Nkhani

‘Sitilembetsa mayeso’

Listen to this article

Aphunzitsi amene alembetse mayeso a Fomu 4 a chaka chino omwe ayambe pa 22 June, aopseza kuti sadzagwira ntchitoyo ngati Unduna wa Maphunziro salandira ndalama zomwe amapatsidwa akamapita kutchuthi.

Izi zikudza pamene ophunzira ndi makolo ena m’sukulu za pulaimale akudandaula kuti sitalaka ya aphunzitsi isokoneza kukonzekera mayeso a temu yachitatu omwe ayambe kumayambiriro kwa mwezi wa July. Aphunzitsi pafupifupi 63 000 akuchita sitalaka pofuna kukakamiza boma kuti liwapatse ndalama zomwe amalandira akamapita kutchuthi za chaka cha boma cha 2016-2017 chomwe chithe pa 30 June.

Apolisi adathamangitsa ana ku Chileka

Tamvani wapeza kuti pambali pa sitalaka imene yachititsanso kuti ana a sukulu za pulaimale zina apite pamsewu kudandaula kuti sakuphunzira, zokonzekera mayeso a Fomu 4 zili gwedegwede chifukwa kusamvana pakati pa boma ndi aphunzitsi kukupitirira.

Mlembi wa Teachers’ Union of Malawi (TUM) Charles Kumchenga adati palibe mphunzitsi alembetse mayeso m’sukulu komanso kuyang’anira mayeso a MSCE asadalandire ndalama ya tchuthi pachaka.

“Boma limayenera kusamalira umoyo wa oyang’anira mayeso omwe ndi aphunzitsi. Ophunzira akulangika chifukwa cha kholo lathu, boma. Boma lidalemba ntchito mphunzitsi kuti asamalire ana kumidzi ndipo lili ndi mayankho pa mavuto onsewa,” iye adatero.

Naye mkulu wa TUM, Willie Malimba, adati aphunzitsi ndi okhumudwa chifukwa boma ndi onse okhudzidwa akukanirana zofuna zawo.

Iye adati boma lingopereka ndalamazi osati kumangoyankhula zomwe zina zikulowa mabodza.

Bungweli lati lipereka chenjezo ku boma ndi nthambi ya mayeso ya Malawi National Examination Board (Maneb) kuti palibe mphunzitsi ayang’anire mayeso asadalandirenso ndalama ya ntchitoyi.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a za maphunziro m’dziko muno la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati mayeso a MSCE akhoza kupepuka malinga ndi zomwe zikuchitikazi.

“Kukhumudwa komwe kulipo kudzetsa kubera mayeso. Choopsa chichitika pa maphunziro m’dziko muno ngati sitisamala. Kulemba kwa mayeso a gawo lachitatu m’sukulu za pulaimale mu July n’kosathandiza chifukwa umafunsa zomwe waphunzitsa ndipo apa ana sakuphunzira. Tisaiwalenso kuti awa ndi mayeso woti ana apite kalasi ina,” iye adatero.

Iye adati ndi wokhumudwa ndi kulekerera kwa boma pa nkhani ya ndalama ya tchuthiyi ndi mavuto ena aphunzitsi omwe likuyenera kukonza.

“Boma silimvera zokhumba za aphunzitsi ndipo avutika kwa nthawi yaitali. Nthawi yakwana yokakamiza boma kupereka zomwe ndi zawo. Kuti boma lilimbikitse maphunziro abwino, makolo alimbe mtima kulifunsa chifukwa chomwe ana awo sakuphunzira ndiponso ana achite zomwezo,” adatero Kondowe.

M’sabatayi, aphunzitsi adalowa sabata yachiwiri akuchita sitalaka ndipo ana nawo adalowerera sitalakayo. Ana ophunzira m’sukulu zina ku Blantyre, Ntcheu ndi Balaka adapita pamsewu kuyambira Lolemba pofuna kukakamiza boma kumva kulira kwa aphunzitsi awo.

Pambali potseka misewu ina, ana enanso adamenya ndi kuvulaza apolisi atatu ku Lunzu mumzinda wa Blantyre, pomwe anthu 23 kuphatikizapo ophunzira 9 adamangidwa ku Ntcheu. Apolisi adathamangitsa ana ku Ndirande ndi utsi okhetsa misozi.

Kafukufuku wa Tamvani adasonyeza kuti ana m’maboma ambiri m’dziko muno sakuphunzira. Ana ndi aphunzitsi ena sakupita ndi kusukulu komwe.

Mwachitsanzo, pasukulu ya pulaimale ndi sekondale ya Katoto mumzinda wa Mzuzu, tidapeza ana ali khumakhuma kulingalira za tsogolo lawo. Ena adali kusewera mpira.

“Sindkuona bwino za kutsogoloku. Tikawafunsa aphunzitsi sitalaka itha liti, akutiyankha kuti sakudziwa, si zili m’manja mwawo. Ena a chifundo akumatiphunzitsa nthawi zina,” adatero wophunzira wa Fomu 2.

Poyankha nkhawa za phungu wa dera la kumpoto m’boma la Salima, Jessie Kabwila, m’Nyumba ya Malamulo Lolemba, nduna ya zachuma Goodall Gondwe idati dongosolo la ndalama za maboma 21 latheka ndipo ziperekedwa ku makhonsolo Lachiwiri.—Zoonjezera: MARTHA CHIRAMBO

Related Articles

Back to top button