Samalani ndi sikelo za chinyengo—MBS

Nthawi yokolola yakwana, pomwe alimi amataya zokolola zawo kwa mavenda akuba amene amamanga sikelo pofuna kuliza alimi.

Koma bungwe loona zoyezayeza za malonda la Malawi Bureau of Standards (MBS) lati a malonda akuyenera aonetsetse kuti sikelo zawo zayezedwa ndipo zili pamlingo wabwino.

Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli Willy Muyila wati bungwe lake ndi lokhalo lomwe lingapime sikelo zisanayambe kugwira ntchito.

“Tili ndi zida zoyenera kupima zoyezera zomwe amalonda akugwiritsa ntchito. Zida zathu zimapimidwa ndi maiko akunja kotero ndife wothekera kuyeza zida za amalonda onse m’dziko muno,” adatero Muyila.

“Tikukambatu masikero oyeza zamadzi, mpweya, katundu wolemera bwanji komanso zipangizo zakuchipatala. Izi ndi zomwe timazipima kuti zisanayambe kugwira ntchito zikhale zili pamlingo wabwino,” adatero Muyila.

Iye adati amalonda amene amaphika kapena kupanga katundu wosiyanasiyana ayenera aonetsetse kuti zipangizo zawo zapimidwa ndi bungweli.

Izitu zimalankhulidwa pamene bungweli lidaitana amalonda kumsonkhano wa zopimapima womwe umachitikira mumzinda wa Blantyre Lachiwiri m’sabatayi.

Muyila adati posakhalitsa bungwe lake likhala likuyenda m’midzi kuti akapime masikero amene mavenda akugwiritsa ntchito.

“Ndipo tsiku lomwe tikupita sitinena kuopa kuwachenjeza mavendawo. Tiyenda paliponse kupima masikero,” adatero.

Mkulu woona za kapangidwe ka katundu pa kampani ya Candlex Ltd, Aaron Nkhoma yemwe adalinawo pa mkumanowo adati zokambiranazo zidali zothandiza.

“Ndi bwino kuti sikelo ikhale pamlingo wake chifukwa tidziwa zoyenera kuika popanga katundu wathu monga sopo. Komanso kuti tidziwe kukula kwa sopo amene tikufuna kupanga,” adatero Nkhoma.

Share This Post