Chichewa – The Nation Online http://mwnation.com Top Malawi Breaking News Headlines Mon, 20 Nov 2017 12:45:51 +0000 en-US hourly 1 https://wordpress.org/?v=4.9 Zipani zikufuna mayankho pa zitupa za unzika http://mwnation.com/zipani-zikufuna-mayankho-pa-zitupa-za-unzika/ http://mwnation.com/zipani-zikufuna-mayankho-pa-zitupa-za-unzika/#comments Fri, 17 Nov 2017 11:53:51 +0000 http://mwnation.com/?p=222442 Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi People’s Party (PP) zati kusowa kwa zitupa zina za olembetsa m’kaundula wa unzika zidzasokoneza chisankho cha patatu cha 2019. Nthambi ya National Registration Bureau (NRB) yati mwa zitupa 1.7 miliyoni zomwe zidajambulidwa m’gawo loyamba la zitupa za unzika, 1.5 miliyoni ndizo zatuluka. Izi zili choncho, bungwe loyendetsa chisankho…

The post Zipani zikufuna mayankho pa zitupa za unzika appeared first on The Nation Online.

]]>
Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi People’s Party (PP) zati kusowa kwa zitupa zina za olembetsa m’kaundula wa unzika zidzasokoneza chisankho cha patatu cha 2019.

Nthambi ya National Registration Bureau (NRB) yati mwa zitupa 1.7 miliyoni zomwe zidajambulidwa m’gawo loyamba la zitupa za unzika, 1.5 miliyoni ndizo zatuluka. Izi zili choncho, bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati lidzagwiritsabe ntchito zitupazo polembera ovota.

Mlembi wa PP Ibrahim Matola adati zitupazo sizimayenera kugwiritsidwa ntchito m’kalembera wa ovota chifukwa ntchitoyi siyinakhazikike.

“Tangoyamba kumene ntchitoyi. Tisayidalire ayi bola mtsogolomu zikadzagwira msewu koma padakalipano tiyeni tigwiritse ntchito njira yomwe timagwiritsa nkale lonse,” adatero Matola.

Mneneri wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati zitupa za unzika zokha sizikuyenera kugwiritsidwa ntchito pa mavoti chifukwa zina zikusowa.

“Kudzazigwiritsa ntchito limodzi ndi zitupa zovotera osati pazokha ayi poopa libolonje,” adatero iye.

Phungu wa ku mmawa kwa boma la Dowa, Richard Chimwendo-Banda wa MCP, adati kufaifa kwa zipangizozo kukhoza kuchititsa kuti anthu ambiri m’chigawo cha pakati asadzakhale ndi zitupa ndikulephera kudzaponya nawo voti.

Mkaka: Alongosole

Mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa watsindika kuti zitupazo zidzagwiritsidwa ntchito popanga kaundula wa odzavota pa chisankho cha 2019.

“Munthu amene adzakhale ndi chitupa, n’zachidziwikire kuti ndi nzika ndiye sitidzalimbana naye zambiri komabe tidzaona momwe tidzathandizire omwe alibe zitupa,” adatero Mwafulirwa.

Iye adati MEC ikuyembekezeka kudzayamba kukonza kaundula wa odzavota ndipo akukhulupilira kuti pofika nthawi yamavoti, nzika iliyonse idzakhala italandira chitupa chake.

Mneneri wa nthambi ya NRB Norman Fulatira wati anthu asakhale ndi nkhawa pankhaniyo chifukwa zivute zitani, Amalawi onse adzakhala ndi zitupazo.

The post Zipani zikufuna mayankho pa zitupa za unzika appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/zipani-zikufuna-mayankho-pa-zitupa-za-unzika/feed/ 1
Zitupa zaunzika zina zasowa http://mwnation.com/zitupa-zaunzika-zina-zasowa/ http://mwnation.com/zitupa-zaunzika-zina-zasowa/#respond Fri, 17 Nov 2017 11:48:37 +0000 http://mwnation.com/?p=222441 Zitupa 93 893 za uzika m’boma la Kasungu zasowa. Tamvani itha kuvumbulutsa. Izitu zadziwika pamene bungwe lolembera unzika la National Registration Bureau (NRB) layamba kupereka zitupazi kwa eni. Mneneri wa wa bungwe la NRB Norman Fulatira watsimikiza izi ndipo wati: “Ili si vuto lalikulu mtima ukhale mmalo.” Maboma amene adayambirira kulembetsa za unzika a Mchinji,…

The post Zitupa zaunzika zina zasowa appeared first on The Nation Online.

]]>
Zitupa 93 893 za uzika m’boma la Kasungu zasowa. Tamvani itha kuvumbulutsa.

Izitu zadziwika pamene bungwe lolembera unzika la National Registration Bureau (NRB) layamba kupereka zitupazi kwa eni.

Mneneri wa wa bungwe la NRB Norman Fulatira watsimikiza izi ndipo wati: “Ili si vuto lalikulu mtima ukhale mmalo.”

Maboma amene adayambirira kulembetsa za unzika a Mchinji, Dowa, Kasungu, Salima, Nkhotakota ndi Ntchisi ayamba kulandira ziphaso zawo zomwe zaonetsa kuti nkhope zina zikusowa.

Anthu 93 893 amene amayembekezera kulandira zitupazi adadzidzimuka kuona kuti maina awo palibe pamene anzawo nkhope zawo zatuluka ndipo alandira zitupa.

Anthu amene dzina lawo lasowa m’bomalo ati chiyembekezo chawathawa ngati angalandire zitupa zawo.

Lufeyo Mwanza wa m’bomalo adauza Tamvani kuti chikhulupiriro pa NRB achotsa kuti zitupa zawo zidzapezeka.

“Inde akutilimbitsa mtima kuti zitupa zathu zibwera komabe chilimbikitso chimenechi nchosakwanira. Tikuganiza kuti zasowa ndipo mwayi wokhala ndi zitupazi watiphonya,” adatero Mwanza.

Iye adati pakhota nyani mchira nkuti anzawo amene adajambulitsira limodzi zitupa zawo zatuluka koma iwo zavuta.

Komabe Fulatira akuti mwa maina 1.7 miliyoni omwe adalembedwa moyambirira, mayina 1.5 miliyoni okha ndiwo adatumizidwa kuti akatulutse zitupa ndipo maina enawo amaunikidwa ngatidi ali a Malawi.

“Anthu [asathamange magazi] kuti zitupa zawo zasowa, chifukwa tikukonza ndipo alandira zonse zikatheka bwinobwino,” adatero Fulatira.

Iye adatinso zitupa 200 000 za m’ndime yoyamba ya kalemberayu ndizo sizidakonzedwe ndipo anthu omwe zitupa zawo zasowawo akhoza kukhala m’gululi.

“Pologalamuyi ndi ya a Malawi choncho timayenera kuunika maina bwinobwino kuti tisapezeke zoti tikupeleka ziphaso kwa alendo. Zonse zikatheka, aliyense yemwe ndi nzika ya dziko lino ndipo adalembetsa, adzalandira chiphaso,” adatero Fulatira.

Senior Chief Kaomba ya m’boma la Kasungu idati iyo siyikuonapo vuto pa nkhaniyi chifukwa zitupa zomwe zikusowa nzochepa poyerekeza ndi zomwe zapezeka.

“Aka nkoyamba boma kupanga kalembera ngati uyu ndiye pa mayina 1.5 miliyoni, kusowa maina okhawo si chodandaulitsa kwenikweni ndipo tikuyenera kumvetsetsa,” adatero Kaomba.

Iye adapempha anthu kuti adekhe chifukwa NRB ikulongosola.

Boma lidakhazikitsa ntchito ya kalembera wa unzika kuti lizitha kuzindikira anthu ake makamaka powathandiza pa ntchito zofunika ngati za umoyo, maphunziro komanso kuwapeza mosavuta akasowa kapena kutsakamira mmaiko a eni.

Kalembera yemwe ali mkati pano adayamba pa 24 May chaka chino ndipo akuyembekezeka kutha mu December.

Malinga ndi Fulatira, ntchitoyi idzakhala ikupitilira mpaka kalekale.

“Iyi idali ndime yokhazikitsira ndipo aliyense amayenera kulembetsa mmalo omwe tikuchita kukhazikitsa koma kuyambira January chaka chamawa, omwe sadalembetse, aziloledwa kukalembetsa mmaofesi athu a m’maboma kapena kotumizira makalata [post office] yomwe angayandikane nayo,” adatero Fulatira.

Iye adatinso amene ayambe kulembetsa chaka chamawa koyamba azidzalembetsa ulere pamene kwa omwe adasowetsa chitupa ndipo akufuna china, azidzapemphedwa kupereka kangachepe.

Kwa amene amakhala kutali ndi post office sadzavutikanso chifukwa NRB idzidzayendera m’madera kuthandiza Amalawi malinga ndi Fulatira.

