Rasta akaseweza zaka 6

Mlandu woba njinga komanso kulasa ndi mpeni paphuzi pa bambo wa kabaza, watumiza Fedson Missi kundende komwe akaseweze zaka 6.

Chigamulochi chagwa Lachiwiri pa 28 November. Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’boma la Mangochi, Amina Daudi, watsimikiza kuti Missi wayamba ntchito yakalavula gaga.

Iye adati bwalo la milandu la Mangochi lidamva kuti pa October 2, chaka chino, Missi limodzi ndi anzake ena asanu-amene akusakidwabe, adalasa mpeni wakabaza wina.

Idali 6 koloko madzulo pamene wakabazayo, John Mandala, 21, wa m’mudzi mwa Mkumbi m’dera la mfumu Mponda m’bomalo adalasidwa pamene amabwerera kunyumba.

Wapolisi wakafukufuku wa ku Mangochi, Grace Mindozo, adauza khoti kuti Mandala adamusiya atasamba magazi ndipo njinga yake adamubera yomwe akuti idali ya K58 000.

“Wovulazidwayu adazindikira munthu mmodzi amene amadziwika kuti ndi wa chirasita,” adatero Daudi pokambapo zomwe Mindozo adanena m’khotimo.

“Ngakhale rasitayu adakana mlanduwu, bwalo lidamubweretsera mboni zitatu ndipo Mindozo adapempha woweruza mlandu kuti asamusekerere woganiziridwayo.”

Woweruza mlandu Ronald M’bwana adamupeza mkuluyu wolakwa ndipo adamugamula kuti akaseweze zaka 6 ku ndende.

Daudi wati apolisi akusakasakabe amuna ena asanu ndipo akawapeza, akayankha mlandu. n

Share This Post