Chichewa

Richard Mbulu: Chilombo cha Mafco FC

Listen to this article

 

Dzina la Richard Mbulu lasanduka nyimbo ya mizinda yonse chifukwa cha ntchito zake zomwetsa zigoli. Pano Mbulu akutsogola mu TNM Super League ndi zigoli 11, adamwetsanso zigoli 17 mu Presidential Cup. Kodi Mbulu ndani? BOBBY KABANGO akucheza naye.

Mbulu: Chilombo pankhani yokankha chikopa
Mbulu: Chilombo pankhani yokankha chikopa

Wawa Mbulu…

Mbuluyo ndiye ineyo, mani.

Kodi ndi Mimbulu? Kapena Mbulu basi?

Ndine Mbulu, koma dzina limeneli likuchokera ku dzina loti Mimbulu, tinyama tovuta kwabasi.

Ndiye iwe ndiwe wovuta?

Kumbali ya mpira basi, kuvuta kwanga ndi kumeneko, koma zinazi ndiye ndine munthu wabwinobwino.

Timudziwe kuti Mbulu ndani?

Mbulu ndi ineyo, mnyamata wochokera ku Mangochi, woyamba kubadwa m’banja la ana asanu.

Mbiri yako pachikopa ndiyotani?

Poyamba ndimasewera ku Navy FC kapena kuti Marine MDF, nditachoka kumeneko, ndidakatera ku [Big] Bullets komwe ndidakhalako kwa miyezi iwiri. Ku Navy ndidachokako nditangolemba mayeso a Form 4 mu 2013.

Zidayenda bwanji ku Bullets?

Sadandipatse mwayi woti ndisewerere m’timuyo, panthawiyo amati ndine mwana. Ndidachoka ulendo ku Mafco FC komwe adandilandira bwino.

Chipitireni ku Mafco wachinya zingati?

Ndachinya zigoli 108 za ligi ndi makapu omwe, apatu ndikutanthauza kuyambira 2013 mpaka lero.

Mphekesera zikuti mwayi wapezeka wokasewera ku Baroka FC ku Joni, ndi zoona?

Zili choncho koma sindingayankhe zambiri pankhaniyi. Ineyo ndine msirikali ndiye oyenera kuyankha pankhani imeneyi ndi mabwana anga.

Ndiwe wokwatira?

Ndili ndi mkazi koma ndilibe mwana.n

Related Articles

Back to top button