The post Zitupa zaunzika zina zasowa appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/zitupa-zaunzika-zina-zasowa/feed/ 0
Achita zionetsero za kuthimathima kwa magetsi http://mwnation.com/achita-zionetsero-za-kuthimathima-kwa-magetsi/ http://mwnation.com/achita-zionetsero-za-kuthimathima-kwa-magetsi/#respond Fri, 10 Nov 2017 13:05:29 +0000 http://mwnation.com/?p=221831 Anthu okhudzidwa a mu mzinda wa Lilongwe adachita ziwonetsero zosonyeza kukwiya kwawo ndi kuthimathima kwa magetsi m’dziko muno. Cholinga cha ziwonetserozo chidali kukakamiza kampani yogulitsa magetsi Escom kuti ifotokoze, komanso kuthana ndi vuto la magetsi. Vuto la magetsi lafika posauzana moti anthu ena akukhala tsiku lathunthu opanda magetsi. Anthuwo, omwe adatsogoleredwa ndi mkulu wodziwika bwino…

The post Achita zionetsero za kuthimathima kwa magetsi appeared first on The Nation Online.

]]>
Anthu okhudzidwa a mu mzinda wa Lilongwe adachita ziwonetsero zosonyeza kukwiya kwawo ndi kuthimathima kwa magetsi m’dziko muno.

Cholinga cha ziwonetserozo chidali kukakamiza kampani yogulitsa magetsi Escom kuti ifotokoze, komanso kuthana ndi vuto la magetsi.

Vuto la magetsi lafika posauzana moti anthu ena akukhala tsiku lathunthu opanda magetsi.

Anthuwo, omwe adatsogoleredwa ndi mkulu wodziwika bwino pa nkhani yomenyera ufulu wa anthu Billy Mayaya, adakapereka chikalata kwa mkulu wa Escom wa m’chigawo chapakati McVitty Chiphwanya.

Anthuwo adanyamula zikwangwani zodzudzula mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti walephera kuthana ndi vuto la magetsi.

Padakali pano mkulu wa kampani yopanga magetsi ya Egenco, William Liabunya, wati boma lagula ma generator kuchokera ku India omwe achepetse vuto la kuthimathima kwa magetsi m’dziko muno.

Ma generator’wo aikidwa ku Blantyre, Mulanje, Mangochi ndi ku Mzuzu ndipo akuyembekezereka kuyamba kufika m’dziko muno kuyambira sabata ya mawa.

The post Achita zionetsero za kuthimathima kwa magetsi appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/achita-zionetsero-za-kuthimathima-kwa-magetsi/feed/ 0
‘Boma likutengera a Malawi kumtoso’ http://mwnation.com/boma-likutengera-malawi-kumtoso/ http://mwnation.com/boma-likutengera-malawi-kumtoso/#comments Fri, 10 Nov 2017 12:49:24 +0000 http://mwnation.com/?p=221829 Pamene nkhani ya malamulo oyendetsera zisankho ili mkamwamkamwa, mkulu womenyera ufulu wa anthu, John Kapito, wati nkhani za magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zofunika kuti ziunikidwe mozama ndi Nyumba ya Malamulo yomwe yayamba dzuloyi. Kapito amathirirapo ndemanga pankhani yomwe yamanga nthenje yoti aphungu a nyumbayo sakambirana malamulo azisankho kaamba koti nduna sizidathe…

The post ‘Boma likutengera a Malawi kumtoso’ appeared first on The Nation Online.

]]>
Pamene nkhani ya malamulo oyendetsera zisankho ili mkamwamkamwa, mkulu womenyera ufulu wa anthu, John Kapito, wati nkhani za magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zofunika kuti ziunikidwe mozama ndi Nyumba ya Malamulo yomwe yayamba dzuloyi.

Kapito amathirirapo ndemanga pankhani yomwe yamanga nthenje yoti aphungu a nyumbayo sakambirana malamulo azisankho kaamba koti nduna sizidathe kuwaunika.

Kayendetsedwe ka chisankho sikasintha aphungu akapanda kukambirana malamulo atsopano

Izi zakwiyitsa mabungwe omenyera ufulu wa anthu a Centre for the Development of People (Cedep) ndi Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) omwe adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano wa nyumbayo mpaka boma litaika pamndandanda wa zokambirana malamulo atsopano oyendetsera zisankho.

Koma Kapito akuti ngakhale nkhaniyo ili yofunikira kwambiri, mavuto a magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zinthu zofunika kuthana nazo mwachangu.

“Anthu ambiri akupanga phokoso kwambiri ndi malamulo oyendetsera zitsankho. N’zoona malamulowo ndi ofunika, koma pali nkhani zina zofunika kwambiri zomwe anthu sakuzitchula. Tiyeni tiunike vuto la magetsi, madzi ndi chuma omwe akhudza miyoyo ya Amalawi ambiri,” adatero Kapito.

Iye adati kulimbikira kuti nyumbayo ikambirane malamulo azisankho n’kusiya mavutowa n’chimodzimodzi bambo kumasunga ndalama zogulira galimoto pamene ana ake akusowa chakudya, zovala, komanso athamangitsidwa fizi ku sukulu.

Padakali pano komiti yoona zokambirana za nyumbayo yatsimikiza kuti pali malamulo 6 omwe aphungu akambirane, koma Kapito wati sakuonapo lamulo lomwe lingathandize Amalawi mwachangu potengera ndi mavuto omwe akukumana nawo.

“Ndaunika malamulo onse omwe ali pamndandanda woti nyumbayo ikambirane, koma palibe lamulo lomwe lithane ndi vuto la magetsi, madzi, komanso kukweza chuma cha dziko lino.

Koma Billy Mayaya, yemwe ndi wodziwika kwambiri pankhani yomenyera ufulu wa anthu, wati boma likutengera Amalawi kumtoso posaika malamulo a zisankho pamndandanda wa zokambirana.

“N’zomvetsa chisoni kuti andale amafuna anthu panthawi yovota, koma kuti apange zofuna zawo amayang’ana kumbali,” adatero mkuluyu.

Mayaya adati malamulo a zisankho ndi ndime yoyamba yoonesetsa kuti Amalawi akulamulidwa ndi anthu omwe akuwafuna.

Imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zili mu lamulolo n’kuonetsetsa kuti boma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu.

Anthu ena omwe akhala akumenyera ufulu wa amayi akuti boma likulakwa kaamba kosatengera malamulowo ku Nyumba ya Malamulo.

Mmodzi mwa amayi omwe amamenyera ufulu wa amayi, Emmie Chanika, adati vuto la Amalawi n’kuyang’anira vuto mpaka likule ngati momwe mwana amayang’anira chilonda mpaka chikule n’kufika potukusira.

“Amalawi, zitsanzo tili nazo za maiko omwe adapatsa amayi mpata ndipo lero akuchita bwino. Nanga ife tidzapereka liti mpata kwa amayi?” adafunsa Chanika.

Iye adati anthu ambiri sachitapo kanthu pankhani zaphindu monga zotukula miyoyo ya amayi, koma nkhani zopanda pake.

Mabungwe a Cedep ndi CHRR adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano ya Nyumba ya Malamulo mpaka boma litabweretsa nyumbayo malamulo a zisankho.

Mkulu wa Cedep, Gift Trapence, ndi wa CHRR, Timothy Mtambo, adapempha boma kuti lichite zofuna za anthu potengera malamulowo ku nyumbayo.

Bungwe la Public Affairs Committee (PAC), lomwe posachedwapa limachititsa misonkhano yokambirana za malamulowo, lati silidayembekezere kuti boma lingawadyetse njomba yotere.

Mwa zina, malamulowo akuti mtsogoleri yemwe wachita bwino pa zisankho azilumbilitsidwa pakatha masiku 30 kuchokera patsiku loulutsa zitsakho, komanso kuti azipeza mavoto oposa theka la anthu omwe adaponya mavotiwo. Malamulowo akufunanso kuti m’boma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu.

Malamulowo akufuna kuti bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lizipatsidwa ndalama zokwanira kuti ntchito zake ziziyenda bwino.

The post ‘Boma likutengera a Malawi kumtoso’ appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/boma-likutengera-malawi-kumtoso/feed/ 1
Titsirika nkhalango zonse—Ng’anga http://mwnation.com/titsirika-nkhalango-zonse-nganga/ http://mwnation.com/titsirika-nkhalango-zonse-nganga/#respond Fri, 03 Nov 2017 16:02:00 +0000 http://mwnation.com/?p=221224 Gulu lina la asing’anga ku Dedza ladzithemba kuti likhoza kuteteza nkhalango za dziko lino ndi chambu koma akuluakulu a boma ati zonse zili m’manja mwa asing’angawo kuti awakhutitse kuti njirayo idzayenda. Mkulu woyang’anira za nkhalango m’dziko muno Clement Chilima adati nthambiyo ndi yokonzeka kupereka mpata kwa asing’angawo kugwira ntchito ndi asing’angawo poteteza nkhalangozo. Iye adati…

The post Titsirika nkhalango zonse—Ng’anga appeared first on The Nation Online.

