Tambala wameza chimanga

Kusadabuzika kwa chipani cha DPP pa chisankho chapadera kukutanthauza kuti Amalawi atopa ndi ulamuliro wa chipanicho, akadaulo a ndale ena atero.

Malinga ndi zotsatira za bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), pachisankho chapadera chimene chidachitika Lachiwiri m’madera a phungu atatu ndi makhansalanso atatu, chipani cha MCP chidasesa mipando yonse ya phungu ndi iwiri ya khansala pomwe chipani cholamula cha DPP chidapeza mpanda wa khansala umodzi.

Otsatira MCP kusangalala mumzinda wa Blantyre

Akadaulo pankhani za ndale, Henry Chingaipe ndi Mustapha Hussein paokhapaokha adati kusakwaniritsa malonjezo amene DPP idapanga pachisankho cha 2014, ndizo zapangitsa kuti anthu ‘ade nacho kukhosi’.

Hussein adati izi zikutanthauza kuti ‘anthu sakukhutira ndi chipani cholamula cha DPP’ chimene wati sichikukwaniritsa malonjezo ake a pachisankho cha 2014.

“Amalawi sakukhutira ndi momwe [DPP] ikuyendetsera zinthu. Ngati chipanicho sichisintha, adzaona zakuda mu 2019,” adatero Hussein.

Zotsatira za chisankhochi zikudza pamene gulu lofufuza momwe ndale ndi zina zikuyendera mu Africa la Afro-barometer litatulutsa kafukufuku wawo amene amasonyeza kuti ngati chisankho chitachitika lero, Amalawi angavotere MCP pamene amati ataya chikhulupiriro mwa DPP.

Kafukufukuyu atatuluka, chipani cha DPP chidatsutsa ndipo chidati anthu sangayiwale ntchito zabwino zomwe akuchitira Amalawi.

Hussein wati zotsatira za chisankhochi zikuphera mphongo pa kafukufukuyo. “Vuto chipani cha DPP chimakonda kutsutsa. Koma akuyenera kusinkhasinkha pa zomwe zachitikazi,” adaonjeza.

Naye Chingaipe akuti chisankhochi ndi ‘uthenga kuti anthu atopa ndi ntchito za DPP’. Iye adati chisankhochi chili ngati ‘mpeni wa nsengwa wothwa konsekonse’.

“Mu 2014, DPP idalonjeza zambiri monga kuthana ndi mavuto a kuzimazima kwa magetsi, kusowa kwa madzi, ziphuphu komanso nkhani za umoyo. Mpaka lero palibe chachitika.

“Lero Amalawi apereka uthenga womveka ku boma kuti ngati sasamala, aika chikhulupiriro chawo pa chipani cha MCP,” adatero Chingaipe.

Koma mneneri wa boma Nicholas Dausi adati avomereza kuti agonja. “Ayi tivomere, tagonja ndewu koma nkhondo sitidagonje,” adatero Dausi.

Iye adati abwerera kwa Amalawi kuti amve pakhota nyani mchira kuti mpaka ziwavute choncho.

Wachiwiri kwa mlembi wa MCP Eisenhower Mkaka wati ichi ndi chizindikiro kuti chipanichi chidaberedwa mavoti mu chisankho cha 2014.

“Mwaona nokha zotsatira, tanthauzo kuti mu 2014 adatibera mavoti. Tili ndi chiyembekezo kuti mu 2019 chipani chathu chidzapambana,” adatero Mkaka.

Polengeza Mkulu wa bungwe loyendetsa chisankho la MEC, Jane Ansah Lachitatu adalengetsa zotsatira za chisankho chapadera chomwe chidachitika m’madera atatu.

Chipani cha MCP chidapeza mipando ya kumpoto kwa  Lilongwe Msozi, komwe adapambana ndi Sosten Gwengwe; kumwera cha kummawa kwa mzinda wa Lilongwe kumene adatola chikwama ndi Ulemu Msungama pomwe Lawrence Sitolo adatenga mpando wa ku Nsanje Lalanje.

Ndipo chipanicho chidazomolanso mipando ya khansala wa kuwodi ya  Mtsiriza ku Lilongwe komwe adapambana ndi Kingwell Zikaola komanso kuwodi ya Ndirande Makata kumene adapambana ndi Thom Litchowa.

Wopambana yekhayo wa DPP adali Nicholas Josiya yemwe adatenga wodi ya kumpoto kwa Mayani ku Dedza.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.