A polisi alanda njinga zoposa 500 ku Mzuzu

Listen to this article
Chulukechuluke ngwa njuchi: Zina mwa njinga zomwe  zikusungidwa kupolisi ya Mzuzu
Chulukechuluke ngwa njuchi: Zina mwa njinga zomwe
zikusungidwa kupolisi ya Mzuzu

Mmene apolisi ankayamba kulanda njinga mumzinda wa Mzuzu, ena ankazitenga ngati tchetera, koma pano azindikira kuti lamulo liposa mphamvu.

Asacramento (ena amati akabanza) omwe adalandidwa njinga zawo ndi apolisi kumathero a chaka chatha mumzinda wa Mzuzu, akuyenera kudikirabe chifukwa silikudziwika tsiku lomwe adzatengere njingazi.

Mkulu wa apolisi mumzindawu, John Nyondo, adauza Msangulutso Lachiwiri kuti eni njingazi, zomwe zilipo pafupifupi 1 000, adzawabwezera pokhapokhapo “mumzinda mutakhala bata”.

“Chomwe tikufuna n’chakuti anjinga asamayende mkatikati mwa tauni. Tikuchita izi pofuna kuchepetsa ngozi zomwe zimadza ndi akabanza. Pakadalipano ambiri achepetsa kuyenda m’tauni, koma pali ena omwe akukakamirabe kuyendetsa njinga m’tauni,” adatero Nyondo.

“Tikukhwimitsabe chitetezo poonetsetsa kuti anthu sakulowa m’tauni ndi njinga. Pachifukwa ichi, njinga zomwe tidazigwira tizipereka kwa eni ake pokhapokhapo titaona kuti amvetsetsa zomwe tikufuna.”

Msangulutso umafuna kumva ngati eni njingazo adapatsidwa popeza kuti chaka chatha apolisi adanena kuti njinga zogwidwa zidzawomboledwa pakutha pa zikondwerero za Khrisimasi ndi Nyuwele.

Koma Nyondo adati tsiku lenileni lomwe anthuwa akuyenera kuyembekeza kupatsidwa njinga zawo silikudziwika koma adati nthawi ikafika azidzapita ndi wapampando wa dera lawo ngati mboni.

“Koma tidzawaphunzitsa kaye za kuipa koyendetsa njinga m’tauni pofuna kukhwimitsa chitetezo m’misewu ya mumzinda wa Mzuzu,” adawonjeza kunena Nyondo.

Mkulu wa apolisiyu adati ayamba akambirana kaye ndi akhonsolo ya mzinda wa Mzuzu kuti apeze mtengo womwe anthuwa azidzawombolera njinga zawo.

Mmodzi mwa oyendetsa njinga ku Mzuzu, yemwe amadziwika ndi dzina loti Dedza Boy, adati iwo si okondwa ndi zomwe anena apolisiwa.

Iye adati akufuna kuti eni njingazo apatsidwe mwamsanga chifukwa amadalira makobidi ochokera m’bizinesi yonyamula anthu panjinga pothandiza mabanja awo.

Asadabwere ku Mzuzu Nyondo amagwira ntchito ku Kasungu komwenso adakhazikitsa lamulo loletsa njinga m’tauni.

Atabwera ku Mzuzu adakhazikitsanso lamuloli lomwe anjinga ambiri sadagwirizane nalo mwakuti miyezi yapitayo padali mpungwepungwe pakati pawo ndi apolisi.

Zinthu zidafika pakuti anjinga adachita ziwonetsero poyendetsa njinga kuchoka kubwalo la masewero la Mzuzu kudutsa pamaofesi a polisi mpaka m’tauni.

Pofuna kubweretsa bata, apolisi adalowererapo koma ena mwa anjingawo akuti adakwenya ndi kumenya mkulu wa apolisiyu.

Ali ku Chitipa asadapite ku Kasungu, Nyondo akuti adakhazikitsanso lamulo loti anthu asamamwe mowa chakummawa koma kuyambira masana pofuna kuchepetsa uchidakwa, womwe amati ndi gwero la umbanda ndi umbava.

Wopezeka ali dzandidzandi mmawa amapatsidwa chilango chokasiyidwa kutali ndi kwawo kuti akhaule pobwerera wa Abrahamu.

Related Articles

Back to top button