]]>
Gulu lina la asing’anga ku Dedza ladzithemba kuti likhoza kuteteza nkhalango za dziko lino ndi chambu koma akuluakulu a boma ati zonse zili m’manja mwa asing’angawo kuti awakhutitse kuti njirayo idzayenda.

Mkulu woyang’anira za nkhalango m’dziko muno Clement Chilima adati nthambiyo ndi yokonzeka kupereka mpata kwa asing’angawo kugwira ntchito ndi asing’angawo poteteza nkhalangozo.

Kodi nsupa ndi zitsamba zingathandize kuteteza nkhalango?

Iye adati chomwe asing’angawa angachite n’kulembera kalata nthambiyo kuti ifunse upangiri pena ndi pena koma ganizo lawolo ndi lolandiridwa ngati silikuphwanya malamulo.

“M’magwiridwe a ntchito yathu, timalandira aliyense yemwe ali ndi njira yothandiza. Ngati asing’angawa akunena zoona ndipo njira yawoyo siyikuphwanya malamulo, abwere tiwapatsa mpata,” adatero Chilima.

Mkulu wa nthambi yoteteza nyama za kutchire Brighton Kumchedwa adati sanganeneretu mwa ndithendithe kuti chambu ndiye yankho koma adati gulu la asing’angalo ndilolandiridwa ngati likudziwadi njira yomwe ingathandize kuteteza nkhalango.

“Ntchito yathu ndi yogwira ndi anthu ndiye ngati papezeka ena omwe akuti ali ndi njira yomwe ingathandize, chowaletsera n’chiyani? Atatipeza n’kutifotokozera bwinobwino, ndipo titamvetsa, tikhoza kuona kuti tingagwire nawo bwanji ntchito,” adatero Kumchedwa.

Iye adati m’dziko muno muli nkhalango 84 zomwe zimafunika chitetezo chifukwa mitengo ndi nyama zopezeka mmenemo zikutha mosakhala bwino chifukwa cha mbala.

Gulu la asing’angali ndi lochokera m’boma la Dedza ndipo lanenetsa kuti chambu chikhoza kugwira ntchito yoteteza nkhalango kuposa ntchito ya alonda ndi asilikali.

Nthambi ya za nkhalango ndi nyama zopezeka mmenemo, itaima mutu ndi mchitidwe opha nyama komanso kudula mitengo mozemba, idalemba alonda omwe amathandizana ndi asilikali kuteteza nkhalango ndi nyama.

Woyang’anira ndi kulangiza asing’anga pantchito yawo m’boma la Dedza, Gulupu Ntambeni Chinyamula adati kupatula chidima, ophotchola m’nkhalango akhoza kukakamiraa mpaka kugwidwa momwemo.

“Chambu n’champhamvu zedi chikhoza kugwira munthu yemwe amafuna kukasokoneza m’nkhalango mpaka kugwidwa momwemo n’kulandira chilango choyenera,” adatero Chinyamula.

Pulezidenti wa asing’anga a mdziko muno Frank Manyowa adati n’zotheka kuteteza nkhalangozi potsirika nkhalangozo ndi chambu mmalo modalira alonda ndi asilikali.

“Ndi chambu, tikhoza kuteteza nkhalango zonse zomwe zikusowa chitetezo kuti owonongawo asamazione powakantha ndi chidima ndipo akhoza kulephera kupanga upandu omwe adakonzawo,” adatero Manyowa.

Iye adati asing’anga ali ndi njira zambiri zomwe akhonza kulangira anthu oononga nkhalango ndipo zilangozo zikhoza kuwapatsa mantha moti sangalakelake kubwerera kunkhalango.

Manyowa adati asing’anga zimawapweteka nkhalango zikamaonongeka chifukwa kasupe wa ntchito yawo wagona mmenemo.

“Timalimbikitsa kuteteza nkhalango chifukwa ndiko timapeza mankhwala athu. Boma lakhala likuyesetsa kuteteza nkhalango koma zikuwoneka kuti zikuvuta koma asing’anga akhoza kukwanitsa ndi chambu,” iye adatero.

The post Titsirika nkhalango zonse—Ng’anga appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/titsirika-nkhalango-zonse-nganga/feed/ 0
Makuponi n’chipsinjo—Mafumu http://mwnation.com/makuponi-nchipsinjo-mafumu/ http://mwnation.com/makuponi-nchipsinjo-mafumu/#respond Fri, 27 Oct 2017 13:12:53 +0000 http://mwnation.com/?p=220589 Kuchepa kwa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo omwe boma limagawa kwa anthu mogwirizana ndi mafumu, kukubweretsa chitonzo kwa mafumuwo ndi maudani osatha mmidzi. Izi zikudzanso makamaka pamene boma latsitsa chiwerengero cha opindula pa chilinganizochi kuchoka pa 1.5 miliyoni kufika pa 900 000. Mafumu ena ati chiwerengero cha makuponi omwe amaperekedwa chimangobweretsa mavuto mmalo…

The post Makuponi n’chipsinjo—Mafumu appeared first on The Nation Online.

]]>
Kuchepa kwa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo omwe boma limagawa kwa anthu mogwirizana ndi mafumu, kukubweretsa chitonzo kwa mafumuwo ndi maudani osatha mmidzi.

Izi zikudzanso makamaka pamene boma latsitsa chiwerengero cha opindula pa chilinganizochi kuchoka pa 1.5 miliyoni kufika pa 900 000.

Mwanamvekha kuyendera makuponi pomwe amafika kubwalo la ndege la Chileka

Mafumu ena ati chiwerengero cha makuponi omwe amaperekedwa chimangobweretsa mavuto mmalo mothetsa umphawi ngati mmene cholinga cha pologalamuyi chimanenera.

Mwachitsanzo, T/A Maseya wa ku Chikwawa limodzi mwa madera omwe akuti makuponi ayamba kale kugawidwa, wati mmudzi mwa Gulupu Tome momwe muli mabanja oposa 70, angolandira makuponi 6 okha chaka chino.

“Chimenechi chakhala chizolowezi, moti anthu amadana ndi mafumu awo pomaona ngati mafumuwo akubisa makuponi. A gulupu a Tome adabwera kudzandidandaulira kuti zinthu zavuta m’dera lawo,” adatero Maseya.

Iye adati zikafika apa, anthu nawo amayamba kunyanyala kutenga nawo gawo pankhani za chitukuko pomati omwe adalandira makuponi ndiwo akagwire ntchitozo zinthu nkumatsalira mafumu.

Senior Chief Chadza wa ku Lilongwe komwe akuti makuponi sadafike adati nkhani ndi ya maudani yomweyo ndipo adapereka chitsanzo choti dera la Gulupu Mnongwa lomwe lili ndi mabanja 170, chaka chatha adalandira makuponi 19 okha.

“Mabanja ambiri sadalandire makuponi ndipo zidali zovuta kwambiri moti pano tingoyembekezera kuti makuponiwo akafika kaya kukhala zotani chifukwa anthu adabzala kale m’mitima yawo kuti mafumu amabisa makuponi pomwe si choncho,” adatero Chadza.

Mfumuyo idati ikuona kuti boma likadapereka mphamvu zonse zopanga mapulani akagawidwe ku makhonsolo mwina bwenzi zinthu zikuyenda koma kuchuluka kwa makuponi opita kwa mafumu amakonzedwa kulikulu la boma.

Ngakhale zili choncho, mfumuyo idati anthu ake ali kalikiliki kukonzekera ulimi chifukwa ambiri mwa iwo adazolowera kuti asamadalire pulogalamu ya sabuside kuopa kugwiritsidwa fuwa la moto.

M’madera a kumpoto nako akuti makuponiwa sadayambe kufika ndipo T/A Khonsolo wa ku Mzimba wati izi zachititsa kuti anthu ayambe kukonzekera ulimi chifukwa sakudziwa pomwe makuponi adzafike.

“Tili ndi midzi ikuluikulu kwambiri koma nzomvetsa chisoni kuti chiwerengero cha makuponi chomwe timalandira moti zimangothera m’maudani osasimbika pakati pa anthu ndi mafumu komanso anthu okhaokha,” adatero Khonsolo.

Pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda adati pulogalamu ya sabuside imalozera tsogolola ntchito za malimidwe choncho n’koyenera kuitenga bwino.

Iye adati boma likuyenera kuunika bwino nkhani ya chiwerengero cha makuponi omwe limapereka pa mfumu iliyonse komanso kuunika nthawi yomwe makuponi amabwerera ndi nyengo yomwe zipangizo zimapezekera.

