Nkhani

Pepa Gaba, Malata

Listen to this article

Chalaka bakha nkhuku siyingatole. Nkhani ya Gabadinho Mhango ndi Lucky Malata ndiyo yatinenetsa mwambiwu. M’sabatayi nkhani idawawasa ndi ya anyamatawa omwenso amasewera Flames.

Akamunawa akadatola chikwama pang’onong’ono ku Joni koma ena alepheretsa. Aganyu sitinadandaule koma pena sitikumvetsa njomba yomwe yaseweredwa apa.

Ife sitidamvepo wosewera chigawo cha pakati atalowera kummwera kukayesa mwayi ndi Blantyre United koma pakutha pa mwezi kumva kuti wayesera mwayi ndi Big Bullets, Mighty Wanderers, Azam Tigers mpaka kufunanso kukadoda ku Evirom.

Lero Gaba wapita ku Joni koma museweretseni matimu ambirimbiri. Kodi zidatero chifukwa chiyani? Kodi timu zonsezi zimamufuna pakamodzi? Kodi zimachitika mwa chiponyeponye kuti kugwere mwayi ndi komweko?

Tikumva kuti matimu ena amafuna wosewera ngati Didier Drogba osati luso la Gaba. Koma izi ndi zoona? Ngati amafuna woteroyo bwanji osangopita ku Ivory Coast kukatenga Drogba? Kodi ndizotheka Gaba kusewera ngati Drogba? Gaba ndi Gaba ndipo Drogba ndi Drogba, sangafanane.

Tikuganiza kuti chilipo chomwe chimachitika kuti Gaba ndi Malata azingowavinitsa. Ku Amazulu pa magemu 5 Gaba adachinya zigoli 4 ndiye apapa akufunanso chiyani?

Komanso tikudabwa kuti bwanji Fam imangowonerera izi zikuchitika? Komadi Fam ndi manthu wa zamasewero m’dziko muno? Kodi zidachitikapo zoterezi?

Tithokoze kuti mwabwerako muli moyo. Pepani kuti mwavina moteromo koma dziwani kuti chitseko chitha kutseguka.

Dekhani timu zokoma zipezeka. Osadanda posakhalitsa tidzikuwonerani pa SuperSport mukumakana ndi Messi kapena Ronaldo.

Related Articles

Back to top button