Chichewa

Tadeyo Mliyenda: Ulendo wa ku Mzuzu

Listen to this article

Tsikulo Abiti Patuma adandipeza pa Wenela kuti ndimuperekeze ku Mzuzu kumene amakacheza ndi Paparazzi komanso anzake.
Tidakwera basi yausiku pa Wenela monga mudziwa kuchoka pa Wenela kukafika ku Mzuzu ndi mtunda wautali zedi. Mudali kuphulika nyimbo za mnyamata uja woukira, Jaso, inde mnyamata amene aliyense akudziwa bwino kuti amacheza kwambiri ndi Mpando Wamkulu koma lero akuti sakufuna kumvana Chichewa ndi mdzukulu wake wa Mpando Wamkulu, inde Atipatsa Likhweru.
Chilipo chikuchitika kuti lero lino Jaso azioneka kuti akuukira Atipatsa Likhweru ndi anzake ena onse ku Ukafuna Dilu Fatsa.
Ulendo uli mkati, Abiti Patuma adayamba kukamba zodziwa yekha. Palibe icho ndimatola pankhani zimene iye amakamba.
“Komatu zinaliko uku ku Kanjedza. Paja mudziwa Lazalo Chatsika uja wa Male Chauvinist Pigs masiku apitawa anamuuziratu Moya Pete kuti zomwe ananena zimakhala ngati zonena mlezi. Ndiye anyamata a Dizilo Petulo Palibe anamutengetsa ku Kanjedza, kufuna kumumenya,” adali kutero Abiti Patuma.
Palibe icho ndidatolapo.
“Koma ndiye kunali kukwenyana anyamata, kutsala pang’ono kutulutsirana nkhwangwa,” adapitiriza.
Abale anzanga, zovuta kumvetsa izi. Tidayenda ulendowo bwino lomwe ndipo pa Jenda tidafika cha mma 2 koloko usiku. Chilankhulo chidayamba kusintha.
Mpando wathu tidakhala anthu atatu. Kuwindo kudali Abiti Patuma, ine pakati ndipo mbali inayi kudali mkulu wina amene ankaoneka kuti wangofika kumene kuchokera ku Joni.
Mkuluyo adandifunsa: “Kasi mukuluta nkhu?”
Ndidamvapo nthawi ina kuti apa akutanthauza kuti mukupita kuti?
“Ine kuyowoya Chitumbuka nikuyowoya koma kweni kuti nipulike, nikutondeka chomene,” ndidayankha.
Ambiri mubasiyo adali mtulo. Kamphepo kadali katawakokera kutulo.
Mwadzidzidzi, tidamva wina akukuwa: “Choka! Choka! Iwe choka! Mayooooo!”
Aliyense mubasimo adadabwa kuti chikuchitika n’chiyani. Ngakhale amene amagona adadzidzimuka. Mkulu uja adadzidzimukanso kutulo kwakeko ndipo tonse tidaseka chikhakhali.
Atafunsidwa kuti amalota chiyani, iye adangoti: “Ndimalota anthu a mapazi ngati nkhwangwa komanso malilime ngati mipeni,” adayankha mkulu uja.
Gwira bango! Upita ndi madzi!

Related Articles

Back to top button
Translate »