“Tiyamike kuti chaka chino zikuoneka ngati zayenda msanga koma tipemphe kuti chimenechi chikhale chizolowezi chifukwa alimi amamangika pa ntchito yawo chifukwa chosadziwa za tsogolo la sabuside,” adatero Kapichira Banda.

Chaka chino monga zidalili chaka chatha, anthu 900 000 ndiwo akuyembekezeka kupindula pa pulogalamu ya sabuside ndipo nduna ya zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Joseph Mwanamvekha adalengeza kuti makuponi onse adafika kale m’dziko muno.

Ndunayi idatsegulira ntchito yogawa makuponi Lachitatu sabata yatha m’boma la Mchinji komwe idachenjeza makampani ogulitsa zipangizo za sabuside, mafumu ndi akuluakulu ena kuti asayerekeze kulowetsapo zachinyengo.

Pakadalipano, bwalo la milandu mumzinda wa Blantyre laimitsa kaye ntchito zonse zokhudzana ndi makuponi, concho unduna wa malimidwe ndi bungwe la alimi aang’ono la Smallholder Farmers Revolving Fund of Malawi (SFFRFM) sapitiriza ntchito yogawa makuponi pomwe makampani amene akutumiza feteleza kumadera asapitirize ntchitoyo. Izi zidadza kampani ya Transglobe imene idachotsedwa pamndandanda wa makampani wopititsa feteleza kumidzi.

Wapampando wa komiti ya zamalimidwe m’Nyumba ya Malamulo Joseph Chidanti Malunga adati n’zokondweretsanso kuti chaka chino makuponi afika nthawi yabwino poyerekeza ndi chaka chatha pomwe makuponi amafika mpaka mu December madera ena asadalandire ndipo pomwe amalandira nkuti chimanga chitafula. n

The post Makuponi n’chipsinjo—Mafumu appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/makuponi-nchipsinjo-mafumu/feed/ 0
Tambala wameza chimanga http://mwnation.com/tambala-wameza-chimanga/ http://mwnation.com/tambala-wameza-chimanga/#comments Fri, 20 Oct 2017 09:08:46 +0000 http://mwnation.com/?p=220022 Kusadabuzika kwa chipani cha DPP pa chisankho chapadera kukutanthauza kuti Amalawi atopa ndi ulamuliro wa chipanicho, akadaulo a ndale ena atero. Malinga ndi zotsatira za bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), pachisankho chapadera chimene chidachitika Lachiwiri m’madera a phungu atatu ndi makhansalanso atatu, chipani cha MCP chidasesa mipando yonse ya phungu ndi iwiri…

The post Tambala wameza chimanga appeared first on The Nation Online.

]]>
Kusadabuzika kwa chipani cha DPP pa chisankho chapadera kukutanthauza kuti Amalawi atopa ndi ulamuliro wa chipanicho, akadaulo a ndale ena atero.

Malinga ndi zotsatira za bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), pachisankho chapadera chimene chidachitika Lachiwiri m’madera a phungu atatu ndi makhansalanso atatu, chipani cha MCP chidasesa mipando yonse ya phungu ndi iwiri ya khansala pomwe chipani cholamula cha DPP chidapeza mpanda wa khansala umodzi.

Otsatira MCP kusangalala mumzinda wa Blantyre

Akadaulo pankhani za ndale, Henry Chingaipe ndi Mustapha Hussein paokhapaokha adati kusakwaniritsa malonjezo amene DPP idapanga pachisankho cha 2014, ndizo zapangitsa kuti anthu ‘ade nacho kukhosi’.

Hussein adati izi zikutanthauza kuti ‘anthu sakukhutira ndi chipani cholamula cha DPP’ chimene wati sichikukwaniritsa malonjezo ake a pachisankho cha 2014.

“Amalawi sakukhutira ndi momwe [DPP] ikuyendetsera zinthu. Ngati chipanicho sichisintha, adzaona zakuda mu 2019,” adatero Hussein.

Zotsatira za chisankhochi zikudza pamene gulu lofufuza momwe ndale ndi zina zikuyendera mu Africa la Afro-barometer litatulutsa kafukufuku wawo amene amasonyeza kuti ngati chisankho chitachitika lero, Amalawi angavotere MCP pamene amati ataya chikhulupiriro mwa DPP.

Kafukufukuyu atatuluka, chipani cha DPP chidatsutsa ndipo chidati anthu sangayiwale ntchito zabwino zomwe akuchitira Amalawi.

Hussein wati zotsatira za chisankhochi zikuphera mphongo pa kafukufukuyo. “Vuto chipani cha DPP chimakonda kutsutsa. Koma akuyenera kusinkhasinkha pa zomwe zachitikazi,” adaonjeza.

Naye Chingaipe akuti chisankhochi ndi ‘uthenga kuti anthu atopa ndi ntchito za DPP’. Iye adati chisankhochi chili ngati ‘mpeni wa nsengwa wothwa konsekonse’.

“Mu 2014, DPP idalonjeza zambiri monga kuthana ndi mavuto a kuzimazima kwa magetsi, kusowa kwa madzi, ziphuphu komanso nkhani za umoyo. Mpaka lero palibe chachitika.

“Lero Amalawi apereka uthenga womveka ku boma kuti ngati sasamala, aika chikhulupiriro chawo pa chipani cha MCP,” adatero Chingaipe.

Koma mneneri wa boma Nicholas Dausi adati avomereza kuti agonja. “Ayi tivomere, tagonja ndewu koma nkhondo sitidagonje,” adatero Dausi.

Iye adati abwerera kwa Amalawi kuti amve pakhota nyani mchira kuti mpaka ziwavute choncho.

Wachiwiri kwa mlembi wa MCP Eisenhower Mkaka wati ichi ndi chizindikiro kuti chipanichi chidaberedwa mavoti mu chisankho cha 2014.

“Mwaona nokha zotsatira, tanthauzo kuti mu 2014 adatibera mavoti. Tili ndi chiyembekezo kuti mu 2019 chipani chathu chidzapambana,” adatero Mkaka.

Polengeza Mkulu wa bungwe loyendetsa chisankho la MEC, Jane Ansah Lachitatu adalengetsa zotsatira za chisankho chapadera chomwe chidachitika m’madera atatu.

Chipani cha MCP chidapeza mipando ya kumpoto kwa  Lilongwe Msozi, komwe adapambana ndi Sosten Gwengwe; kumwera cha kummawa kwa mzinda wa Lilongwe kumene adatola chikwama ndi Ulemu Msungama pomwe Lawrence Sitolo adatenga mpando wa ku Nsanje Lalanje.

Ndipo chipanicho chidazomolanso mipando ya khansala wa kuwodi ya  Mtsiriza ku Lilongwe komwe adapambana ndi Kingwell Zikaola komanso kuwodi ya Ndirande Makata kumene adapambana ndi Thom Litchowa.

Wopambana yekhayo wa DPP adali Nicholas Josiya yemwe adatenga wodi ya kumpoto kwa Mayani ku Dedza.

The post Tambala wameza chimanga appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/tambala-wameza-chimanga/feed/ 1
Za anamapopa sizikuzilala http://mwnation.com/za-anamapopa-sizikuzilala/ http://mwnation.com/za-anamapopa-sizikuzilala/#respond Thu, 19 Oct 2017 22:57:46 +0000 http://mwnation.com/?p=220021 Nkhani ya anamapopa ikulephera kutha. Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atangomaliza kuyendera maboma amene anthu angapo aphedwa powaganizira kuti ndi wopopa magazi. Sabata yomweyi, munthu wina wa zaka 22 adaphedwa ku Chileka mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti ndiwopopa magazi. Anthu okwiya adaswa polisi ya pa Chatha kuderalo atamupeza atagona m’munda wina, chonsecho mkuluyo anali…

The post Za anamapopa sizikuzilala appeared first on The Nation Online.

]]>
Nkhani ya anamapopa ikulephera kutha. Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atangomaliza kuyendera maboma amene anthu angapo aphedwa powaganizira kuti ndi wopopa magazi.

Sabata yomweyi, munthu wina wa zaka 22 adaphedwa ku Chileka mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti ndiwopopa magazi. Anthu okwiya adaswa polisi ya pa Chatha kuderalo atamupeza atagona m’munda wina, chonsecho mkuluyo anali wakhunyu ndipo amachokera kuchipatala.

Mbale wa mfumu Mtenje, Henry Kawisa (Kumanja) kuyendera khola

Ndipo mkulu winanso adaphedwa ku Balaka atapezeka akuyendayenda mbandakucha. Ndipo kwa Mtenje ku Chigumula mumzinda wa Blantyre, anthu adathyola khola la mfumu ya deralo ndi kubamo nkhumba 12, kuswa mawindo a nyumba yake mpaka kupulumutsidwa ndi apolisi.

