewa wa ife tonse. Monga okhulupirira tiyenera kudziwa kuti Mulungu sangatitaye.”

Zuza adati zina mwa zomwe Amalawi ayenera kupempherera kuti zichepe ndi katangale ndi ziphuphu, kukondera ochokera kudera kwanu, kusankhana mitundu, zilakolako zakuthupi, ufiti, nkhanza kwa ana, uchidakwa ndi kupembedza Satana.

Zuza adapempha akatolika kuti aziyesetsa kukhala Akhristu achitsanzo, ndikutsatira malamulo a Mulungu.

“Aliyense ayenera kuonetsetsa kuti akukhala okhulupirika pamaso pa Mulungu,” adatero Zuza.

Ndipo muuthenga wake m’nyengoyi, Papa Benedict wachikhumi ndi chisanu n’chimodzi adati masiku 40 amene Akatolika akhale akupunguza ayenera kulingalira za mawu opezeka pa Ahebri 10 ndime 24.

“Tiyenera kukhudzidwa ndi mavuto a ena; kukhala okondana kumanso kugwira ntchito zabwino,” adatero Papayo.

Kwa masiku 40, Akatolika amakhala akupunguza ndipo zimayamba ndi tsiku la phulusa, lomwe lidali Lachitatu.

Panthawiyo, iwo amakhala akupemphera, kugawana, kulingalira molimba, kusala komanso kuchita zachifundo mpaka nthawi ya Pasaka mu Epulo.

Share This Post