Ndipo ena adachita zionetsero ngakhale pakati pausiku ku Bangwe, kwa Kachere, Machinjiri ndi Sigelege.

Zonsezitu zimachitika pomwe kuyambira Lachisanu mpaka Lolemba Mutharika adayendera maboma a Mulanje, Nsanje, Phalombe ndi Chiradzulu kumva anthu opulumuka ku ‘opopa magazi’, amene amaganiziridwa kuti ndi anamapopa komanso mafumu.

Chachikulu chimene chidatuluka pamisonkhanoyo n’choti mfumu yaikulu ya Alhomwe Paramount Ngolongoliwa idati akuchita izi ndi amatsenga ochokera ku Mozambique. Mfumuyo idapempha Mutharika kuti awasiyire zonse athane nawo m’matsenga.

“Mundipatse masiku 21, ife mafumu anu tithana nawo. Sangamachoke ku Mozambique kudzatiseweretsa kuno ngati tilibe ufiti. Tithana nawo basi,” adatero Ngolongoliwa.

Pamene adapempha Amalawi kusunga bata, makamaka pomwe akuganizira ena kukhala opopa magazi, Mutharika adati ngati nkhanizi ndi za matsenga azisiya m’manja mwa Ngolongoliwa ndi mafumu ena.

Koma mlembi wamkulu wa bungwe la oimira ena pamilandu la Malawi Law Society (MLS) Michael Goba wati ngati Ngolongoliwa adanena izi adaphwanya gawo 6 la malamulo okhudza nkhani za ufiti ndipo akhonza kumangidwa ndi kufunsidwa mafunso pakhoti.

“Gawoli limati onena kapena zochita zake zikusonyeka kuti ndi mthakati kapena wochita zaufiti adzalipa $50 (K36 500) ndi kukhala kundende zaka 10. Zomwe akuti zidanenedwa ndi mfumuyo ndi mlandu. Malamulo ndi wothekera kuthana ndi vutoli pokhapokha adindo a mphamvu zotero atawagwiritsa bwino ntchito,” adatero Chipeta.

Iye adati n’zokhumudwitsa ngati Ngolongoliwa adanenadi izi chifukwa udindo wake ndi wolemekezeka komanso uli pansi pa malamulo a dziko lino.

Pankhani yokhudza ufiti m’dziko muno, Chipeta adati polingalira mwakuya ndi povuta kunena kuti ulipo kapena ayo chifukwa ngati chipembedzo zimatengera katanthauziridwe ka mphamvu zapaderazi ndi zikhulupiriro za anthu. Iye adaonjezeranso kuti pachifukwachi sunganeneretu kuti munthu angachite kapena kusachita ufiti m’dziko lomwe silivomereza mchitidwewu.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la Association of Secular Humanism (ASH) George Thindwa, yemwe amalimbikitsa ganizo loti ufiti kulibe, Ngolongoliwa sadathandize kuthana ndi mpheketserayi ndipo amayenera kutsata malamulo a dziko lino chifukwa anamapopawo kulibe.

The post Za anamapopa sizikuzilala appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/za-anamapopa-sizikuzilala/feed/ 0
Amangidwa popha ‘anamapopa’ http://mwnation.com/amangidwa-popha-anamapopa/ http://mwnation.com/amangidwa-popha-anamapopa/#respond Fri, 13 Oct 2017 13:27:04 +0000 http://mwnation.com/?p=219509 Ndende ya Nsanje ikusunga anthu awiri omwe akuyenera kuyankha mlandu wopha Landani Chipira wa zaka 48 atamuganizira kuti ndi ‘namapopa’ m’mudzi mwa Gulupu Mchacha James kwa T/A Mlolo m’bomalo. Malingana ndi mneneri wapolisi ya Nsanje Agnes Zalakoma, anthuwa, omwe sadawatchule maina poopa kusokoneza kafukufuku wawo, adaonekera mukhoti Lachiwiri ndipo mlandu udzapitirira pa 20 October 2017.…

The post Amangidwa popha ‘anamapopa’ appeared first on The Nation Online.

]]>
Ndende ya Nsanje ikusunga anthu awiri omwe akuyenera kuyankha mlandu wopha Landani Chipira wa zaka 48 atamuganizira kuti ndi ‘namapopa’ m’mudzi mwa Gulupu Mchacha James kwa T/A Mlolo m’bomalo.

Malingana ndi mneneri wapolisi ya Nsanje Agnes Zalakoma, anthuwa, omwe sadawatchule maina poopa kusokoneza kafukufuku wawo, adaonekera mukhoti Lachiwiri ndipo mlandu udzapitirira pa 20 October 2017. Koma kafukufuku wa Tamvani wapeza kuti awiriwo ndi gulupu ndi mfumu ina kumeneko.

An artist’s impression of the arrest

Zalakoma adati anthu a m’mudziwo adakwiya ndi machitidwe a Chipira, yemwe anali mfumu Chizinga, ngati ‘namapopa’ ndipo adamugenda mpaka kupha.

“Masana apa 28 September, anthu olusa adathyola nyumba ya mkuluyo ndi kumugenda. Kufika lero, tamanga anthu awiri powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfayo. Sitiwatchula maina awo kuopa okhudzidwa ena angathawe,” iye adatero.

Pa nkhani yomweyi, mneneriyu adati apolisi amanganso amayi awiri a m’mudziwo, Chrissy Goba ndi Nota Tomas powaganizira kuti adafalitsa mauthenga abodza odzetsa mantha mwa anthu zomwe ndi zosemphana ndi gawo 60 la malamulo a zilango m’dziko muno.

Mbusa Danger Giant, wa mpingo wa Open Door m’dera La Gulupu Mchacha James, adati chibwana chalanda ndipo anthu akudandaula chifukwa chotaya moyo wa mfumu pa mpheketsera chabe.

“Munthu wina m’mudzi mwa malemuwa adati wapopedwa magazi ndiye ambiri adangoti mfumu ikudziwapo kanthu ndi kukayigenda. Chibwana ndi kuchita zinthu m’chigulu zadzetsa chisoni m’mudzimo,” adatero Giant.

Kumangidwa kwa awiriwo kudadza pomwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adadzudzula mchitidwe wopha anthu oganiziridwa kukhala a namapopa. Pamsonkhano wandale, Mutharika adakonza zokayendera maboma amene mchitidwewu wakula m’chigawo chakummwera monga Mulanje, Phalombe, Thyolo ndi Nsanje.

Mutharika adati: “Ndakhudzidwa ndi zopopana magazi. Amalawi mitima ikhale pansi. Tiyenera kupewa kufalitsa nkhanizi chifukwa zilibe umboni ndipo n’zopweteketsa anthu osalakwa.”

Anthu 7 aphedwa kale poganiziridwa kuti ndi anapopa zimene zachititsa dziko la United States of America komanso bungwe la United Nations kuchotsa ogwira ntchito ake m’madera okhudzidwa.”  

Zoonjezera: BOBBY KABANGO

The post Amangidwa popha ‘anamapopa’ appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/amangidwa-popha-anamapopa/feed/ 0
Chipalamba ku Malawi http://mwnation.com/chipalamba-ku-malawi/ http://mwnation.com/chipalamba-ku-malawi/#respond Fri, 13 Oct 2017 13:21:07 +0000 http://mwnation.com/?p=219506 Dziko la Malawi likusanduka chipalamba. Kafukufuku wathu wapeza kuti mafumu ndi apolisi ena ndiwo akuthandizira kusambula dzikoli pamene akuthandizira kudula mitengo mosasamala ndi kuotcha makala. Lidali dziko la nkhalango zowirira. Koma lero, madera ambiri ali mbee! Ukaona mitengo, ndiye kuti ndi pamanda. Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, dziko lino lili pamwamba pa maiko a mu…

The post Chipalamba ku Malawi appeared first on The Nation Online.

]]>
Dziko la Malawi likusanduka chipalamba. Kafukufuku wathu wapeza kuti mafumu ndi apolisi ena ndiwo akuthandizira kusambula dzikoli pamene akuthandizira kudula mitengo mosasamala ndi kuotcha makala.

Lidali dziko la nkhalango zowirira. Koma lero, madera ambiri ali mbee! Ukaona mitengo, ndiye kuti ndi pamanda.

Makala kudikira kuti awatengere kumalonda

Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, dziko lino lili pamwamba pa maiko a mu Sadc posakaza mitengo ndipo padziko lonse lapansi, lili pa nambala 4.

Mtolankhani wathu sabata yatha adalowa geni ya makala m’boma la Ntcheu. Uku ndi kumalire a Neno ndi Mwanza.

Iye adapeza anthu ochuluka akuchita bizinesi yootcha ndi kugula makala. Mitengo yambiri yatsala kuderali ndipo amene amapanga makala m’maboma a Mwanza ndi Neno asamukira kumeneko.

Mtunda woposa makilomita 90 umene udali ndi mitengo yambiri yachilengedwe lero ndi mpala. Mitengo yatha ndipo mitengoyi ikugwetsedwa m’malire a Malawi ndi Mozambique.

Mtolankhaniyu atafika, adauzidwa kuti akakumane ndi nyakwawa Kabwayibwayi ya m’boma la Ntcheu yomwe imupatse malo woti agwetse mitengo. Mfumuyo idatsimikiza kuti mitengo ilipo ndipo kuti mtolankhaniyu aotche makala, akuti amayenera kulipira ‘cha nkhalango’.

“Cha nkhalango ndi K2 000,” idatero mfumuyo.

Mtolankhani adauza mfumuyi kuti akufuna apange uvuni zisanu zotalika mamita 20. “Koditu kuli golide [mitengo], ndi zotheka,” idatero mfumuyo.

“Mita imodzi ndi K2 000, ngati mulibe ndalama ndiye mukaphula makalawo mudzapereka matumba atatu [olemera makilogalamu 50 lililonse],” adaonjeza.

Poona kuti zitenga masiku ambiri, mtolankhaniyu adaganiza zogula makala kwa ogulitsa ena kumeneko. Thumba lililonse limagulidwa K2 000.

Kuti thumba lifike ku Blantyre kokagulitsira, umayenera ulipe K2 500 kwa mwini galimoto. Kupatula izi, adatinso ndipereke K300 pa thumba lililonse yomwe imakhala ya apolisi.

“Masiku ambiri timakumana ndi apolisi amene amatilipiritsa. Ndiye timakonzeratu kunoko kuti tisavutike mayendedwe,” amene amathandiza mtolankhaniyo kupanga makalawa, Happy adatero.

Mtolankhaniyo atafunsa Happy kuti pa ‘roadblock’ ya polisi ya Zalewa akalipira chiyani, iye adayankha kuti malowo ngosavuta. Harry adaoda matumba 70.

“Mungomupatsa dalaivala K2 500 ndi K300, ndalamayi imathandiza zonsezi ndipo matumba anu akakupezani ku Blantyre,” adatero.

Anthu onse amene adali ndi makala adapereka ndalama zawo kwa woyang’anira kampuyo pamene iwo adanyamuka ulendo ku Blantyre.

Lachisanu onse amene adakwezetsa makala awo adachoka kumaloko. “Sitiyenda limodzi ndi galimotoyi, adzangotiuza kuti makala afika, tiyeni tibakadikirira ku Blantyre,” adatero Happy.

Sipadatenge nthawi, Loweruka m’ma 3 koloko mmawa, mtolankhaniyu adalandira foni kuti galimotoyo yomwe idanyamula matumba 250 yafika msika wa Khama ku Machinjiri. Onse amene adakweza makalawo adali pamalopo kugulitsa makalawo.

Patsikulo bizinesi simayenda bwino chifukwa thumba lomwe poyamba limagulidwa K9 000, limapita pa K5 000 mpakanso kumafika pa K3 500.

Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, pafupifupi mahekitala 3.4 miliyoni aonongeka pootcha makala. Mu June chaka chino, komiti yoona zachilengedwe ku Nyumba ya Malamulo idapempha undunawu kuti uletse kuotcha komanso kugulitsa makala m’dziko muno.

Wachiwiri kwa mkulu wa za nkhalango Ted Kamoto akuti dera la Neno, Ntcheu ndi Mwanza ndi lomwe likutulutsa makala ambiri pakadalipano. “Kumeneko mitengo ikugwetsedwa kwambiri pamene akupanga makala,” adatero.

Malinga ndi Kamoto vuto la kuotcha makala lakulanso kwambiri chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi komanso kuchepa kwa chiwerengero cha Amalawi amene amagwiritsa ntchito magetsi pophika.

“Amalawi 85 mwa 100 alionse amagwiritsa ntchito makala ndi nkhuni pophika. Izi zili choncho, 15 mwa 100 ndiwo amagwiritsa ntchito magetsi. Izi zafika pena chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi,” adatero iye.

Koma mneneri wa polisi James Kadadzera akuti anthu akuyenera akanene kupolisi ngati wapolisi wina akufuna ziphuphu kuti adutsitse makala.

“Ngatinso akuti akumapereka ndalama ku 997, atiuze nambala ya galimotoyo. Komanso atiuze wapolisi amene walandirayo,” adatero iye.

The post Chipalamba ku Malawi appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/chipalamba-ku-malawi/feed/ 0
Bambo amwalira pofuna kulemera http://mwnation.com/bambo-amwalira-pofuna-kulemera/ http://mwnation.com/bambo-amwalira-pofuna-kulemera/#respond Sun, 08 Oct 2017 07:45:42 +0000 http://mwnation.com/?p=218978 Bambo wina m’boma la Dedza wamwalira atamwa mankhwala oti alemere. “Ukakamwa mankhwalawa, ukafa sabata imodzi. Ukatuluka mphutsi, ndipo  akazi awo akatole mphutsizo zomwe zikasanduke ndalama. Kenaka ukadzukanso.” Awa ndi mawu amene sing’anga wina m’dziko la Mozambique akuganiziridwa kuti adauza bamboyo, Limbani Nsalawatha kuti akachite. Izitu zidachitika pa 13 September pamene bamboyu adakagwada kwa sing’anga pofuna…

The post Bambo amwalira pofuna kulemera appeared first on The Nation Online.

]]>
Bambo wina m’boma la Dedza wamwalira atamwa mankhwala oti alemere.

“Ukakamwa mankhwalawa, ukafa sabata imodzi. Ukatuluka mphutsi, ndipo  akazi awo akatole mphutsizo zomwe zikasanduke ndalama. Kenaka ukadzukanso.”

Awa ndi mawu amene sing’anga wina m’dziko la Mozambique akuganiziridwa kuti adauza bamboyo, Limbani Nsalawatha kuti akachite.

Izitu zidachitika pa 13 September pamene bamboyu adakagwada kwa sing’anga pofuna kuthana ndi umphwawi.

Malinga ndi mkazi wa bamboyo, Gloria, sing’angayo akuti adapatsa mwamuna wake mankhwala amene adamuchenjeza kuti afa kwa sabata imodzi yokha ndipo akadzuka.

Mayiyu, adauza apolisi ya Dedza kuti mwamuna wake adafadi atangobwera kwa sing’angayo adauzidwa kuti asauze munthu za imfa yake ndipo azidzangotolera mphutsi zake ndikuika m’thumba momwe zidzasanduke ndalama.

“Akuti adamuuza kuti sabata ikangotha, mwamuna wake adzuka ndipo adzakhala akusangalala ndi ndalama zomwe apanga kuthetseratu umphawi wawo,” adatero mneneri wa police ya Dedza Edward Kabango.

“Atafa sadalire kapena kuuza anthu. Mmalo mwake adayika thupi lake m’chipinda chapadera kwa masiku 6,” adaonjeza Kabango.

Gloria akuti adauza apolisiwa kuti nkhani yonse idadziwika pamene anzake oyandikana nyumba adayamba kumva fungo la chinthu choola komanso ntchentche zomwe zimauluka mozinga nyumbayo.

“Pochita mantha iye adathamangira kwa achibale a bamboyo amene adafika pakhomopo. Nkhaniyi idafikira kupolisi ya Njonja isadafike kupolisi kwathu,”  adatero Kabango.

Pa 20 September bamboyu akuti amayembekezera kudzuka malinga ndi zomwe adauzidwa kwa ng’anga koma mkazi wake adangoona chetechete popanda kutakataka mmalo mwake mphutsi ndizo zimasangalala.

Pa 21 malemuwa adakaikidwa mmanda. Zotsatira za chipatala, zidaonetsa kuti Nsalawatha, 22, adamwalira chifukwa chobanika.

Apolisi achenjeza anthu kuti asamangotengeka ndi zilizonse.

“Si zoona kuti mphutsi zingasanduke ndalama. Ili ndi bodza ndipo anthu asatengeke ndi zilizonse,” adalangiza Kabango.

Malemuwa amachokera m’mudzi mwa chimowa kwa T/A Kachere m’boma la Dedza.

The post Bambo amwalira pofuna kulemera appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/bambo-amwalira-pofuna-kulemera/feed/ 0
Gule alipo pa 17 October http://mwnation.com/gule-alipo-pa-17-october/ http://mwnation.com/gule-alipo-pa-17-october/#respond Fri, 29 Sep 2017 15:03:48 +0000 http://mwnation.com/?p=218436 Zipani za UDF ndi PP zaimika manja kuti sizidzapikisana nawo pamipando ya phungu pachisankho cha chibwereza chimene chikhalepo pa 17 October chifukwa maso awo ali pachisankho chapatatu mu 2019. Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho cha chibwereza m’malo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya…

The post Gule alipo pa 17 October appeared first on The Nation Online.

]]>
Zipani za UDF ndi PP zaimika manja kuti sizidzapikisana nawo pamipando ya phungu pachisankho cha chibwereza chimene chikhalepo pa 17 October chifukwa maso awo ali pachisankho chapatatu mu 2019.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho cha chibwereza m’malo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene enawo ndi makhansala.

Chisankho cha chibwereza chidalikonso mmbuyomu

Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu.

Mneneri wa UDF Ken Ndanga akuti ndondomeko ya chipani chawo ndi kupikisana malo amene akudziwa kuti achita bwino.

“Komabe sikuti tangokhala, tili ndi zochitika m’maderawo,” adatero Ndanga amene wati kusapikisana kwawo si tanthauzo lothandiza chipani cha DPP.

Ndipo mneneri wa chipani cha PP, Nowa Chimpeni adati maso awo lili pomanga chipani chomwe chidzalowenso m’boma mu 2019.

“Iyi ndiye ndondomeko yathu. Musandifunse kuti ndi ndondomeko zanji,” adatero Chimpeni amene adatsindika kuti PP siyikutha.

Koma katsiwri wa ndale Mustapha Hussein wati zipanizo zikadaganiza mozama chifukwa chisankho chilichonse ndi mwayi wopima mphamvu za chipani.

Ndanga: Chipani sichikutha

Zipanizo zati maso awo ali pachisankho cha patatu chomwe chichitike mu 2019. Mmalo mwake, chipani cholamula cha DPP ndi MCP ndiwo sakumwetsana madzi.

Koma Hussein wati PP ndi UDF akuyenera aganize kawiri chifukwa chisankho chilichonse n’chofunika popima mphamvu za chipani.

“Kukonzekera 2019 kumayenera kyamba pano, ndipo njira yabwino ndi kuchita nawo chisankho chachibwereza chomwe chimaonetsa mphamvu zachipani,” adatero Hussein.

Poyankhapo pa maganizo a Hussein, Ndanga akuti chisankhochi sichisonyezo zomwe zidzachitike pachisankho cha 2019.

Chimpeni: Tikukonzekera 2019

“Taonapo chipani chikupambana chisankho chachibwereza, koma kubwera chisankho chenicheni kugonja,” adatero.

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho chachibwereza m’malo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene ena ndi makhansala.

Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu.

MEC idakhazikitsa nthawi ya kampeni pa 13 September ndipo kampeniyi idzatsekedwa pa 15 October kuti pa 17 chisankho chidzachitike.

Bungweli lavomereza anthu 19 kuti apikisane nawo, amuna 15 ndi amayi anayi. Chisankho cha aphungu chichitika kumpoto chakummawa kwa boma la Lilongwe. Kumeneko apikisane ndi Ellen Shaban Kadango woyima payekha, Christopher Joseph Manja woyima payekha, Ulemu Msungama wa MCP ndi Ruben Ngwenya wa DPP.

Aphungu apikisananso kumpoto kwa Lilongwe Msozi komwe apikisane Bruno Daka wa DPP ndi Sosten Gwengwe wa MCP, yemwe adali wotsatira Joyce Banda wa PP pachisankho cha patatu mu 2014.

Ku Nsanje Lalanje apikisane ndi Gladys Ganda wa DPP, Laurence Mark Sitolo wa MCP, ndi Winnie Wakudyanaye woima payekha.

Chisankho cha makhansala chichitika ku Mtsiliza wodi komwe Brighton Golombe Edward wa UDF, Julio Benedicto Jumbe wa DPP ndi Kinwel Frank Zikaola wa MCP apikisane. Kummawa kwa Mayani wodi komwe Nicholas Fackson Josiya wa DPP, Everister Ndaziona Kusina wa UDF, Benson William Lameck wa MCP sakumwetsana madzi.

Nako ku Ndirande Makata wodi chilipo cha makhansala komwe Ishmael Chilambo wa UDF, Thom Lita wa DPP, Thom Harry Litchowa wa MCP, Mathews Joseph Shaba wa PP akupikisana.

Mneneri wa MEC, Sangwani Mwafulirwa wamema anthu ndi zipani kuti zisunge bata pa nthawiyi ndipo aliyense wodzetsa chisokoneza adzalangidwa.

The post Gule alipo pa 17 October appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/gule-alipo-pa-17-october/feed/ 0
Pulogalamu ya ECRP yatha http://mwnation.com/pulogalamu-ya-ecrp-yatha/ http://mwnation.com/pulogalamu-ya-ecrp-yatha/#respond Fri, 29 Sep 2017 14:56:14 +0000 http://mwnation.com/?p=218433 Pulogalamu yophunzitsa anthu kuteteza chilengedwe ya Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) yatha itakhalapo zaka 6 ikuphunzitsa anthu m’maboma 7. Mkulu woyendetsa pologalamuyi, Sophie Makoloma wati ndi wokondwa kuti m’zaka 6 zomwe akhala akuphunzitsa anthu, dziko la Malawi ndilosinthika. Maboma omwe apindula ndi Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga ndi Kasungu. “Ndine wa chimwemwe kuti anthu…

The post Pulogalamu ya ECRP yatha appeared first on The Nation Online.

]]>
Pulogalamu yophunzitsa anthu kuteteza chilengedwe ya Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) yatha itakhalapo zaka 6 ikuphunzitsa anthu m’maboma 7.

Mkulu woyendetsa pologalamuyi, Sophie Makoloma wati ndi wokondwa kuti m’zaka 6 zomwe akhala akuphunzitsa anthu, dziko la Malawi ndilosinthika. Maboma omwe apindula ndi Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga ndi Kasungu.

Kheli pano ali ndi ziweto,kuphatikizapo mbuzi

“Ndine wa chimwemwe kuti anthu akudziwa chochita kuti azembe ngozi zachilengedwe komanso akukwanitsa kusunga ndalama. Akutha kupanga mapulogalamu osiyanasiyana kuti chilengedwe chisamalike,” adatero Makoloma.

Kutseka pulogalamuyo kudachitika Lachitatu m’sabatayi pamene akuluakulu apulogalamuyo adakumana mumzinda wa Blantyre.

Pulogalamuyi imaphunzitsanso anthu momwe angachitire kuti asakhudzidwe ndi kusefukira kwa madzi komanso momwe angathanirane ndi kusintha kwa nyengo.

Zina zomwe anthuwa amaphunzitsidwa ndi monga kugwiritsa ntchito mbaula zamakono, ulimi wa mthirira, ulimi wa kasakaniza, kusunga ndi kubwereketsa ndalama, kubzala mitengo komanso kuweta ziweto.

Malinga ndi Makoloma, pulogalamuyi idacharira kuti ipindulitse anthu 177 000 koma pakutha pa ndime, anthu oposa 1.5 miliyoni ndiwo akumwemwetera kuti zawo zayera.

“Pamene tikutseka pologalamuyi, tikunena kuti tagwiritsa ntchito pafupifupi K15 biliyoni]. Komatu ndasangalala kuti zomwe timafuna zatheka,” adatero Makoloma.

Woyang’anira polojekitiyi koma akugwira ntchito ku Churches Action in Relief and Development (Card) m’boma la Thyolo, Chifundo Macheka akuti anthu a m’bomalo zawo zayera.

“Anthu akutha kubwereka ndi kubwereketsa ndalama. Ulimi ndiye simungachite kufunsa komanso anthu akuweta mbuzi kudzera m’polojekitiyi,” adatero Macheka.

Mabungwe a Department for International Development (DfID), Irish Aid ndi Norwegian Embassy ndiwo amathandiza ndi ndalama.

Mlimi mmodzi amene wathandizika ndi pologalamuyi, James Kheli wa m’mudzi mwa Sudala kwa Senior Chief Kanduku m’boma la Mwanza wati zake zidayenda ndipo palibe kubwerera mmbuyo.

Kheli ali ndi mbuzi 10, wayamba kukolola matumba 50 a chimanga kuchoka pa 15. Iye ndi banja lake abzala mitengo 300; akupanga ulimi wa mleranthaka komanso ali ndi munda wa chinangwa momwe akupha ndalama.

“Ndikulipirira mwana wa Folomu 4, pa telemu ndi K20 000. Ndamanga nyumba ya malata, ndagula wailesi komanso mpando wapamwamba,” adatero Kheli.

The post Pulogalamu ya ECRP yatha appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/pulogalamu-ya-ecrp-yatha/feed/ 0
Maofesala a kalembera ayera mmanja http://mwnation.com/maofesala-kalembera-ayera-mmanja/ http://mwnation.com/maofesala-kalembera-ayera-mmanja/#comments Fri, 22 Sep 2017 15:10:44 +0000 http://mwnation.com/?p=217927 Maofesala omwe akugwira ntchito yolembera nzika za dziko lino m’nkalembera wa anthu mwaunyinji ayamba kulandira malipiro awo atsopano. Chiyambireni ntchitoyi mwezi wa May chaka chino, maofesalawa akhala akudandaula ndi kuchepa kwa malipiro awo omwe adali pa K5 600 pa tsiku. M’kulira kwawo, maofesalawa amati ndalamayo siyikugwirizana ndi momwe katundu wakwerera m’dziko muno. Pachifukwachi, ogwira ntchitowa…

The post Maofesala a kalembera ayera mmanja appeared first on The Nation Online.

]]>
Maofesala omwe akugwira ntchito yolembera nzika za dziko lino m’nkalembera wa anthu mwaunyinji ayamba kulandira malipiro awo atsopano.

Chiyambireni ntchitoyi mwezi wa May chaka chino, maofesalawa akhala akudandaula ndi kuchepa kwa malipiro awo omwe adali pa K5 600 pa tsiku.

M’kulira kwawo, maofesalawa amati ndalamayo siyikugwirizana ndi momwe katundu wakwerera m’dziko muno.

Pachifukwachi, ogwira ntchitowa akhala akuopseza kuti anyanyala ntchito ngati malipiro awo sakwera kufika pa K10 000 patsiku, kutanthauza kuti ndalamayi njokwana K250 000 pa gawo lililonse la ntchitoyi.

Pachiyambi, maofesala ongogwirizirawa amalandira K120 000 pa gawo lililonse pomwe owayang’anira amalandira K150 000 ndipo ndalamayi idaonjezeredwa kufika  pa K175 000 ndi K205 000 mwa ndondomeko yomweyo.

Ndipo kuopsezaku kudapherezera sabata ino pomwe maofesalawa adanyanyaladi ntchito kwa masiku awiri ngakhale chifukwa chenicheni chidali chokakamiza boma kutulutsa anzawo 14 omwe adatsekeredwa m’chitokosi cha apolisi mumzinda wa Mzuzu la Mulungu lapitali.

Nduna ya za chitetezo Grace Chiumia ndiyo idalamula apolisi kutsekera anthuwa itawapeza atasonkhana pa Shoprite ya mzindawu kukambirana zokhudza ndalama yapamwambayi.

Anthuwa adatulutsidwa Lolemba lapitali pa belo ya polisi.

Mneneri wa bungwe loyendetsa ntchito ya kalemberayu la National Registration Bureau(NRB), Norman Fulatira, adauza Tamvani Lachitatu kuti mavutowa athana nawo chifukwa bungwe la United Nations Development Programme (UNDP) layamba kupereka ndalama zapamwambazi zomwe lakhala likulonjeza kuchokera mwezi wa May.

“Ndalama za ofesalawa aliyense zidakwera ndi K55 000 kuyambira gawo lachiwiri la kalemberayu lomwe lidayamba mwezi wa June,” adatero Fulatira.

Iye adaonjeza kuti kunyanyala ntchito kudatha chifukwa  padali mgwirizano pakati pa maofesalawa ndi UNDP kuti ilipire ndalama zapamwamba zonse m’masiku anayi; ndipo ntchitoyi idayamba lachiwiri.

Iye adati kunyanyala kwa ntchitoku kwakhudza ntchito ya kalemberayu koma kuti kunyanyalaku kwakhudza kwakukulu bwanji ntchitoyi, zioneka masiku 25 akadutsa.

Pakadali pano ntchitoyi ikulowa m’gawo lachisanu lomwe muli maboma a Mzimba, Rumphi, Karonga, Chitipa ndi Nkhata Bay.

Anthu pafupifupi 6 miliyoni ndiwo alembetsapo, chiyambireni cha kalembera wa unzika m’dziko muno. n

The post Maofesala a kalembera ayera mmanja appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/maofesala-kalembera-ayera-mmanja/feed/ 1
DPP ikhumudwitsa ku KK http://mwnation.com/dpp-ikhumudwitsa-ku-kk/ http://mwnation.com/dpp-ikhumudwitsa-ku-kk/#comments Fri, 22 Sep 2017 15:07:33 +0000 http://mwnation.com/?p=217926 Mafumu ena ku Nkhotakota ndi okwiya ndi chipani cha DPP chimene akuchidzudzula pogwiritsa ntchito galimoto ya chipatala pa ntchito zachipani. Lachisanu pa 15, chipanicho chidatenga galimoto ya chipatala cha Nkhotakota kukasiya otsatira chipani ku Lilongwe komwe amakatsanzikana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa ulendo wake wopita ku msonkhano wa United Nations General Assembly…

The post DPP ikhumudwitsa ku KK appeared first on The Nation Online.

]]>
Mafumu ena ku Nkhotakota ndi okwiya ndi chipani cha DPP chimene akuchidzudzula pogwiritsa ntchito galimoto ya chipatala pa ntchito zachipani.

Lachisanu pa 15, chipanicho chidatenga galimoto ya chipatala cha Nkhotakota kukasiya otsatira chipani ku Lilongwe komwe amakatsanzikana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa ulendo wake wopita ku msonkhano wa United Nations General Assembly (Unga) m’dziko la United States of America.

Galimoto limene lidanyamula a chipani kupita ku Lilongwelo

Izitu zimachitika pamene anthu pachipatalapo amasowekera thandizo la mayendedwe malinga ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Nkhotakoka, Peter Mazizi.

T/A wina amene adapempha kuti tisamutchule, adati mafumu ena akhala akupempha kuti mchitidwewu uthe komabe izi sizikuphula kanthu.

“Si koyamba kuti a DPP agwiritsire ntchito galimoto ya pachipatalapa. Timalankhula koma palibe yankho,” idatero mfumuyi. “Anthu amene akufuna thandizo la galimotoyo amadikira kaye kuti ithandize achipani.”

Koma mlembi wa chipanicho, Greselder Jeffery wati izi ndi ndale chabe ndipo si zoona kuti adagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala.

“Mmmh! abale, komatu ndalezi ndiye zafika penapake,” adatero potsutsa nkhaniyi. “Si zoona kuti tidagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala. Kodi anthu asamavale makaka a chipani chathu akakwera galimoto ya boma?

“Mwina anthuwo amapita ku maliro, chifukwa masiku ano anthu akumavala makaka achipani chathu ngakhale pa ukwati,” adatero Jeffery yemwenso ndi phungu kumpoto kwa boma la Nkhotakota.

Titafunsa mneneri wa chipatala cha Nkhotakota ngatidi zidali zoona kuti galimoto yawo idanyamula anthu a chipani, mneneriyu, Samson Mfuyeni adavomera koma adati galimotoyo si ya boma.

“Ogwira ntchito pachipatalachi ndiwo adagula galimotoyo.” Adaonjeza: “Ndi galimoto ya chipatala osati boma. Timaigwiritsira ntchito zinthu zambiri. Ndi zoona achipani cha DPP adabwereka poperekeza apulezidenti,” adatero.

Malinga ndi Mfuyeni, palibe cholakwika kubwereketsa galimotoyo chifukwa si ya boma.

Koma kafukufuku wathu wapeza kuti galimotoyo, MG 697AJ ndi ya unduna wa zaumoyo ndipo ikugwira ntchito pachipatala cha Nkhotakota.

Malinga ndi mkulu wina ku Plant and Vehicle Hire Organisation—nthambi yomwe ili pansi pa unduna wa zamayendedwe, galimotoyi yomwe ndi lole, ili m’manja mwa boma ku unduna wa zaumoyo.

Khalidwe la DPP lakwiyitsa phungu Mazizi wa deralo amene wati aka si koyamba kuti chipanichi chitenge galimotoyo.

Iye wati wakwiya kwambiri chifukwa patsiku lomwe galimotoyo imatumikira chipani, pachipatalapo padali maliro anayi amene amafunika anyamulidwe.

“Anamfedwa adandidandaulira, ndipo ndidasiya zomwe ndimachita kukawathandiza pamene galimoto yathu imatumikira chipani,” adatero.

Nkhaniyi ikudza pamene a mabungwe omwe si aboma akukakamiza chipanichi kuti chibweze K13 miliyoni yomwe chidalandira ku nthambi zaboma pa mwambo womwe chipanichi chidachititsa pa 29 July ngati njira imodzi yopezera ndalama.

Kadaulo pandale Mustafa Hussein wati zomwe chapanga chipani cha DPP pogwiritsira ntchito galimoto ya chipatala ponyamula masapota ake pokaperekeza pulezidenti Peter Mutharika ndi kulakwira Amalawi ndipo zotere zitheretu.

“Amalawi sangavomere kuti ndalama zawo zizigwiritsidwa ntchito chonchi. Ndi kulakwa posatengere chipani chomwe chikupanga izi,” adatero Hussein.

The post DPP ikhumudwitsa ku KK appeared first on The Nation Online.

]]>
http://mwnation.com/dpp-ikhumudwitsa-ku-kk/feed/ 1